bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Revelation 9
Revelation 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 10 →
1
Pamenepo mngelo wachisanu adaliza lipenga lake. Atatero ndidaona nyenyezi itagwa pansi kuchokera ku thambo. Idapatsidwa kiyi ya dzenje lopita ku Chiphompho chakuya.
2
Nyenyeziyo idatsekula padzenjepo, ndipo padatuluka utsi wonga wam'ching'anjo. Dzuŵa ndi thambo zidada chifukwa cha utsi wotuluka m'dzenjewo.
3
Muutsimo mudatuluka dzombe kukaloŵa m'dziko lapansi, ndipo dzombelo lidapatsidwa mphamvu zoluma zonga za zinkhanira za pa dziko lapansi.
4
Dzombelo lidalamulidwa kuti lisaononge udzu wa pa dziko lapansi, kapena chomera chilichonse, kapena mtengo uliwonse. Lidaloledwa kungoononga anthu opanda chizindikiro cha Mulungu chija pamphumi pao.
5
Silidaloledwe kuŵapha, koma kungoŵazunza pa miyezi isanu. Kuŵaŵa kwake kwa mazunzowo kunkalingana ndi ululu wa chinkhanira chikaluma munthu.
6
Masiku amenewo anthuwo adzafunafuna imfa, koma osaipeza. Adzafunitsitsa kufa, koma imfa izidzaŵathaŵa.
7
Dzombelo linkaoneka ngati akavalo okonzekera nkhondo. Pamitu pake panali ngati zisoti zaufumu zagolide, nkhope zake ngati za anthu.
8
Tsitsi lake linali litalilitali ngati la azimai, mano ake ngati a mkango.
9
Pachifuwa pake panali mamba onga ngati malaya achitsulo apachifuwa. Kulira kwa mapiko ake kunali ngati kwa magareta ankhondo ambiri okokedwa ndi akavalo othamangira ku nkhondo.
10
Dzombelo lili ndi michira ngati zinkhanira, ndipo lili ndi mbola. Mphamvu yake ija yopwetekera anthu pa miyezi isanu inali kumichira kwake.
11
Mfumu yake inali mngelo wolamulira Chiphompho chija. Pa Chiyuda dzina lake ndi Abadoni, pa Chigriki ndi Apoliyoni (tanthauzo lake ndiye kuti, “Woononga uja”.)
12
Tsoka loyamba lija lapita. Atsalabe masoka enanso aŵiri oyenera kubwera.
13
Mngelo wachisanu ndi chimodzi adaliza lipenga lake. Atatero ndidamva liwu lochokera ku ngodya zinai za guwa lagolide lija lokhala pamaso pa Mulungu.
14
Liwulo lidauza mngelo wachisanu ndi chimodzi wokhala ndi lipenga uja, kunena kuti, “Amasule angelo anai aja amene ali omangidwa pa mtsinje waukulu wa Yufurate.”
15
Adaŵamasuladi angelowo kuti akaphe chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu onse. Angelowo Mulungu anali ataŵakonzera ora lake, tsiku lake, mwezi wake ndi chaka chake.
16
Ndidamva chiŵerengero cha ankhondo a pa akavalo aja, kuti chinali mamiliyoni 200.
17
M'masomphenya momwemo, akavalowo ndidaŵaona motere: okwerapo ake adaavala malaya achitsulo apachifuwa a maonekedwe ofiira ngati moto, obiriŵira ngati utsi, ndi achikasu ngati miyala ya sulufure. Mitu ya akavalowo inali ngati ya mikango, ndipo m'kamwa mwao munkatuluka moto, utsi ndi sulufure.
18
Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu onse chidaphedwa ndi miliri itatu iyi: wa moto, wa utsi ndi wa sulufure, zimene zinkatuluka m'kamwa mwa akavalo aja.
19
Akavalowo mphamvu zao zinali m'kamwa ndi ku michira. Michira yaoyo inali ngati njoka, yokhala ndi mitu yopwetekera anthu.
20
Anthu ena onse otsala, amene sadaphedwe ndi miliri ija, sadatembenuke mtima kuti asiye ntchito za manja ao. Sadaleke kupembedza mizimu yoipa, ndi mafano agolide, asiliva, amkuŵa, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda.
21
Anthuwo sadatembenukenso kuti aleke kupha anzao, ufiti, dama ndi kuba.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22