bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Revelation 13
Revelation 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 14 →
1
Pambuyo pake ndidaona chilombo chikuvuuka m'nyanja. Chinali ndi nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iŵiri. Pa nyanga iliyonse chidaavala chisoti chaufumu, ndipo pa mutu uliwonse panali dzina lonyoza Mulungu.
2
Chilombo chimene ndidaaonacho chinali ngati kambuku, mapazi ake ngati a chimbalangondo, kukamwa kwake ngati kwa mkango. Chinjoka chija chidaapatsa chilombocho mphamvu zake, mpando wake wachifumu, ndiponso ulamuliro waukulu.
3
Umodzi mwa mitu yake unkaoneka ngati uli ndi bala lofa nalo, koma balalo linali litapola. Pamenepo anthu onse ankachitsata chilombocho ali odabwa.
4
Adachipembedza chinjoka chija chifukwa chidaapatsa ulamuliro wake kwa chilombo chija. Nachonso chilombo chija adachipembedza nkumanena kuti, “Ndani angafanane ndi chilombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?”
5
Chilombo chija chidaloledwa kulankhula mau onyada ndi onyoza Mulungu mwachipongwe. Ndipo chidapatsidwa mphamvu zolamulira pa miyezi 42.
6
Tsono chidayamba kunena mau achipongwe onyoza Mulungu, dzina lake, malo ake okhalamo, ndi onse okhala Kumwamba.
7
Chidaloledwa kuŵathira nkhondo anthu a Mulungu ndi kuŵagonjetsa. Chidapatsidwanso mphamvu zolamulira anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi a chilankhulo chilichonse.
8
Onse okhala pa dziko lapansi adzachipembedza, ndiye kuti aliyense amene, chilengedwere dziko lapansi, dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo la Mwanawankhosa adaphedwa uja.
9
Ngati wina ali ndi makutu, amve.
10
Woyenera kutengedwa ku ukapolo, kuukapoloko akapitadi. Woyenera kuphedwa ku nkhondo, kunkhondoko akaphedwadi. Pamenepa ndiye pamene anthu a Mulungu ayenera kuwonetsa kupirira ndi kulimbika m'chikhulupiriro.
11
Kenaka ndidaona chilombo china chikutuluka pansi. Chinali ndi nyanga ziŵiri ngati mwanawankhosa, kulankhula kwake ngati kwa chinjoka.
12
Chinkalamulira pamaso pa chilombo choyamba chija ndi mphamvu zimene chilombo choyambacho chidaachipatsa. Chinkakakamiza dziko lapansi ndi onse okhalamo kuti azipembedza chilombo choyamba chija chimene bala lake lofa nalo lija linali litapola.
13
Chilombo chachiŵirichi chinkachita zozizwitsa kwambiri, mpaka kumadzetsa moto pa dziko lapansi kuchokera kumwamba, anthu akuwona.
14
Chinkanyenganso anthu okhala pa dziko lapansi ndi zozizwitsa zimene chidaaloledwa kuchita pamaso pa chilombo choyamba chija. Chinkauza anthu okhala pa dziko lapansiwo kuti apange fano lolemekezera chilombo chimene chidaavulazidwa ndi lupanga, koma nkukhalabe moyo.
15
Chidaaloledwa kuuzira mpweya wopatsa moyo mu fano la chilombo choyamba chija, kuti mpaka lizilankhula, ndi kuphetsa aliyense wosalipembedza.
16
Chinkakakamiza anthu onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu, olemera ndi osauka, mfulu ndi akapolo, kuti alembedwe chizindikiro pa dzanja lamanja kapena pa mphumi.
17
Chinkachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi, ndiye kuti dzina la chilombo choyamba chija, kapena nambala yotanthauza dzina lake.
18
Pano pafunika nzeru. Yemwe ali ndi nzeru atanthauze nambala ya chilomboyo, pakuti nambalayo ikutanthauza munthu. Nambala yake ndi 666.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22