bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Revelation 14
Revelation 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 15 →
1
Pambuyo pake nditayang'ana, ndidaona Mwanawankhosa ataimirira pa Phiri la Ziyoni. Pamodzi ndi Iye panali anthu zikwi 144, olembedwa dzina lake ndiponso dzina la Atate ake pamphumi pao.
2
Tsono ndidamva liwu lochokera kumwamba longa ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Liwu limene ndidaamvalo linkamveka ngati anthu akuimba azeze ao.
3
Anthu aja ankaimba nyimbo yatsopano pamaso pa mpando wachifumu uja ndi pamaso pa Zamoyo zinai zija, ndi Akuluakulu aja. Panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kuiphunzira nyimboyo, kupatula anthu zikwi 144 aja amene anali ataomboledwa mu ukapolo wa dziko lapansi.
4
Ndi ameneŵa amene ankadzisunga angwiro osadziipitsa ndi akazi. Ndi ameneŵa amene amatsata Mwanawankhosa uja kulikonse kumene akupita. Ndiwo amene adaomboledwa pakati pa anthu ena onse, kuti akhale oyambirira kuperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa uja.
5
Sadanenepo bodza konse. Alibe cholakwa.
6
Pambuyo pake ndidaona mngelo wina akuuluka mu mlengalenga. Anali ndi Uthenga Wabwino wamuyaya woti akalalike kwa anthu okhala pa dziko lapansi, kwa anthu a mtundu uliwonse, a fuko lililonse, ndi a chilankhulo chilichonse.
7
Mngeloyo adanena mokweza mau kuti, “Opani Mulungu ndi kumtamanda, pakuti yafika nthaŵi yoti aweruze anthu. Mumpembedze Iye amene adalenga thambo, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe a madzi.”
8
Padafika mngelo wina wachiŵiri wotsatana ndi woyamba uja. Adati, “Wagwa, wagwa Babiloni wotchuka uja, amene ankamwetsa anthu a mitundu yonse vinyo wa zilakolako zake zadama.”
9
Kenaka padafikanso mngelo wina wachitatu, wotsatana ndi aŵiri ena aja. Mokweza mau adati, “Aliyense wopembedza chilombo chija ndi fano lake, ndi kulembedwa chizindikiro pa mphumi kapena pa dzanja,
10
nayenso adzamwako vinyo wa ukali wa Mulungu. Vinyo wake adzathiridwa, popanda kanthu kochepetsa mphamvu yake, m'chikho cha mkwiyo wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto ndi miyala yasulufure yoyaka. Zimenezi zidzachitikira pamaso pa angelo a Mulungu, ndi Mwanawankhosa uja.
11
Utsi wa moto woŵazunzawo umakwera kumwamba mpaka muyaya. Anthu amene adapembedza chilombo chija ndi fano lake, ndiponso amene adalembedwa chizindikiro cha dzina lake chija, sapeza mpumulo usana kapena usiku.
12
“Pamenepa mpofunika kuti anthu a Mulungu akhale opirira, amene amatsata malamulo ake ndipo ali ndi chikhulupiriro mwa Yesu.”
13
Pambuyo pake ndidamva mau ochokera Kumwamba. Adati, “Lemba kuti, Ngodala anthu akufa amene kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo muno afa ali otumikira Ambuye.” Mzimu Woyera akuti, “Inde, ngodaladi. Akapumule ntchito zao zolemetsa, pakuti ntchito zaozo zimaŵatsata.”
14
Pambuyo pake nditayang'ana ndidaona mtambo woyera. Pamtambopo padaakhala wina ngati Mwana wa Munthu, kumutu atavala chisoti chaufumu chagolide, m'manjamu ali ndi chikwakwa chakuthwa.
15
Mngelo wina adatuluka m'Nyumba ya Mulungu nafuula ndi mau amphamvu kwa Uja wokhala pamtamboyu. Adati, “Gwiritsa ntchito chikwakwa chako, yambapo kudula dzinthu. Tsopano nyengo yamasika yafika, ndipo dzinthu dza pa dziko lapansi dzidacha kale.”
16
Pamenepo wokhala pamtambo uja adakayambadi ntchitoyo ndi chikwakwa chake, nadula dzinthu dzonse dza pa dziko lapansi.
17
Pambuyo pake mngelo wina adatuluka m'Nyumba ya Mulungu Kumwamba. Nayenso anali ndi chikwakwa chakuthwa.
18
Kenaka mngelo winanso, amene amalamulira moto, adatulukira kuchokera ku guwa lansembe. Adafuula ndi mau amphamvu kwa Uja wokhala ndi chikwakwa chakuthwa. Adati, “Gwiritsa ntchito chikwakwa chakocho, yambapo kudula mphesa za m'munda wamphesa wa pa dziko lapansi, pakuti mphesazo zidapsa kale.”
19
Pamenepo mngelo uja adakayambadi ntchitoyo ndi chikwakwa chake, nadula mphesa zonse za pa dziko lapansi, nkuziponya m'chopondera mphesa cha ukali woopsa wa Mulungu.
20
Mphesazo zidapondedwa m'chopondera mphesa kunja kwa mzinda. Ndipo m'chopondera mphesacho mudatuluka magazi nkumayenderera ngati mtsinje, kutalika kwake makilomita 300, kuzama kwake ngati mita ndi hafu.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22