bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hosea 1
Hosea 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 2 →
1
Pa nthaŵi ya ufumu wa Uziya, wa Yotamu, wa Ahazi ndi wa Hezekiya, mafumu a ku Yuda, ndiponso pamene Yerobowamu mwana wa Yowasi anali mfumu ya ku Israele, Chauta ankamupatsa uthenga Hoseya, mwana wa Beeri.
2
Pamene Chauta adalankhula koyamba kudzera mwa Hoseya, adamuuza kuti, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubale naye ana omwe adzakhalenso achiwerewere. Pakuti anthu a m'dziko muno akhala osakhulupirika, pakusiya Ine Chauta.”
3
Motero Hoseya adapita, nakakwatira mkazi, dzina lake Gomeri, mwana wa Dibulaimu. Mkaziyo adatenga pathupi, namubalira mwana wamwamuna.
4
Tsono Chauta adauza Hoseya kuti, “Umutche dzina loti Yezireele. Pakuti patapita kanthaŵi pang'ono, ndidzalanga banja la Yehu chifukwa cha anthu amene iye adaŵapha ku Yezireele, ndipo ndidzathetsa ufumu wa Israele.
5
Nthaŵi imeneyo ndidzathetsa mphamvu za Israele m'chigwa cha Yezireele.”
6
Gomeri adatenganso pathupi, nabala mwana wamkazi. Chauta adauza Hoseya kuti, “Umutche dzina loti ‘Sakondedwa,’ pakuti Israele sindidzamkondanso, ndipo sindidzamkhululukiranso.
7
Koma ndidzaonetsa chikondi kwa banja la Yuda, ndipo ndidzaŵapulumutsa ndi mphamvu zanga, Ine Chauta, Mulungu wao. Ndidzaŵapulumutsa osati pochita kumenya nkhondo ndi mauta, malupanga, akavalo ndi anthu okwera pa akavalo ai.”
8
Sakondedwa ataleka kuyamwa, Gomeri adatenganso pena pathupi, nabala mwana winanso wamwamuna.
9
Pamenepo Chauta adauza Hoseya kuti, “Umutche dzina loti ‘Si-anthu-anga’, pakuti inu Aisraele sindinunso anthu anga, ndipo Ine sindinenso Mulungu wanu.”
10
Komabe Aisraele adzachuluka ngati mchenga wakunyanja umene sangathe kuuyesa kapena kuuŵerenga. Pamalo pamene Mulungu adaanena anthuwo kuti “Sindinu anthu anga,” pomweponso adzaŵatchula kuti, “Ana a Mulungu Wamoyo.”
11
Anthu a ku Yuda ndi a ku Israele adzaŵasonkhanitsanso pamodzi, ndipo adzadzisankhira mtsogoleri mmodzi. Tsono adzatukuka m'dziko mwao, ndithu tsiku la Yezireele lidzakhala lalikulu kwambiri.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14