bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Revelation 12
Revelation 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 13 →
1
Pambuyo pake kudaoneka chizindikiro chachikulu kuthambo: mai atavala dzuŵa, mapazi ake ataponda pa mwezi, pamutu pake pali chisoti chaufumu cha nyenyezi khumi ndi ziŵiri.
2
Maiyo anali ndi pathupi, ndipo pa nthaŵi yochira adalira nako mokuwa kupweteka kwa kubala.
3
Kudaonekanso chizindikiro china kuthambo: chinjoka chachikulu, chofiira, cha mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi; pa mutu uliwonse chitavala chisoti chaufumu.
4
Ndi mchira wake chidakokolola chimodzi mwa zigawo zitatu za nyenyezi zakuthambo, nkuzigwetsa pa dziko lapansi. Chinjokacho chidadzaimirira pamaso pa mai uja amene anali pafupi kubala mwana, kuti akangobadwa mwanayo, chimudye.
5
Maiyo adabala mwana wamwamuna, woyenera kudzalamulira anthu a mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo. Mwanayo adalandidwa kumanja kwa mai wake kupita naye kwa Mulungu ndi ku mpando wake wachifumu.
6
Apo mai uja adathaŵira ku chipululu. Kumeneko Mulungu adaakonzeratu malo ake, kuti akasamalidweko masiku 1,260.
7
Tsono kudabuka nkhondo Kumwamba, Mikaele ndi angelo ake kumenyana ndi chinjoka chija. Chinjokacho pamodzi ndi angelo ake chidatengana nawo,
8
koma onsewo adagonjetsedwa, mwakuti adataya malo ao Kumwamba.
9
Chinjoka chachikulu chija chidagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakale ija yotchedwa “Mdyerekezi” ndiponso “Satana”, wonyenga anthu a pa dziko lonse lapansi. Chidagwetsedwa pa dziko lapansi pamodzi ndi angelo ake onse.
10
Pamenepo ndidamva mau amphamvu Kumwamba akunena kuti, “Tsopano Mulungu wathu watipulumutsa. Waonetsa mphamvu zake ndi ufumu wake. Tsopano Wodzozedwa uja waonetsa ulamuliro wake. Woneneza abale athu uja wagwetsedwa pansi, amangokhalira kuŵaneneza kwa Mulungu wathu usana ndi usiku.
11
Abale athuwo adamgonjetsa ndi magazi a Mwanawankhosa uja, ndiponso ndi mau amene iwo ankaŵachitira umboni. Iwo adadzipereka kotheratu, kotero kuti sadaope ngakhale kufa.
12
Choncho kondwerani inu, Dziko la Kumwamba, ndi onse okhalamo. Koma muli ndi tsoka, inu dziko lapansi ndi nyanja, pakuti Satana adatsikira kwa inu, ali wokalipa kwambiri, chifukwa wadziŵa kuti yangomutsalira nthaŵi pang'ono.”
13
Tsono chinjoka chija chitaona kuti chagwetsedwa pa dziko lapansi, chidayamba kumpirikitsa mai uja amene anali atabala mwana wamwamuna.
14
Koma maiyo adapatsidwa mapiko aŵiri a chiwombankhanga chachikulu kuti athaŵire ku malo ake aja akuchipululu. Kumeneko adzasamalidwa zaka zitatu ndi hafu, kuwopa kuti chinjoka chija chingamuwone.
15
Pamenepo chinjokacho chidalavulira mai uja madzi ochuluka ngati mtsinje, kuti amkokolole.
16
Koma dziko lapansi lidamthandiza maiyo: lidayasama nkuumeza mtsinje umene chinjoka chija chidaalavula.
17
Apo chinjokacho chidamupsera mtima kwambiri mai uja, nkungochokapo kuti chikayambane ndi ana ena onse a maiyo, ndiye kuti anthu otsata malamulo a Mulungu ndi kuchitira Yesu umboni. Motero chidakaimirira pambali pa nyanja.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22