bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hosea 6
Hosea 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 7 →
1
Anthu akunena kuti, “Tiyeni, tibwerere kwa Chauta. Watikadzula, komabe adzatichiritsa. Watikantha, komabe adzamanga mabala athu.
2
Posachedwa adzatitsitsimutsa. Patangopita masiku aŵiri kapena atatu, adzatiwukitsa kuti tikhale ndi moyo pamaso pake.
3
Tiyeni tilimbikire kusamala za Chauta. Adzabwera kwa ife mosapeneka konse ngati mbandakucha. Kubwera kwake kudzakhala madalitso ngati mvula, mvula yake yachilimwe imene imakhathamiza nthaka.”
4
Koma Chauta akuti, “Inu Aefuremu, kodi ndikuchiteni chiyani? Nanga inu Ayuda, ndikuchiteni chiyani? Chikondi chanu chimazimirira ngati nkhungu yam'maŵa, chili ngati mame okamuka msanga.
5
Nchifukwa chake ndakuŵazani ngati nkhuni ndi machenjezo a aneneri, ndakuphani ndi mau anga. Chigamulo changa nchoonekeratu ngati kuŵala kwa dzuŵa.
6
Kunena zoona Ine ndimafuna chikondi chosasinthika, osati nsembe chabe. Ndifuna kuti anthu andidziŵe Ine Mulungu m'malo mwa kumangopereka nsembe zopsereza.
7
“Koma anthuwo adaphwanya chipangano changa monga adachitira Adamu. Potero, adandichitira zosakhulupirika.
8
Giliyadi ndi mzinda wa anthu ochita zoipa, akungophana basi.
9
Monga mbala zimalalira munthu, momwemonso ansembe amasonkhana kuti azipha anthu pa njira ya ku Sekemu. Zoonadi amachita zachifwamba zambiri.
10
Pakati pa Aisraele ndaonapo zinthu zonyansa. Aefuremu adachita zadama, Aisraele adadziipitsa pakupembedza mafano.
11
“Inunso Ayuda mudzakolola chilango.
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14