bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hosea 4
Hosea 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 5 →
1
Inu Aisraele, imvani mau a Chauta, chifukwa Iye akukuimbani mlandu, inu anthu okhala m'dziko. Mlandu wake ndi wakuti, m'dziko mulibe kukhulupirika kapena kukoma mtima, ndipo Mulungu samulabadira.
2
Akulumbira monama, kunena zabodza, kupha, kuba ndi kuchita chigololo. Machimo achita kunyanya, ndipo akungophanaphana.
3
Nchifukwa chake mudzagwa chilala m'dziko, ndipo onse okhalamo adzavutika pamodzi ndi nyama zakuthengo zomwe, ndi mbalame zamumlengalenga. Ngakhale nsomba zam'nyanja zidzafa.
4
Chauta akuti, “Wina aliyense asatsutsepo kanthu, wina aliyense asaimbe mnzake mlandu, pakuti mlandu uli pakati pa Ine ndi inu ansembe onyenganu.
5
Mumakhumudwa usana ndi usiku, ndipo aneneri nawonso amachita chimodzimodzi, motero ndidzaononga Israele mai wanu.
6
Anthu anga akuwonongeka chifukwa Ine sandidziŵa. Ndidzakukanani kuti musanditumikire ngati ansembe, chifukwa choti mwakana kuphunzitsa za Ine. Mwaiŵala malamulo a Mulungu wanu, tsono Inenso Mulungu wanu ndidzaiŵala ana anu.
7
“Ansembe ankati akamachulukirachulukira, ndi m'menenso ankanyanyira kundichimwira. Ndidzasandutsa ulemu wao kuti ukhale manyazi.
8
Amalemererapo pa kuchimwa kwa anthu anga, ndipo amafunitsitsa kuti anthuwo azichimwirachimwira.
9
Tsono ansembewo ndidzaŵachita zomwe ndidzaŵachite anthu. Ndidzaŵalanga chifukwa cha makhalidwe ao oipa ndi kuŵalipsira pa ntchito zaozo.
10
Azidzadya koma sadzakhuta. Azidzachita zachiwerewere, koma sadzachulukana, poti adasiya Chauta, kuti adzipereke ku zachiwerewere.”
11
Chauta akuti, “Vinyo, kaya ndi wakale kaya ndi watsopano, amaononga nzeru.
12
Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo, ndipo amaombeza ndi ndodo yao. Mzimu wonyansa waasokeretsa, motero posiya Mulungu wao, akhala osakhulupirika.
13
Amapereka nsembe pa mapiri, amafukiza lubani pa zitunda, patsinde pa mitengo yogudira monga thundu, mnjale ndi mkundi, chifukwa amati mithunzi yake njabwino. “Nchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere, ndipo akamwana anu akuchita zigololo.
14
Koma sindidzaŵalanga ana anu aakazi chifukwa chochita zachiwerewere, sindidzaŵalanga akamwana anu chifukwa cha zigololo zao. Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere, ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi adama akuchipembedzo. Anthu opanda nzeru chitere adzaonongeka.
15
“Ngakhale Aisraele amachita zosakhulupirika, anthu a ku Yuda asapezeke ndi mlandu wotere. Asapite kukapembedza ku Giligala kapena ku Betehaveni. Asakalumbirenso kumeneko kuti, ‘Pali Chauta wamoyo!’
16
Aisraele ndi okanika ngati anaang'ombe. Kodi Chauta angathe kuŵadyetsa tsopano ngati anaankhosa pa busa lokoma?
17
“Anthu a ku Efuremu aphathana ndi mafano, izo nzao.
18
Amati akamwa kwambiri, amangochita zigololo. Amakonda zamanyazi kupambana ulemu wao.
19
Adzachotsedwa ngati chinthu chotengedwa ndi mphepo, ndipo adzachititsidwa manyazi chifukwa cha nsembe zao zachikunja.”
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14