bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Revelation 11
Revelation 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 12 →
1
Pambuyo pake adandipatsa bango loyesera, longa ndodo, nandiwuza kuti, “Nyamuka, kayese Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, ndipo ukaŵerenge opembedza m'Nyumbamo.
2
Koma bwalo la kunja kwa Nyumbayo ulisiye, osaliyesa. Bwalo limeneli lidapatsidwa kwa anthu akunja, ndipo iwowo adzaupondereza Mzinda woyerawo pa miyezi 42.
3
Ndidzatuma mboni zanga ziŵiri zovala chiguduli, kuwonetsa chisoni, kuti zidzalalike mau ochokera kwa Mulungu pa masiku 1,260.”
4
Mboni ziŵirizo ndi mitengo iŵiri ija ya olivi, ndi ndodo za nyale ziŵiri zija zimene zili pamaso pa Ambuye olamulira dziko lonse lapansi.
5
Wina aliyense akafuna kuzipweteka mbonizo, moto umatuluka kukamwa kwao nkuwononga adani aowo. Ndipo munthu aliyense wofuna kuzipweteka, adzayenera kuphedwa mwa njira yomweyo.
6
Mbonizo zili ndi mphamvu zomanga mvula kuti isagwe masiku amene iwo akulalika mau ochokera kwa Mulungu. Zili ndi mphamvu zosandutsira madzi kuti akhale magazi. Ndipo zili ndi mphamvu zodzetsera mliri uliwonse pa dziko lapansi, nthaŵi iliyonse imene zingafune.
7
Tsono mbonizo zikadzatsiriza umboni waowo, chilombo chotuluka m'Chiphompho chija chidzachita nazo nkhondo. Chidzazigonjetsa nkuzipha.
8
Mitembo yao idzakhala ili thasa pa mseu wa mu mzinda waukulu, kumene Ambuye ao adapachikidwa pa mtanda. Mokuluŵika mzindawo umatchedwa “Sodomu” mwina “Ejipito”.
9
Anthu a mitundu yonse, a mafuko onse ndiponso a zilankhulo zonse azidzayang'anitsitsa mitemboyo masiku atatu ndi hafu, akukana kuti iikidwe m'manda.
10
Ndipo anthu onse okhala pa dziko lapansi adzakondwera nazo zimenezi. Adzachita chikondwerero ndi kutumizirana mphatso, chifukwa aneneri aŵiriŵa ankaŵasautsa kwambiri anthu okhala pa dziko lapansiwo.
11
Koma atatha masiku atatu ndi hafu aja, mpweya wopatsa moyo, wochokera kwa Mulungu, udaloŵa mwa aneneriwo. Motero adaimirira, ndipo onse amene adaŵaona adagwidwa ndi mantha aakulu.
12
Aneneri aja adamva mau amphamvu ochokera Kumwamba oŵauza kuti, “Bwerani kuno.” Iwowo adapitadi Kumwamba mu mtambo, adani ao aja akuŵapenya.
13
Nthaŵi yomweyo kudachita chivomezi chachikulu, mwakuti chimodzi mwa zigawo khumi za mzinda chidagwa, ndipo anthu zikwi zisanu ndi ziŵiri adaphedwa ndi chivomezicho. Otsalawo adaopsedwa kwambiri nayamba kutamanda Mulungu wa Kumwamba.
14
Tsoka lachiŵiri lija lapita tsopano, koma lachitatu likubwera posachedwa.
15
Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chiŵiri adaliza lipenga lake. Atatero kumwamba kudamveka mau okweza. Mauwo adati, “Tsopano mphamvu zolamulira dziko lapansi zili m'manja mwa Ambuye athu ndi mwa Wodzozedwa wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”
16
Pamenepo Akuluakulu 24 aja okhala pa mipando yao yachifumu pamaso pa Mulungu, adadzigwetsa chafufumimba napembedza Mulungu.
17
Adati, “Ambuye Mulungu, Mphambe, Inu amene mulipo ndipo munaliponso kale, tikukuyamikani chifukwa mwaonetsa mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwayamba kukhazikitsa ufumu wanu.
18
Anthu akunja adakalipa, koma yafika nthaŵi yoonetsa mkwiyo wanu, ndiye kuti nthaŵi yoweruza anthu akufa. Yafika nthaŵi yoti mupereke mphotho kwa atumiki anu, aneneri, ndi kwa anthu anu, ndiye kuti onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu, amene amaopa dzina lanu. Yafika nthaŵi yoti muŵaononge amene akuwononga dziko lapansi.”
19
Pamenepo mudatsekuka m'Nyumba ya Mulungu Kumwamba, ndipo bokosi lachipangano lidaoneka m'Nyumbamo. Kenaka kudachita mphezi, phokoso, mabingu ndi chivomezi, ndipo kudagwa matalala akuluakulu.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22