bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hosea 9
Hosea 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 10 →
1
Musakondwere Aisraele inu! Musakhale ndi chisangalalo chonga cha mitundu ina ya anthu. Mwasiya Mulungu wanu monga amachitira mkazi wosakhulupirika. Mwadzigulitsa kwa Baala ngati mkazi wadama, kuti mukalandireko zokolola zambiri.
2
Tirigu ndi mphesa simudzakhala nazo zokwanira. Mudzasoŵanso vinyo woti muzimwa.
3
Simudzakhalanso m'dziko la Chauta. Aefuremu inu, mudzabwerera ku ukapolo ku Ejipito, mudzadya chakudya choletsedwa ku dziko la Asiriya.
4
Kumeneko anthu sadzaperekanso zopereka za chakumwa kupereka kwa Chauta. Sadzamkondwetsanso ndi nsembe zao. Chakudya chao chidzakhala ngati chakudya chapamaliro, onse amene adzadya chakudya chimenecho adzaipitsidwa. Chakudyacho chidzangokhala chodyera njala chabe, osati choti nkukapereka ku Nyumba ya Chauta.
5
Kodi pa tsiku la chikondwerero, tsiku lolemekeza Chauta, anthuwo adzachitapo chiyani?
6
Nthaŵi ya chilango ikadzafika, iwo nkubalalika, Aejipito adzaŵakusa, nakaŵaika m'manda komweko ku Memfisi. Khwisa adzamera pa ziŵiya zao zasiliva. M'nyumba mwao mudzamera minga.
7
Nthaŵi ya chilango yafikadi, masiku olipsira aŵagwera. Pamenepo adzadziŵa kuti zimenezi nzoonadi. Tsopano akunena kuti, “Mneneriyu nchitsilu, munthu wa nzeru za kwa Mulunguyu ndi wamsala!” Amatero chifukwa zolakwa zao zachuluka, chidani chao nchachikulukulu.
8
Mneneri ndiye wochenjeza Aefuremu, anthu a Mulungu wanga. Koma mneneriyo amtchera msampha m'njira zake zonse, ndipo adani akumlalira m'Nyumba ya Mulungu.
9
Anthu aipiratu monga zidachitikira ku Gibea. Nchifukwa chake Mulungu sadzaiŵala kuipa kwao, ndipo adzalanga machimo ao.
10
Chauta akuti, “Israele ndidampeza ngati mphesa zam'thengo. Makolo ake aja ndidaŵakondwerera ngati nkhuyu zoyamba kupsa. Koma iwowo adapita kwa Baala-Peori, ndipo kumeneko adadzipereka kwa Baala. Motero adasanduka chinthu chonyansa ngati fano laolo, limene ankalikonda lija.
11
Ulemerero wa Aefuremu udzaŵathaŵa mouluka ngati mbalame. Sadzabalanso ana. Akazi ao sadzaima, sadzatenga pathupi.
12
Ngakhale abale ana, ndidzaŵaononga, sadzakhalapo ndi mmodzi yemwe. Tsoka kwa anthuwo ndikadzaŵasiya.”
13
Inu Chauta, monga ndikuwonera, ana a Efuremu adzakhala ngati nyama zojiwa. Aefuremu adzatsogolera ana ao kunkhondo kumene adzaphedwe.
14
Muŵapatse, Inu Chauta. Kodi mudzaŵapatse chiyani? Muŵapatse mimba yopita padera ndi maŵere ouma!
15
Chauta akuti, “Kuipa kwao konse kudaoneka makamaka ku Giligala. Ndidayamba kudana nawo kumeneko. Ndidzaŵapirikitsa m'dziko mwanga, chifukwa makhalidwe ao ndi oipa. Sindidzaŵakondanso, atsogoleri ao onse andiwukira.
16
Efuremu ali ngati mtengo wodulidwa umene mizu yake yauma, ndipo sudzabalanso zipatso. Ngakhale anthuwo abale ana, ndidzaŵapha ana ao okondedwawo.”
17
Mulungu wanga adzaŵataya anthu amenewo chifukwa choti sadamumvere. Adzasanduka oyendayenda pakati pa mitundu ya pa dziko lapansi.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14