bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Revelation 22
Revelation 22
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
1
Pambuyo pake mngelo uja adandiwonetsa mtsinje wa madzi opatsa moyo. Mtsinjewo madzi ake anali onyezimira ngati galasi, ndipo unkachokera ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uja.
2
Unkayenda pakati pa mseu wamumzinda uja. Pa mbali zonse ziŵiri za mtsinje panali mtengo wopatsa moyo. Mtengowo umabala zipatso khumi ndi kaŵiri pa chaka, kamodzi mwezi uliwonse, ndipo masamba ake ndi ochiritsa anthu a mitundu yonse.
3
Mumzindamo simudzapezekanso kanthu kalikonse kotembereredwa ndi Mulungu. Mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uja udzakhala m'menemo, ndipo atumiki ake adzampembedza.
4
Iwo azidzaona nkhope yake, ndipo dzina lake lidzakhala lolembedwa pamphumi pao.
5
Sikudzakhalanso usiku, ndipo sipadzafunikanso kuŵala kwa nyale kapena kuŵala kwa dzuŵa, pakuti Ambuye Mulungu adzakhala kuŵala kwake, ndipo iwo adzakhala mafumu olamulira mpaka muyaya.
6
Pambuyo pake mngelo uja adandiwuza kuti, “Mau aŵa ndi oona ndiponso oyenera kuŵakhulupirira. Ndipo Ambuye Mulungu amene amalankhulitsa aneneri, adatuma mngelo wao kuti aonetse atumiki ao zimene zidzachitike posachedwa.”
7
Yesu akuti, “Mvetsetsani, ndikubwera posachedwa. Ngwodala munthu amene amatsata mau a m'buku lino oneneratu zam'tsogolo.”
8
Ndine, Yohane, amene ndidamva ndi kuwona zimenezi. Ndipo nditazimva ndi kuziwona, ndidadzigwetsa ku mapazi a mngelo uja amene adandiwonetsa zimenezi. Ndidaati ndimpembedze,
9
koma iye adandiwuza kuti, “Zimenezo iyai. Ndine mtumiki chabe, ngati iwe wemwe, ngati abale ako aneneri, ndiponso ngati onse otsata mau olembedwa m'buku lino. Iwe pembedza Mulungu.”
10
Adandiwuzanso kuti, “Usabise mau a m'buku lino oneneratu zam'tsogolo, pakuti nthaŵi yake ili pafupi.
11
Wochita zoipa apitirire kuchita zoipazo, ndipo wodetsedwa ndi zonyansa apitirire kudzidetsa ndi zonyansazo. Wochita zabwino apitirire kuchita zabwinozo, ndipo woyera mtima apitirire kukhala woyera mtima.”
12
Yesu akuti, “Mvetsetsani, ndikubwera posachedwa. Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense molingana ndi zimene adachita.
13
Alefa ndi Omega ndine. Ndiye kuti Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chimalizo ndine.”
14
Ngodala amene amachapa mikanjo yao, kuti aloledwe kudya zipatso za mtengo wopatsa moyo, ndiponso kuloŵa mu mzinda kudzera pa zipata zija.
15
Koma ochita zautchisi, zaufiti, zadama, zopha anzao, zopembedza mafano, ndi okonda zabodza nkumazichita, adzakhala kunja kwa mzindawo.
16
“Ine, Yesu, ndatuma mngelo wanga kuti akufotokozereni zimenezi ndipo zithandize mipingo. Ine ndine chiphukira chotuluka mwa mfumu Davide, ndine chidzukulu chake. Ndine Nthanda, nyenyezi yoŵala m'mamaŵa!”
17
Mzimu Woyera ndi Mkwati wamkazi akuti, “Bwerani!” Aliyense womva mauŵa, anenenso kuti, “Bwerani!” Aliyense womva ludzu, abwere. Aliyense woŵafuna, aŵalandire mwaulere madzi opatsa moyo.
18
Ine Yohane, ndikuchenjeza aliyense womva mau a m'buku lino oneneratu zam'tsogolo. Wina akadzaonjezerapo kanthu pa mau ameneŵa, Mulungu adzamuwonjezera miliri ija yalembedwa m'buku munoyi.
19
Ndipo wina akadzachotsapo kanthu pa mau a m'buku lino loneneratu zam'tsogolo, Mulungu adzamchotsera gawo lake la zipatso za mtengo wopatsa moyo uja, ndi malo ake omwe mu Mzinda Woyera uja, monga zalembedwera m'buku muno.
20
Amene akufotokoza zimenezi akuti, “Indedi, ndikubwera posachedwa.” Inde, bwerani, Ambuye Yesu.
21
Ambuye Yesu akukomereni mtima nonse.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22