bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hosea 11
Hosea 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 12 →
1
Chauta akuti, “Pamene Israele anali mwana, ndinkamukonda. Mwana wangayo ndidamuitana kuti atuluke ku Ejipito.
2
Ine ndikamakangaza kumuitana, iye ndiye kumandithaŵa kunka kutali. Ankaperekabe nsembe kwa Baala ndi kulitenthera lubani fanolo.
3
Komabe ndine amene ndidaphunzitsa Aefuremu kuyenda. Ndidaŵalera, koma sadavomereze kuti amene ndidaŵasamala ndine.
4
Ndidaŵakokera kwa Ine mwachifundo ndi mwachikondi. Ndidaŵanyamula nkuŵatsamiza kutsaya kwanga. Ndidaŵerama, nkuŵadyetsa.
5
“Tsono anthuwo adzabwereranso ku ukapolo ku Ejipito. Aasiriya adzakhala oŵalamulira, pakuti iwo akana kubwerera kwa Ine.
6
Nkhondo idzaononga mizinda yao. Adani adzaphwanya zipata za malinga ao ndi kuŵaononga, chifukwa chotsata nzeru zaokha.
7
Anthu anga akangamira zondipandukira Ine. Tsono adzalira chifukwa cha goli lachilango limene lili pa iwo, koma palibe amene adzaŵachotsere.
8
“Kodi ndingakusiye bwanji iwe Efuremu? Kodi ndingathe kukutaya bwanji iwe Israele? Kodi ndingathe bwanji kukusandutsa ngati Adima? Kodi ndingathe kukuwononga ngati Zeboimu? Mtima wanga wakana kutero, chifundo changa chikukula.
9
Sindidzalekerera kuti mkwiyo wanga ukulangitse, sindidzamuwononganso Efuremu, pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu. Ine, Woyera uja, ndili nawe, ndipo sindidzabwera kudzakuwononga.
10
“Ndidzaŵabangulira ngati mkango, ndipo anthu anga adzanditsata. Ndidzabanguladi, ndipo adzathamangira kwa Ine ali njenjenje kuchokera kuzambwe.
11
Adzabwera akunjenjemera ngati mbalame kuchokera ku Ejipito, adzabwera ngati njiŵa kuchokera ku Asiriya. Motero ndidzaŵabwezeranso kwao. Ndikutero Ine Chauta.”
12
Chauta akuti, “Anthu a ku Efuremu andizinga ndi mabodza. Banja limeneli la Israele nlonama kwambiri. Nawonso anthu a ku Yuda akundipandukirabe Ine Mulungu, Woyera ndi wokhulupirika.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14