bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Revelation 2
Revelation 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 3 →
1
“Mtsogoleri wa mpingo wa ku Efeso umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa uja wanyamula nyenyezi zisanu ndi ziŵiri m'dzanja lake lamanja, ndi kuyenda pakati pa ndodo za nyale zisanu ndi ziŵiri zagolide zija.
2
Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndikudziŵa kuti mwakhala mukugwira ntchito kolimba, ndipo kuti muli ndi kupirira kosatepatepa. Ndikudziŵanso kuti anthu ochimwa simungaŵalekerere. Anthu amene amadzitcha atumwi, pamene sali atumwi konse, mwaŵayesa, ndipo mwaŵapeza kuti ngonama.
3
Ndinudi opirira kolimba, ndipo mwasauka kwambiri chifukwa cha Ine, osatopa.
4
Komatu pokudzudzulirani palipo: ndi apa pakuti mwasiya chikondi chimene munkandikonda nacho poyamba paja.
5
Kumbukirani tsono kuti munali okwera kwambiri musanagwe; nchifukwa chake mutembenuke mtima, muzichitanso zija munkachita poyambazi. Mukapanda kutero, ndidzabwera nkudzachotsa ndodo ya nyale yanu pamalo pake.
6
Komabe chokomera chanu ndi ichi chakuti, mumadana ndi zochita za Anikolai, zimene inenso ndimadana nazo.
7
“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, ndidzampatsa mwai wodya zipatso za mtengo wopatsa moyo umene uli ku Paradizo la Mulungu Kumwamba.”
8
“Mtsogoleri wa mpingo wa ku Smirina umlembere kuti: Naŵa mau ochokera kwa Iye amene ali Woyamba ndiponso Wotsiriza, amene adaafa nkukhalanso moyo.
9
Akuti: Ndikudziŵa masautso anu ndiponso umphaŵi wanu, koma kwenikweni ndinu olemera. Ndikudziŵanso zomwe amakusinjirirani anthu amene amanama kuti ndi Ayuda, pamene sali Ayuda konse, koma ndi a mpingo wa Satana.
10
Musachite nazo mantha zoŵaŵa zimene mukukakumana nazo. Ndithu enanu Satana adzakuponyetsani m'ndende kuti akuyeseni, ndipo mudzazunzika pa masiku khumi. Khalani okhulupirika mpaka kufa, ndipo ndidzakupatsani moyo ngati mphotho yanu.
11
“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, siidzamkhudza imfa yachiŵiri.”
12
“Mtsogoleri wa mpingo wa ku Pergamo umlembere kuti: Naŵa mau ochokera kwa uja ali ndi lupanga lakuthwa konsekonse lija.
13
Akuti: Ndikudziŵako kumene inuyo mumakhala, ndiye kuti kumene kuli mpando wachifumu wa Satana. Inu ndinu okhulupirika kwa Ine, simudataye chikhulupiriro chanu, ngakhale pa nthaŵi ya Antipa, mboni yanga, munthu wanga wokhulupirika. Paja iye uja adamuphera kwanu komwe, kumene amakhala Satana.
14
Koma pali zinthu zingapo zoti ndikudzudzulireni. Kwanuko muli ndi anthu ena otsata chiphunzitso cha Balamu mneneri wonama uja. Iye uja adaaphunzitsa mfumu Balaki kukopa Aisraele kuti azidya za nsembe zoperekedwa kwa mafano, ndi kumachita chigololo.
15
Chimodzimodzi inuyo, muli nawonso anthu ena otsata chiphunzitso cha Anikolai.
16
Mutembenuke mtima tsono. Mukapanda kutero, ndidzabwera kwanuko posachedwa, ndipo ndidzakuthirani nkhondo ndi lupanga lotulukira m'kamwa mwanga lija.
17
“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, ndidzampatsako chakudya chobisika cha mana. Ndidzampatsanso mwala woyera wolembedwapo dzina latsopano, lodziŵa iye yekha, osati wina aliyense.”
18
“Mtsogoleri wa mpingo wa ku Tiatira umlembere kuti: Naŵa mau ochokera kwa Mwana wa Mulungu, uja ali ndi maso onyezimira ngati malaŵi a moto, ndi mapazi onga chitsulo choŵala.
19
Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndikudziŵa chikondi chanu, kukhulupirika kwanu, kutumikira kwanu, ndi kupirira kwanu kosatepatepa. Ndikudziŵa kuti ntchito zanu zatsopano nzabwino koposa zoyamba zija.
20
Komatu pokudzudzulirani palipo: ndi apa pakuti mumamlekerera mkazi uja Yezebele, amene amadzitcha mneneri. Iye uja amanyenga atumiki anga nkumaŵaphunzitsa kuti azichita dama ndi kumadya zansembe zoperekedwa kwa mafano.
21
Ndidampatsa nthaŵi kuti atembenuke mtima, koma safuna kutembenuka ndi kuleka kusakhulupirika kwake.
22
Tsono ndidzamgwetsa m'matenda, ndipo ochita naye dama lakelo, ndidzaŵagwetsa m'masautso aakulu, akapanda kutembenuka mtima ndi kuleka zoipa zonse zimene ankachita naye.
23
Ana akenso ndidzaŵapha. Motero mipingo yonse idzazindikira kuti Ine ndine uja ndimadziŵa za m'mitima mwa anthu ndi za m'maganizo mwao. Aliyense mwa inu ndidzachita naye molingana ndi ntchito zake.
24
“Koma enanu a ku Tiatira simudatsate nao chiphunzitso choipachi, ndipo simudaphunzireko zimene iwo amati zinsinsi zozama za Satana. Kwa inu mau anga ndi akuti sindikuwonjezerani malamulo ena,
25
koma inu, mungogwiritsa zimene mudaphunzira, mpaka Ine ndidzabwere.
26
Amene adzapambane ndi kuchita mpaka potsiriza zimene ndamlamula, ndidzampatsa ulamuliro pa mitundu yonse ya anthu.
27
Adzailamulira ndi ndodo yachitsulo, nadzaiphwanyaphwanya ngati mbiya. Ulamuliro umenewu ndi womwe Ine ndidaulandira kwa Atate.
28
Ndidzampatsanso Nthanda, nyenyezi yoŵala m'mamaŵa ija.
29
“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi.”
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22