bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Revelation 18
Revelation 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 19 →
1
Zitatha izi, ndidaona mngelo wina akutsika kuchokera Kumwamba. Anali ndi ulamuliro waukulu, ndipo pa dziko lonse lapansi padayera chifukwa cha kuŵala kwake.
2
Adafuula mokweza mau ndi kunena kuti, “Wagwa, wagwa Babiloni wotchuka uja! Wasanduka malo okhalamo mizimu yoipa, malo othaŵiramo mizimu yonse yonyansa, malo othaŵiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodedwa.
3
Pakuti adamwetsa anthu a mitundu yonse vinyo wa zilakolako zadama. Mafumu a pa dziko lonse lapansi adachita naye chigololo, ndipo anthu amalonda a pa dziko lonse lapansi ankalemererapo pa zolakalaka zake zodziwunjikira chuma.”
4
Pambuyo pake ndidamva mau ena ochokera Kumwamba. Adati, “Inu anthu anga, tulukanimo mumzindamo, kuti mungachimwire nawo pamodzi, miliri yao ingakugwereniko.
5
Paja machimo ake ndi ofika mpaka ku thambo, ndipo Mulungu wakhala akukumbukira ntchito zake zoipa.
6
Mumubwerezere monga momwe iye adakuchitirani. Mumchite zomwe iye adaŵachita ena zija, ndipo mumubwerezere moŵirikiza pa zimene iye adachita. M'chikho chimene iye ankamwetseramo ena, mumkonzeremo chakumwa moŵirikiza.
7
Monga momwe iye ankanyadira chuma ndi zosangalatsa, momwemonso mumsautse ndi kumliritsa. Iyeyo mumtima mwake amati, ‘Ine pano, mfumu! Sindine mkazi wamasiye, sindidzaona konse zondiliritsa.’
8
Nchifukwa chake miliri yomugwera idzamufikira pa tsiku limodzi. Miliriyo ndi iyi: nthenda, chisoni, ndi njala. Ndipo adzamtentha ndi moto. Pakuti ndi amphamvu Ambuye Mulungu amene amuweruza.”
9
Mafumu a pa dziko lapansi amene ankachita naye chigololo ndi kudzisangalatsa naye, adzalira ndi kumva naye chisoni kwambiri, poona utsi uli phaphapha, mzindawo ulikupsa.
10
Iwo adzaima patali chifukwa cha kuwopsedwa ndi mazunzo ake. Ndipo adzanena kuti, “Uli ndi tsoka, uli ndi tsoka, iwe Babiloni, mzinda wotchuka, mzinda wamphamvu! Pa ora limodzi lokha chilango chako chakugwera.”
11
Anthu amalonda a pa dziko lapansi adzalira ndi kumva naye chisoni kwambiri, pakuti palibenso wogula malonda ao.
12
Palibenso wogula malonda ao a golide, siliva, ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu; nsalu zoyera, zofiirira, zasilika ndi zamlangali; mitengo yamitundumitundu yonunkhira; zinthu zamitundumitundu zopangidwa ndi mnyanga wanjovu, ndiponso ndi mitengo yamtengowapatali; zinthu zopangidwa ndi mkuŵa, chitsulo ndi mwala wokongola;
13
zokometsera chakudya zamitundumitundu, mure, lubani ndi zofukiza zina, vinyo ndi mafuta, ufa wosalala ndi tirigu, ng'ombe ndi nkhosa, akavalo ndi ngolo, akapolo ndi akaidi.
14
Amalondawo adzamuuza kuti, “Zokoma zimene mtima wako unkalakalaka, zakuthera. Zachuma ndi zamakaka zako zonse zakutayikira, sudzazipezanso konse.”
15
Anthu ogulitsa zimenezi, amene adalemerera pa iye, adzaima patali chifukwa cha kuwopsedwa ndi mazunzo ake. Adzalira ndi kumva chisoni kwambiri,
16
ndipo adzanena kuti, “Uli ndi tsoka, uli ndi tsoka mzinda wotchukawu. Unkavala nsalu zoyera, zofiirira ndi zamlangali. Unkadzikongoletsa ndi golide, ndiponso ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu.
17
Koma pa ora limodzi lokha chuma chonsechi chaonongeka.” Onse oyendetsa zombo, onse oyenda pa nyanja, antchito apazombo, ndi onse oyendetsa malonda ao pa nyanja, adaima patali.
18
Poona utsi uli phaphapha, mzindawo ulikupsa, adafuula kuti, “Ndi mzinda uti udalinganapo ndi mzinda wotchukawu?”
19
Adadzithira fumbi kumutu, akulira ndi kumva chisoni kwambiri. Ankafuula kuti, “Uli ndi tsoka, uli ndi tsoka mzinda wotchukawu, mzinda umene anthu onse okhala ndi zombo zapanyanja adalemera nacho chuma chake. Koma pa ora limodzi lokha wasanduka bwinja.”
20
Kondwerani inu, Dziko la Kumwamba, chifukwa cha kuwonongeka kwake. Kondwerani inu, anthu a Mulungu, inu atumwi, ndi inunso aneneri. Pakuti Mulungu pakuulanga mzindawo, wautsutsa kuti ndi wolakwa pa zimene udakuchitani.
21
Pambuyo pake mngelo wina wamphamvu adanyamula mwala, kukula kwake ngati chimphero. Adauponya m'nyanja nanena kuti, “Umu ndi m'mene Babiloni, mzinda wotchuka uja, “Udzaponyedwere pansi mwamphamvu, ndipo sudzapezekanso.
22
Mwa iwe simudzamvekanso konse liwu la oimba zeze, kapena la akatswiri a zoimbaimba, kapena la oliza chitoliro kapena lipenga. Mwa iwe simudzapezekanso konse mmisiri wa ntchito iliyonse. Mwa iwe simudzamvekanso konse liwu la kupera.
23
Mwa iwe simudzaonekanso konse kuŵala kwa nyale. Mwa iwe simudzamvekanso konse mau a mkwati wamwamuna kapena wamkazi. Amalonda anali anthu otchuka kwambiri aja a pa dziko lapansi. Unkanyenga anthu a mitundu yonse ndi maula ako.”
24
Mu mzinda umenewo mudapezeka magazi a aneneri, ndi a anthu a Mulungu, ndi a anthu onse amene adaphedwa pa dziko lapansi.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22