bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hosea 14
Hosea 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
1
Inu Aisraele, bwererani kwa Chauta, Mulungu wanu, pakuti mwagwa chifukwa cha machimo anu,
2
Bwererani kwa Chauta, ndipo mumpemphe kuti, “Mutikhululukire machimo athu onse. Mumvere pempho lathu ndipo tidzakuyamikani ndi mau otamanda.
3
Aasiriya sadzatipulumutsa, akavalo ankhondo sadzatiteteza. Chimene tidapanga ndi manja athu sitidzachitchulanso kuti, ‘Mulungu wathu,’ pakuti ndinu amene mumachitira chifundo amasiye.”
4
Chauta akuti, “Ndidzachiza matenda ao a kusakhulupirika. Ndidzaŵakonda kwambiri, pakuti ndaleka kuŵakwiyira.
5
Ndidzatsitsimutsa Israele ngati mame. Adzachita maluŵa ngati kakombo, adzazika mizu ngati mtengo wa ku Lebanoni.
6
Ziphukira zake zidzatambasukira kutali, adzakhala wokongola ngati mtengo wa olivi, adzakhala wonunkhira ngati mkungudza wa ku Lebanoni.
7
Aisraele adzapezanso chitetezo mwa Ine. Adzakolola tirigu wambiri, adzachuluka ngati mphesa. Adzakhala otchuka ngati vinyo wa ku Lebanoni.
8
Kodi Aefuremu adzachita nawonso chiyani mafano? Ndine amene ndimamva pemphero lao ndi kuŵasamala. Ndili ngati mkungudza wogudira nthaŵi zonse, ndine amene ndimaŵapatsa zipatso.”
9
Amene ali wanzeru amvetse zimenezi. Amene ali womvetsa, azisunge. Pakuti njira za Chauta nzolungama, ndipo olungama amayendamo, koma ochimwa amakhumudwamo.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14