bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hosea 7
Hosea 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 8 →
1
Ndikati ndibwezere anthu anga pabwino, ndikati ndichiritse Aisraele, uchimo wao umaonekera poyera. Ntchito zoipa za anthu a ku Samariyawo sizibisika ai. Sakhulupirika, amanyenga anthu, amathyola nyumba ngati mbala, ndi achifwamba, amalandanso zinthu za anthu poyera.
2
Koma saganiza kuti Ine sindiiŵala ntchito zao zoipa. Zolakwa zao zaŵazinga, ndipo sizichoka m'maso mwanga.”
3
Anthu amakopa mfumu ndi makhalidwe ao oipa, nduna zake amazinyenga ndi mabodza ao.
4
Onsewo ndi osakhulupirika, udani wao ndi wonyeka ngati moto wamuuvuni, umene mphikabuledi sasonkhezera kuyambira pamene akukanyanga mtanda wa buledi mpaka utafufuma.
5
Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu, nduna zake zimadakwa, mfumu nkuloŵa nawo m'gulu la anthu oipanganirana.
6
Mitima yao imatentha ngati uvuni ndi upo wao. Usiku wonse, ukali wao umanyeka, ndipo m'maŵa umayaka ngati moto.
7
Onsewo amakhala juu ngati uvuni, ndipo amapha olamulira ao. Imodziimodzi mafumu ao onse agwa, koma palibe ndi mmodzi yemwe wondiitana.
8
Chauta akuti, “Aefuremu ali ngati keke yopsa kumodzi, chifukwa amasakanizikana ndi anthu a mitundu ina.
9
Alendowo akuŵatha mphamvu, iwo osadziŵako. Akuyamba kumera imvi, iwo osadziŵako.
10
Aisraele kunyada kwao komwe kukuŵatsutsa. Koma pa zonsezi sakubwerera kwa Chauta Mulungu wao, sakumfunafuna konse.
11
“Aefuremu ali ngati nkhunda yopusa, yopanda nzeru. Amaitana Aejipito, namapita ku Asiriya kukapempha chithandizo.
12
Kulikonse kumene amapita, ndidzaŵatchera ukonde. Ndidzaŵagwetsa pansi ngati mbalame zamumlengalenga. Ndidzaŵalanga chifukwa cha zolakwa zao.
13
“Tsoka kwa iwo pakuti andisiya Ine. Aonongeke chifukwa chakuti andipandukira. Ndimafuna kuŵapulumutsa, koma amangolankhula zabodza za Ine.
14
Kulira kwao kwa Ine nkwabodza, amalira ali gone pa bedi. Amadzichekacheka ngati akunja chifukwa chofuna chakudya ndi chakumwa, komabe amandipandukira.
15
Ngakhale ndimaŵalera ndi kuŵalimbitsa, komabe amandichita zachiwembu.
16
Amatembenukira kwa mulungu wachabechabe, osati kwa Mulungu wopambanazonse. Ali ngati uta wokhota. Atsogoleri ao adzaphedwa ndi lupanga chifukwa chakuti amandilankhulira zachipongwe. Motero a ku Ejipito adzaŵaseka kwambiri.”
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14