bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Revelation 7
Revelation 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 8 →
1
Pambuyo pake ndidaona angelo anai ataimirira pa mbali zinai za dziko lapansi. Anali atagwira mphepo zinai za dziko lapansi kuti ndi imodzi yomwe isaombe pa dziko, kapena pa nyanja, kapena pa mtengo uliwonse.
2
Kenaka ndidaona mngelo wina akukwera kuchokera kuvuma, ali ndi chidindo cha Mulungu wopatsa moyo. Mokweza mau adafuulira angelo anai aja amene Mulungu adaaŵapatsa mphamvu yoonongera dziko ndi nyanja.
3
Adaŵauza kuti, “Musaononge msanga dziko, kapena nyanja, kapenanso mitengo, tiyambe taŵalemba chizindikiro pa mphumi atumiki a Mulungu wathu.”
4
Tsono ndidamva chiŵerengero cha olembedwa chizindikiro aja. Chidakwanira zikwi 144, ndipo olembedwa chizindikirowo anali a m'fuko lililonse la Aisraele.
5
Olembedwa chizindikiro: A m'fuko la Yuda anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Rubeni anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Gadi anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
6
A m'fuko la Asere anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Nafutali anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Manase anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
7
A m'fuko la Simeoni anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Levi anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Isakara anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
8
A m'fuko la Zebuloni anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Yosefe anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Benjamini anali zikwi khumi ndi ziŵiri.
9
Pambuyo pake nditayang'ana, ndidaona chinamtindi cha anthu osaŵerengeka. Anthuwo anali ochokera m'mitundu yonse ya anthu, ndi m'mafuko onse, ndipo anali a zilankhulo zonse. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja ndi pamaso pa Mwanawankhosa uja; anali atavala mikanjo yoyera, nthambi zakanjedza zili m'manja.
10
Ankafuula mokweza mau kuti, “Chipulumutso nchochokera kwa Mulungu wathu wokhala pa mpando wachifumu, ndiponso kwa Mwanawankhosa.”
11
Angelo onse adaimirira kuzungulira mpando wachifumu uja, kuzunguliranso Akuluakulu aja ndi Zamoyo zinai zija. Angelowo adadzigwetsa chafufumimba patsogolo pa mpando wachifumuwo, napembedza Mulungu.
12
Adati, “Amen! Mulungu wathu alandire matamando, ulemerero, nzeru, chiyamiko, ulemu, mphamvu ndi nyonga mpaka muyaya. Amen.”
13
Pamenepo mmodzi mwa Akuluakulu aja adandifunsa kuti, “Kodi ovala mikanjo yoyeraŵa ndani, ndipo achokera kuti?”
14
Ine ndidati, “Mbuyanga, mukudziŵa ndinu.” Ndipo iye adandiwuza kuti, “Ameneŵa ndi amene adapambana m'masautso aakulu aja. Adachapa mikanjo yao ndi kuiyeretsa m'magazi a Mwanawankhosa.
15
“Nchifukwa chake ali pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu, ndipo amampembedza m'Nyumba mwake usana ndi usiku. Wokhala pa mpando wachifumu uja adzakhala ngati hema lao loŵateteza.
16
Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu. Sadzaombedwanso ndi dzuŵa kapena kusauka ndi kutentha.
17
Pakuti Mwanawankhosa uja amene ali pakatikati pa mpando wachifumu, adzakhala Mbusa wao, adzaŵatsogolera ku akasupe a madzi amoyo. Ndipo Mulungu adzaŵapukuta misozi yonse m'maso.”
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22