bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hosea 12
Hosea 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 13 →
1
Efuremu chakudya chake ndi mpweya wokhawokha. Amanka nasaka mphepo yakuvuma tsiku lonse. Amachulukitsa mabodza ndi chiwawa. Amachita chipangano ndi dziko la Asiriya, ndipo amapereka mitulo ya mafuta ku Ejipito.”
2
Chauta akuŵaimba mlandu anthu a ku Yuda. Adzalanga a m'banja la Yakobe chifukwa cha makhalidwe ao, adzaŵabwezera zolingana ndi ntchito zao zoipa.
3
Akali m'mimba mwa mai wake, Yakobe adakangana ndi mbale wake, ndipo atakula adalimbana ndi Mulungu.
4
Yakobeyo adalimbana ndi mngelo ndipo adapambana. Adalira napempha madalitso. Mulungu adakumana naye ku Betele, ndipo kumeneko podzera mwa iyeyo adalankhula nafe.
5
Ameneyu ndiye Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse. Anthu azimkumbukira ndi dzina lakeli loti Chauta.
6
Motero bwererani nonsenu ndi chithandizo cha Mulungu wanu. Mukhale achikondi ndi olungama, ndipo muzidalira Mulungu wanu nthaŵi zonse.
7
Chauta akuti, “Aisraele ali ngati wamalonda wonyenga amene amagwiritsa ntchito masikelo onama. Amakonda kumeta anthu.
8
Aefuremu akunena kuti, ‘Ndithu talemera, takhuphuka zedi, wina sangatiloze chala pa kulemera kumeneku.’
9
Koma Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani ku Ejipito. Ndidzakukhalitsaninso m'mahema, monga munkachitira masiku amakedzana m'chipululu muja.
10
Ndidalankhula ndi aneneri. Ndine amene ndidaŵaonetsa zinthu zambiri ngati kutulo. Ndidalankhula m'mafanizo kudzera mwa iwo.
11
Komabe anthu ankapembedza mafano ku Giliyadi. Ndithu mafano ameneŵa adzaonongedwa. Ankapereka nsembe za nkhunzi ku Giligala, koma maguwa ansembewo ndidzaŵasandutsa miyulu ya miyala m'munda.”
12
(Yakobe adathaŵira ku dziko la Aramu. Israeleyo adagwira ntchito kumeneko kuti apeze mkazi. Ankaŵeta nkhosa kuti akwatire mkaziyo).
13
Chauta adatulutsa Aisraele ku Ejipito kudzera mwa mneneri. Ndipo mwa mneneriyo adaŵasungabe.
14
Koma Aefuremuwo adaputa mkwiyo wake, nchifukwa chake Chauta adzaŵalanga ndi imfa. Adzaŵalanga chifukwa adamchititsa manyazi kwambiri.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14