bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Revelation 16
Revelation 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 17 →
1
Pambuyo pake ndidamva mau amphamvu ochokera m'Malo Opatulika aja. Adauza angelo asanu ndi aŵiri aja kuti, “Pitani, kathireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu, umene uli m'mikhate isanu ndi iŵiri ija.”
2
Motero mngelo woyamba adakakhuthulira za mumkhate mwake pa dziko lapansi. Pamenepo zilonda zonyansa ndi zopweteka zidabuka pa anthu onse aja, amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, napembedza fano lake.
3
Pambuyo pake mngelo wachiŵiri adakhuthulira za mumkhate mwake pa nyanja. Pomwepo madzi ake adasanduka magazi, magazi ake ngati a munthu wakufa. Ndipo zamoyo zonse za m'nyanjamo zidafa.
4
Kenaka mngelo wachitatu adakhuthulira za mumkhate mwake pa mitsinje, ndi pa akasupe a madzi. Pomwepo madziwo adasanduka magazi.
5
Tsono ndidamva mngelo wolamulira madzi uja akunena kuti, “Mwachita chilungamo m'mene mwaweruza motero, Inu Woyera uja, amene mulipo ndipo munalipo kale.
6
Pakuti iwo aja adakhetsa magazi a anthu a Mulungu, ndi a aneneri, nchifukwa chake mwaŵapatsa magazi kuti amwe. Zimenezi ndi zimene zikuŵayenera.”
7
Pamenepo ndidamva mau ochokera ku guwa lansembe. Adati, “Zoonadi Ambuye, Mulungu Mphambe, chiweruzo chanu chilichonse nchoona ndi cholungama.”
8
Pambuyo pake mngelo wachinai adakhuthulira za mumkhate mwake pa dzuŵa. Nthaŵi yomweyo lidaloledwa kupsereza anthu ndi moto wake.
9
Anthu adapserera nako kutentha koopsako, ndipo adayamba kunyoza dzina la Mulungu, amene ali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi. Komabe iwo sadatembenuke mtima kuti azitamanda Mulungu.
10
Kenaka mngelo wachisanu adakhuthulira za mumkhate mwake pa mpando wachifumu wa chilombo chija. Nthaŵi yomweyo mdima udagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu ankadziluma lilime chifukwa cha ululu umene ankaumva.
11
Adayamba kunyoza dzina la Mulungu wa Kumwamba chifukwa cha zoŵaŵa zao ndi zilonda zao. Komabe sadatembenuke mtima ndi kuleka zochita zao.
12
Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chimodzi adakhuthulira za mumkhate mwake pa mtsinje waukulu uja wa Yufurate. Pomwepo madzi ake adaphwa, kuti pakhale njira yodzera mafumu ochokera kuvuma.
13
Kenaka ndidaona mizimu yonyansa itatu, yonga achule, ikutuluka wina m'kamwa mwa chinjoka chija, wina m'kamwa mwa chilombo chija, wina m'kamwa mwa mneneri wonama uja.
14
Imeneyi ndi ija timati mizimu yoipa imene imachita zozizwitsa. Imapita ponseponse kwa mafumu a pa dziko lapansi kukaŵaitana kuti adzabwere ku nkhondo ya pa tsiku lalikulu lija la Mulungu Mphambe.
15
“Mvetsetsani! Ndikubwera ngati mbala. Ngwodala munthu amene ali maso, nasunga zovala zake, kuwopa kuti angamayende osavala, ndipo anthu angaone maliseche ake.”
16
Pamenepo mizimu ija idasonkhanitsa mafumu aja ku malo amene pa Chihebri amatchedwa “Armagedoni.”
17
Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chiŵiri adakhuthulira za mumkhate mwake mu mlengalenga. Pomwepo kudamveka mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu wa m'Nyumba ya Mulungu. Adati, “Kwatha!”
18
Nthaŵi yomweyo kudachita mphezi, phokoso ndi mabingu. Kudachitanso chivomezi champhamvu. Chilengedwere cha anthu pa dziko lapansi sikudachitikeponso chivomezi chotero: chimenecho chinali choopsa zedi.
19
Mzinda waukulu uja udagaŵika patatu, ndipo mizinda ya m'maiko ena onse idagwa. Mulungu adakumbukira Babiloni wamkulu uja, ndipo adamumwetsa chikho cha vinyo wa mkwiyo wake waukali.
20
Zilumba zonse zidafafanizika, mapiri osaonekanso.
21
Matalala akuluakulu adagwa pa anthu kuchokera kumwamba. Lililonse kulemera kwake pafupi makilogaramu 45. Ndipo anthu adanyoza Mulungu chifukwa cha mliri wa matalalawo, pakuti mliriwo unali woopsadi.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22