bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hosea 13
Hosea 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 14 →
1
Kale Aefuremu ankati akalankhula, anthu ankachita mantha chifukwa ankalemekezeka m'dziko la Israele, koma adalakwa popembedza Baala, motero adzafa.
2
Masiku ano akuchimwirachimwira. Akudzipangira mafano oumba pogwiritsa ntchito siliva wao. Mafano onsewo ndi ntchito ya anthu aluso. Amati, “Perekani nsembe kwa ameneŵa, pembedzani anaang'ombeŵa poŵampsompsona.”
3
Nchifukwa chake adzazimirira ngati nkhungu yam'maŵa, kapena mame okamuka msanga. Adzamwazika ngati mungu wouluzika kuchokera pa malo opunthira tirigu, kapena ngati utsi wotuluka pa zenera.
4
Chauta akuti “Ine ndakhala Chauta Mulungu wako kuyambira nthaŵi imene ndidakutulutsa ku Ejipito. Sudziŵa Mulungu wina, koma Ine ndekha, Mpulumutsi wako ndine ndekha.
5
Ndine ndidakusamalani m'chipululu, m'dziko lotentha kwambiri.
6
Ndidaŵadyetsa, nakhuta, koma atakhuta, adanyada, ndipo adandiiŵala Ine.
7
Motero ndidzaŵalumphira ngati mkango, ndidzaŵalalira ngati kambuku m'mbali mwa njira.
8
Ndidzaŵambwandira ngati chimbalangondo cholandidwa ana. Ndidzathyola nthiti zao, ndipo ndidzaŵamwamwata pomwepo ngati mkango, ndidzaŵankhanthula ngati chilombo choopsa.
9
“Ndidzaononga inu Aisraele. Kodi ndani angakuthandizeni?
10
Inu munkati, ‘Tipatseni mfumu ndi atsogoleri.’ Nanga tsopano mfumu yanuyo, yoti ikulanditseni, ili kuti? Nanga atsogoleri anuwo, oti akutchinjirizeni, ali kuti?
11
Ndidakupatsani mafumu mwachipsera mtima. Kenaka atandikwiyitsa, ndidaŵachotsa.
12
“Kuipa kwa anthu a ku Efuremu kwalembedwa m'buku, buku lake la machimo ao ndalisunga.
13
Zoŵaŵa zonga za mkazi pobala mwana zidzaŵagwera. Akadapulumutsidwa, koma ali ngati mwana wopanda nzeru, wosafuna kutuluka pa nthaŵi yake yobadwa.
14
Kodi ngati ndidzaŵapulumutsa kwa akufa? Kodi ngati ndidzaŵaombola ku imfa? Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti? Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti? Anthu ameneŵa sindidzaŵachitiranso chifundo.
15
Ngakhale kuti Efuremu akondwe ngati bango, mphepo yakuvuma mphepo ya Chauta, idzakuntha kuchokera kuchipululu. Motero kasupe wake adzaphwa, ndipo chitsime chake chidzauma. Adani adzaononga chuma chake chamtengowapatali.
16
A ku Samariya adzalangidwa chifukwa choti adapandukira Mulungu wao. Adzaphedwa ndi lupanga, ana ao adzaphedwa moŵakankhanthitsa pansi. Akazi ake apathupi adzang'ambidwa.”
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14