bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Revelation 8
Revelation 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 9 →
1
Pomaliza Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu ndi chiŵiri. Pamenepo onse Kumwamba adangoti chete pa hafu la ora.
2
Kenaka ndidaona angelo asanu ndi aŵiri aja amene amaimirira pamaso pa Mulungu, akupatsidwa malipenga asanu ndi aŵiri.
3
Mngelo wina adabwera naimirira ku guwa lansembe ali ndi chofukizira chagolide. Adapatsidwa lubani wambiri kuti ampereke pamodzi ndi mapemphero a anthu a Mulungu pa guwa lagolide patsogolo pa mpando wachifumu uja.
4
Pamodzi ndi mapemphero a anthu a Mulunguwo, utsi wa lubaniyo udakwera pamaso pa Mulungu kuchokera m'manja mwa mngelo uja.
5
Pamenepo mngeloyo adatenga chofukiziracho nachidzaza ndi moto wochokera ku guwa lija. Adachiponya pa dziko lapansi, ndipo nthaŵi yomweyo padachitika mabingu, phokoso, mphezi ndi chivomezi.
6
Tsono angelo asanu ndi aŵiri amene anali ndi malipenga asanu ndi aŵiri aja adakonzeka kuti alize malipengawo.
7
Mngelo woyamba adaliza lipenga lake. Atatero, padadza matalala ndi moto zosanganizika ndi magazi. Zimenezi zidaponyedwa pa dziko lapansi, ndipo chimodzi mwa zigawo zitatu za dziko ndi za mitengo chidapsa. Pamenepo padapsanso udzu wonse wauŵisi.
8
Mngelo wachiŵiri adaliza lipenga lake. Atatero, chinthu chooneka ngati chiphiri choyaka moto chidaponyedwa m'nyanja.
9
Pomwepo chimodzi mwa zigawo zitatu za nyanja chidasanduka magazi, ndipo chimodzi mwa zigawo zitatu za zolengedwa zonse zamoyo zam'nyanjamo chidafa. Chimodzinso mwa zigawo zitatu za zombo chidaonongeka.
10
Mngelo wachitatu adaliza lipenga lake. Atatero chinyenyezi choyaka ngati muuni chidagwa kuchokera kuthambo. Chidagwera pa chimodzi mwa zigawo zitatu za mitsinje, ndi pa akasupe.
11
Chinyenyezicho dzina lake ndi “Kuŵaŵa”. Chimodzi mwa zigawo zitatu za madzi chidasanduka choŵaŵa, mwakuti anthu ambiri adafa nawo madziwo chifukwa cha kuŵaŵa kwakeko.
12
Mngelo wachinai adaliza lipenga lake. Atatero chimodzichimodzi mwa zigawo zitatuzitatu za dzuŵa, za mwezi ndi za nyenyezi chidamenyedwa. Zitachitika zimenezi, chimodzi mwa zigawo zitatu za zonsezo chidada. Panalibenso kuŵala pa chimodzi mwa zigawo zitatu za usana, ndi chimodzimodzinso usiku.
13
Pambuyo pake ndidayang'ana, ndipo ndidaona chiwombankhanga chikuuluka mu mlengalenga, ndipo ndidamva chikulira mokweza kuti, “Tsoka! Tsoka! Tsoka kwa anthu onse okhala pa dziko lapansi, angelo atatu otsala aja akangoliza malipenga ao.”
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22