bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Revelation 10
Revelation 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 11 →
1
Pambuyo pake ndidaona mngelo wina wamphamvu akutsika kuchokera Kumwamba. Adaavala mtambo, ndipo pozungulira mutu wake panali utawaleza. Nkhope yake inali ngati dzuŵa, miyendo yake ngati mizati yamoto.
2
M'manja mwake anali ndi kampukutu kofutukula. Ndi mwendo wa ku dzanja lamanja adaaponda pa nyanja, ndi wakumanzere adaaponda pa mtunda.
3
Tsono adaafuula mokweza ngati kubangula kwa mkango. Mngeloyo atangofuula choncho, mabingu asanu ndi aŵiri aja adagunda.
4
Mabinguwo atangogunda, ndidaati ndilembe. Koma ndidamva mau ochokera Kumwamba akuti, “Zisunge mu mtima zimene mabingu asanu ndi aŵiri aja anena. Usazilembe.”
5
Pamenepo mngelo amene ndidaaona ataponda pa nyanja ndi pa mtunda uja, adakweza dzanja lake lamanja kumwamba.
6
Atatero adalumbira m'dzina la Mulungu wokhala ndi moyo mpaka muyaya, amene adalenga thambo lakumwamba ndi zonse zokhala kumeneko, dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo, ndiponso nyanja ndi zonse zokhala m'menemo. Mngeloyo kulumbira kwake adati, “Pasakhalenso zochedwa tsopano.
7
Pamene mngelo wachisanu ndi chiŵiri adzaliza lipenga lake, zachinsinsi zimene Mulungu adakonzeratu zidzachitika, monga momwe Iye adaalonjezera kwa atumiki ake aja, aneneri.”
8
Pamenepo mau amene ndidaamva kuchokera Kumwamba adandilankhulanso, adati, “Pita, katenge kampukutu kofutukula kaja kamene kali m'manja mwa mngelo woponda pa nyanja ndi pa mtunda uja.”
9
Ndidapitadi kwa mngeloyo nkumupempha kuti andipatse kampukutuko. Iye adati, “Kwaya, idya. M'mimba mwako kaziŵaŵa, koma m'kamwa mwako kazizuna ngati uchi.”
10
Ndidalandira kampukutuko m'manja mwa mngelo uja, ndipo ndidadyadi. M'kamwamu kankazuna ngati uchi, koma nditakameza, m'mimbamu munkaŵaŵa.
11
Pamenepo adandiwuza kuti, “Uyenera kulengezanso za mitundu yambiri ya anthu, za zilankhulo zosiyanasiyana, ndi za mafumu ambiri.”
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22