bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Revelation 4
Revelation 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 5 →
1
Pambuyo pake nditayang'ana, ndidaona pakhomo potsekuka Kumwamba. Ndipo ndidamva wina akulankhula nane ndi liwu lomwe ndidaamva poyamba lija, limene linkamveka ngati kulira kwa lipenga. Adandiwuza kuti, “Bwera Kumwamba kuno, ndidzakuwonetse zimene ziyenera kuchitika bwino lino.”
2
Nthaŵi yomweyo ndidagwidwa ndi Mzimu Woyera. Kumwambako ndidaona mpando wachifumu, wina atakhalapo pampandopo.
3
Amene adaakhala pampandoyo, maonekedwe ake anali oŵala ngati miyala yoyera ndi yofiira, yonyezimira. Pozungulira mpando wachifumuwo panali utawaleza, maonekedwe ake ngati mwala woŵala, wobiriŵira.
4
Pozungulira mpando wachifumu pomwepo panali mipando inanso 24 yachifumu, ndipo pamipandopo padaakhala Akuluakulu 24, atavala zovala zoyera, ali ndi zisoti zachifumu zagolide pamutu.
5
Mu mpando wachifumu munkatuluka mphezi, phokoso ndi mabingu. Patsogolo pake pa mpando womwewo pankayaka miyuni isanu ndi iŵiri, ndiye kuti mizimu ya Mulungu isanu ndi iŵiri.
6
Patsogolo pake panalinso ngati nyanja yagalasi yonyezimira. Pakatimpakati, pozungulira mpando wachifumu uja, panali Zamoyo zinai, zokhala ndi maso ponseponse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe.
7
Chamoyo choyamba chinkaoneka ngati mkango, chachiŵiri ngati ng'ombe, chachitatu chinali ndi nkhope ya munthu, ndipo chachinai chinkaoneka ngati chiwombankhanga chouluka.
8
Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo zinali ndi maso ponseponse ndi m'kati momwe. Usana ndi usiku zimaimba mosalekeza kuti, “Ngoyera, ngoyera, ngoyera Ambuye, Mulungu Mphambe, amene analipo, amene alipo, amene alikudza.”
9
Zamoyozo zimapereka ulemerero, ulemu ndi mayamiko kwa uja wokhala pa mpando wachifumuyu, amene ali ndi moyo wamuyaya.
10
Pamene zikuchitika zimenezi, Akuluakulu 24 aja amadzigwetsa pamaso pa wokhala pa mpando wachifumuyo, ndi kumpembedza wokhala ndi moyo wamuyayayo. Ndipo amaponya pansi zisoti zao zaufumu patsogolo pa mpando wachifumuwo ndi kunena kuti,
11
“Inu Ambuye athu ndi Mulungu wathu, ndinu oyenera kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu, pakuti ndinu mudalenga zinthu zonse. Mudafuna kuti zonsezo zikhalepo, ndipo zidalengedwa.”
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22