bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Judges 3
Judges 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 4 →
1
Tsono Chauta adasiya mitundu ina ya anthu, kuti ayese nayo Aisraele, ndiye kuti Aisraele onse amene sadamenye nao nkhondo ku Kanani.
2
Chauta ankangofuna kuti mibadwo yonse ya Aisraele idziŵe kumenya nkhondo, ndiponso kuti aphunzitse makamaka amene sadaidziŵe nkhondo nkale lonse.
3
Mitunduyo ndi iyi: mafumu asanu a Afilisti, Akanani onse, Asidoni onse ndi Ahivi amene ankakhala ku mapiri a Lebanoni, kuyambira ku phiri la Baala-Heremoni mpaka ku mpata wa Hamati.
4
Adaŵasiya kuti aziyesa nawo Aisraele, kuti aone ngati Aisraele adzamvera malamulo amene Chauta adaapatsa makolo ao kudzera mwa Mose.
5
Choncho Aisraele adakhala pakati pa Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.
6
Aisraelewo adayamba kukwatirana ndi anthu a mitundu imeneyo, ndiponso kukwatitsa ana ao kwa amuna a mitundu inayo. Kenaka adayamba kupembedza milungu yao.
7
Aisraele adachita zinthu zoipira Chauta. Adaiŵala Chauta, Mulungu wao, namatumikira mafano a Abaala ndi Asitaroti.
8
Nchifukwa chake Chauta adaŵapsera mtima Aisraelewo, naŵagulitsa kwa Kusani-Risataimu mfumu ya ku Mesopotamiya. Choncho Aisraele adatumikira Kusani-Risataimu zaka zisanu ndi zitatu.
9
Koma pamene Aisraele adalira kwa Chauta, Chautayo adaŵautsira munthu woŵapulumutsa; amene adaŵapulumutsayo ndi Otiniyele, mwana wa Kenazi, mng'ono wake wa Kalebe.
10
Mzimu wa Chauta udatsika pa iye, ndipo adasanduka mtsogoleri wa Aisraele. Adapita kukamenya nkhondo, ndipo Chauta adapereka Kusani-Risataimu, mfumu ya ku Mesopotamiya, m'manja mwake, namgonjetsa.
11
Motero dziko lidakhala pa mtendere zaka makumi anai. Pambuyo pake Otiniyele, mwana wa Kenazi, adamwalira.
12
Aisraele adachitanso zinthu zoipira Chauta. Ndiye Chauta adapatsa mphamvu Egiloni, mfumu ya ku Mowabu, kuti alimbane ndi Aisraele, chifukwa chakuti iwowo adaachita zinthu zoipira Chauta.
13
Egiloniyo adamemeza Aamoni ndiponso Aamaleke, napita kukagonjetsa Aisraele. Ndipo adalanda Yeriko, mzinda wamigwalangwa.
14
Tsono Aisraele adakhala akapolo a Egiloni, mfumu ya ku Mowabu, zaka 18.
15
Koma pamene Aisraele adalira kwa Chauta, Chautayo adaŵautsira munthu woŵapulumutsa. Iyeyu anali Ehudi, mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini, munthu wamanzere. Aisraele ankatumiza msonkho kwa Egiloni, mfumu ya ku Mowabu, kudzera kwa Ehudi.
16
Tsono Ehudi adasula lupanga lake lakuthwa kuŵiri, kutalika kwake masentimita 50. Ndipo adamangirira lupangalo pa ntchafu yake yakumanja m'kati mwa zovala zake.
17
Adapita kukapereka msonkho kwa Egiloni, mfumu ya ku Mowabu, amene anali wonenepa kwambiri.
18
Ehudi atamaliza kupereka msonkhowo, adauza anthu onyamula msonkhowo kuti azipita.
19
Koma iyeyo adabwerera pa malo a miyala yozokotedwa ku Giligala, ndipo atafika kwa mfumu adati, “Zikomo amfumu, ndimati ndikuuzeni mau achinsinsi.” Pamenepo mfumuyo idalamula atumiki ake kuti akhale chete, niŵatulutsa onsewo.
20
Tsono Ehudi adasendera pafupi ndi mfumuyo, iyoyo itakhala yokhayokha m'chipinda cham'mwamba chozizira bwino. Ndipo adati, “Ndili ndi mau ochokera kwa Mulungu oti ndikuuzeni.” Mfumuyo idadzuka pa mpando wake.
21
Apo Ehudi ndi dzanja lake lamanzere, adasolola lupanga pa ntchafu yake yakumanja ndi kubaya nalo mfumuyo pa mimba.
22
Lupangalo lidaloŵa ndi chigumbu chomwe, ndipo mafuta adaphimba lupangalo pakuti sadalitulutsenso m'mimbamo, adalisiya litatulukira kumbuyo.
23
Ehudi adatulukira m'khonde, atatseka ndi kukhoma zitseko za chipinda cham'mwambacho.
24
Ehudi atachoka, atumiki a mfumu adabwera. Ataona kuti zitseko za chipinda cham'mwamba nzokhoma, adaganiza kuti, “Kapena mfumu ikudzithandiza m'katimo.”
25
Iwo adadikira nthaŵi yaitali, kotero kuti sadaone konse chochita. Koma ataona kuti mfumuyo sidatsekulebe zitseko zija, adatenga kii natsekula zitsekozo, ndipo adangoona mfumu yao ili thasa pansi, itafa.
26
Ehudi adathaŵa pamene iwo ankachedwa nkudikira. Adapitirira malo a miyala yozokota ija, nathaŵira ku Seira.
27
Atangofika adaimba lipenga m'dziko lamapiri la ku Efuremu. Aisraele onse adatsika pamodzi naye kuchokera ku dziko lamapirilo, iyeyo akuŵatsogolera.
28
Adauza anthuwo kuti, “Tiyeni kuno, Chauta wapereka Amowabu, adani anu, m'manja mwanu.” Choncho anthuwo adamtsata nakalanda madooko a Yordani natsekereza Amowabuwo, osalola kuti munthu ndi mmodzi yemwe aoloke.
29
Nthaŵi imeneyo adapha Amowabu pafupi 10,000. Anthu onse ophedwawo anali amphamvu ndiponso odziŵa kumenya nkhondo, koma sadapulumukepo ndi mmodzi yemwe.
30
Choncho Amowabu adagonjetsedwa ndi Aisraele pa tsiku limenelo. Ndipo dzikolo lidakhala pa mtendere zaka makumi asanu ndi atatu.
31
Atamwalira Ehudi, padabwera Samigara, mwana wa Anati, amene adapha Afilisti 600 ndi ndodo yomenyera ng'ombe. Motero iyeyunso adapulumutsa Aisraele.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21