bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Judges 9
Judges 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 10 →
1
Tsono Abimeleki, mwana wa Yerubaala, adapita ku Sekemu kwa achibale a mai wake, nakaŵauza iwowo ndi fuko la banja la mai wake kuti,
2
“Funsani nzika zonse za ku Sekemu kuno kuti, ‘Chabwino koposa nchiti kwa inu, kuti ana onse 70 a Yerubaala azikulamulirani, kapena kuti mmodzi yekha azikulamulirani? Muzikumbukiratu kuti paja ine ndine mbale wanu weniweni.’ ”
3
Achibale a mai wakewo adamlankhulirako kwa anthu onse a ku Sekemu ndipo mitima yao ya anthuwo inali pa Abimeleki pakuti ankati, “Ameneyu ndi mbale wathu.”
4
Adampatsa ndalama zasiliva 70 za m'nyumba yachipembedzo ya Baala wa Chipangano. Ndalama zimenezo Abimeleki uja adaalembera anthu aganyu achabechabe ndi osasamala ntchito kuti azimtsata.
5
Adapita ku nyumba ya bambo wake ku Ufura, nakaŵaphera pa mwala umodzi abale ake 70, ana a Yerubaala. Koma Yotamu, mzime wa Yerubaala, sadaphedwe nao chifukwa adaabisala.
6
Tsono nzika zonse za ku Sekemu zidasonkhana ndi anthu a ku nyumba ya Betemilo, nkupita ku mtengo wa thundu pafupi ndi chipilala chachipembedzo cha ku Sekemu, kukalonga Abimeleki ufumu.
7
Yotamu atamva zimenezi, adapita kukaima pamwamba pa phiri la Gerizimu, ndipo adafuula kwambiri kuti, “Tamverani inu anthu a ku Sekemu, kuti nanunso Mulungu akumvereni.
8
Padangotere: mitengo idapita kukalonga mfumu yoti iziilamulira. Ndiye mitengoyo idauza mtengo wa olivi kuti, ‘Iwe ukhale mfumu yathu.’
9
Koma mtengo wa oliviwo udalandula, udati, ‘Ine sindingasiye mafuta angaŵa amene amalemekezera milungu ndi anthu omwe, kuti ndizikalamulira mitengo.’
10
Apo mitengoyo idauza mkuyu kuti, ‘Bwera ndiwe, ukhale mfumu yathu.’
11
Koma mkuyuwo udalandula, udati, ‘Ine sindingasiye zipatso zanga zokomazi nkuzuna kwakeku, kuti ndizikalamulira mitengo.’
12
Tsono mitengo ija idauza mtengo wamphesa kuti, ‘Bwera ndiwe, ukhale mfumu yathu.’
13
Koma mtengo wamphesawo udalandula, udati, ‘Ine sindingasiye kupereka vinyo amene amasangalatsa milungu ndi anthu omwe, kuti ndizikalamulira mitengo.’
14
Apo mitengo yonse ija idauza mkandankhuku kuti, ‘Bwera ndiwe ukhale mfumu yathu.’
15
Mkandankhukuwo udayankha kuti, ‘Ngati mukundidzoza ndi mtima wonse kuti ndikhale mfumu yanu, bwerani mudzabisale mumthunzi mwangamu. Mukapanda kutero, moto utuluke mwa ine ndi kupsereza mikungudza ya ku Lebanoni.’ ”
16
Yotamu popitiriza adati, “Kodi tsono mudachita ndi mtima wonse ndiponso mokhulupirika pakumdzoza Abimeleki kuti akhale mfumu? Kodi mwamchitira ulemu Yerubaala ndi banja lake, poyang'anira ntchito zimene adachita?
17
Suja bambo wanga adakumenyerani nkhondo naika moyo wake m'zoopsa, kuti akupulumutseni kwa Amidiyani?
18
Koma lero inu mwaukira banja la bambo wanga. Mwapha ana ake 70 pa mwala umodzi, ndipo mwalonga ufumu Abimeleki, mwana wa mzikazi wake, kuti azilamulira nzika za ku Sekemu, chifukwa chakuti ngwapachibale wanu.
19
Tsono ngati zimene lero mwachitira Yerubaala ndi banja lake mwazichita ndi mtima wonse ndiponso mokhulupirika, mukondwere naye Abimelekiyo ndipo nayenso akondwere nanu.
20
Koma ngati sizili choncho, moto utuluke mwa Abimeleki, upsereze nzika za ku Sekemu pamodzi ndi anthu a ku nyumba ya Betemilo. Ndipo moto utuluke mwa nzika za ku Sekemu ndiponso mwa anthu a ku nyumba ya Betemilo ndi kupsereza Abimeleki.”
21
Tsono Yotamu adathaŵa napita ku Beere ndipo adakakhala komweko, kuwopa Abimeleki mbale wake.
22
Abimeleki adalamulira Aisraele zaka zitatu.
23
Mulungu adaika chidani pakati pa Abimeleki ndi anthu a ku Sekemu, ndipo anthu a ku Sekemuwo adamuukira Abimeleki.
24
Izi zidachitika kuti zoipa zimene iye adaŵachita ana 70 a Yerubaala aja zimubwerere, ndipo kuti magazi ao akhale pa Abimeleki mbale wao amene adaŵaphayo, ndiponso pa anthu a ku Sekemu amene adamulimbitsa mtima kuti aphe abale ake.
25
Motero anthu a ku Sekemu adaika anthu pamwamba pa mapiri kuti abisalire Abimeleki, ndipo ankaŵalanda zinthu zao anthu onse odzera njira imeneyo. Abimeleki zimenezi adazimva.
26
Tsiku lina Gaala, mwana wa Ebedi, adasamukira ku Sekemu pamodzi ndi achibale ake. Ndipo anthu a ku Sekemu adamkhulupirira iyeyo.
27
Anthuwo adapita ku munda kukathyola mphesa, nafinya mphesazo. Kenaka adachita chikondwerero nakaloŵa m'nyumba ya milungu yao. M'menemo adadya ndi kumwa ndipo adayamba kutukwana Abimeleki.
28
Pambuyo pake Gaala, mwana wa Ebedi, adati, “Kodi ife ndife anthu otani m'Sekemu muno? Chifukwa chiyani tikutumikira Abimeleki? Ndipo kodi ndaninso amene uja? Ha, si mwana wa Gideoni! Zebuli amalamulidwa ndi iye uja, koma nanga ife kuti tizimtumikira nchifukwa chiyani? Tiyeni tikhale pambuyo pa kholo lathu Hamori, tate wa fuko lathu.
29
Anthu amumzindamu akadakhala pansi pa ulamuliro wanga, bwenzi nditamchotsa Abimelekiyo, ndipo ndikadamuuza kuti, ‘Onjezera ankhondo ako ndipo bwera, timenyane nkhondo.’ ”
30
Pamene Zebuli, munthu wolamulira mzindawo, adamva mau a Gaala mwana wa Ebedi, adapsa mtima.
31
Adatuma amithenga kwa Abimeleki ku Aruma kukanena kuti, “Gaala, mwana wa Ebedi, pamodzi ndi achibale ake, abwera ku Sekemu, akuutsa mitima ya anthu mu mzinda kuti akuukireni.
32
Nchifukwa chake, mupite usiku inuyo ndi anthu amene muli nawo, kukabisala m'minda.
33
Tsono m'maŵa dzuŵa likamatuluka, mudzuke msanga, mukauthire nkhondo mzindawo. Pamene Gaalayo ndi anthu ake azibwera kudzalimbana nanu, muŵakanthe monga m'mene mungathere.”
34
Choncho Abimeleki ndi anthu onse amene anali naye adadzuka usiku nakabisalira mzinda wa Sekemu m'magulu anai.
35
Gaala mwana wa Ebedi adatuluka nakaima pa khomo la chipata cha mzinda. Ndipo Abimeleki ndi anthu ake adavumbuluka kumene adabisala kuja.
36
Gaala ataŵaona anthuwo, adauza Zebuli kuti, “Ona, anthu akutsika kuchokera pamwamba pa mapiri.” Zebuli adayankha kuti, “Si anthu amenewo, ndi zithunzithunzi chabe zapamapiri zonga anthu.”
37
Gaala adalankhulanso nati, “Ona, anthu akutsika kuchokera pakati penipeni pa phiri, ndipo gulu limodzi likuchokera mbali ya ku mtengo wa thundu wa amaula.”
38
Tsono Zebuli adamufunsa kuti, “Pakamwa pako paja pali kuti tsopano, iweyo amene unkati, ‘Abimeleki ndaninso kuti ife tizimtumikira?’ Kodi si ameneŵa anthu aja unkaŵanyozaŵa? Tulukatu tsopano ukamenyane nawo nkhondo.”
39
Gaala adatuluka akutsogolera anthu a ku Sekemu nakamenyana naye nkhondo Abimeleki.
40
Koma Abimelekiyo adampirikitsa ndipo Gaalayo adathaŵa. Anthu ake ambiri adavulala njira yonse mpaka ku khomo la chipata.
41
Abimeleki adakhazikika ku Aruma, ndipo Zebuli adapirikitsa Gaala pamodzi ndi achibale ake, kotero kuti sadathenso kukhala ku Sekemu.
42
M'maŵa mwake anthu a ku Sekemu adapangana kuti apite ku minda, ndipo Abimeleki adazimva zimenezi.
43
Iye adatenga anthu ake, adaŵagaŵa m'magulu atatu, nakabisala m'minda. Ataona anthu akutuluka mu mzinda, pompo adapita kukalimbana nawo, naŵapha onsewo.
44
Abimeleki pamodzi ndi gulu lake adathamangira kutsogolo, nakakhalira pa khomo la chipata cha mzinda, ndipo nthaŵi yomweyo magulu aŵiri ena aja adaŵathamangira anthu onse amene anali m'minda aja, naŵapha.
45
Nkhondo idakhala tsiku lathunthu. Abimeleki adalanda mzindawo, naŵapha anthu amene anali m'menemo. Adauwonongeratu mzinda wonsewo, nauwaza mchere.
46
Anthu onse a ku nsanja ya Sekemu atamva zimenezo, adakaloŵa m'linga la nyumba yachipembedzo ya Baala wa Chipangano.
47
Abimeleki adazimva zakuti anthuwo asonkhana kumeneko.
48
Tsono adapita ku phiri la Zalimuna ndi anthu ake onse. Kumeneko adatenga nkhwangwa m'manja mwake nadula nthambi za mtengo, ndipo adazinyamula nazisenza pa phewa. Tsono adauza anthu akewo kuti, “Zimene mwaona ndikuchitazi, fulumirani inunso muchite chimodzimodzi, monga momwe ndachitira inemu.”
49
Choncho aliyense adadula mtolo wake natsatira Abimeleki, nakayedzeka mtolo wakewo pa linga lija ndipo adaliyatsa moto, kotero kuti anthu onse a ku nsanja ya Sekemu adafa. Analipo anthu ngati chikwi chimodzi, amuna ndi akazi.
50
Pambuyo pake, Abimeleki adapita ku Tebezi. Adauzinga mzindawo naulanda.
51
Mumzindawo munali nsanja yolimba, ndipo anthu onse amumzindamo, amuna onse ndi akazi omwe, adathaŵira m'nsanjamo, nadzitsekera m'kati. Ndipo adakwera ku tsindwi la nsanjayo.
52
Abimeleki adabwera ku nsanja ija, naithira nkhondo, ndipo adakafika pafupi ndi chitseko cha nsanjayo kuti achitenthe.
53
Koma mkazi wina wake adaponya mwala wa mphero pa mutu wa Abimeleki, nautswanya.
54
Apo Abimeleki uja adaitana msangamsanga mnyamata wake womunyamulira zida zake zankhondo namuuza kuti, “Solola lupanga lako, unditsirize, sindifuna kuti anthu azikati, ‘Mkazi ndiye amene adamupha.’ ” Apo mnyamata wakeyo adambayadi ndi lupanga, mpaka kutulukira kunja lupangalo, naafa.
55
Aisraele ataona kuti Abimeleki wafa, onse adapita kwao.
56
Umu ndimo m'mene Mulungu adalipsirira tchimo la Abimeleki limene adachitira bambo wake, pakupha abale ake 70 aja.
57
Mulungu adaŵalanganso anthu a ku Sekemu chifukwa cha kuipa kwao, ndipo matemberero aja a Yotamu, mwana wa Yerubaala, adaŵagweradi.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21