bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hosea 2
Hosea 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 3 →
1
Nchifukwa chake abale ako uŵauze kuti, “Ndinu anthu a Chauta”, ndiponso kuti, “Chauta wakukondani”.
2
“Mudzudzule mai wanu, mumdzudzule pakuti salinso mkazi wanga, ndipo ine sindinenso mwamuna wake. Mumdzudzule kuti aleke kuchita chigololo, zibwenzi zake azichotse pachifuwa pake.
3
Akapanda kutero ndimuvula, kuti akhale monga momwe adabadwira. Ndidzamuumitsa ngati chipululu, adzakhala ngati dziko lopanda madzi, ndidzamphetsa ndi ludzu.
4
Ana ake onse sindidzaŵachitira chifundo chifukwa ndi ana am'chiwerewere.
5
Paja mai wao ndi wachiwerewere. Amene adaŵabala ankachita zomvetsa manyazi. Ankati, ‘Nditsatira zibwenzi zanga zimene zimandipatsa chakudya ndi madzi, ubweya ndi thonje, mafuta ndi vinyo.’
6
“Nchifukwa chake njira yake ndidzaitseka ndi minga. Ndidzamuzinga ndi khoma, kuti asayendenso m'njira zake zakale.
7
Adzathamangira zibwenzi zake, koma sadzapezana nazo. Adzazifunafuna, koma osazipeza. Tsono adzati, ‘Ndibwereranso kwa mwamuna wanga uja, chifukwa ndidaali pabwino ndi iyeyo kupambana tsopano.’
8
Sankadziŵa kuti ndine amene ndinkamupatsa tirigu, vinyo ndi mafuta. Sankadziŵa kuti ndine amene ndinkamupatsa siliva ndi golide wambiri zimene anthuwo ankapangira mafano a Baala.
9
Nchifukwa chake ndidzamlanda tirigu wanga pa nthaŵi yodula ndi vinyo wanga pa nthaŵi yofinya. Ndidzamlandanso ubweya ndi thonje langa zimene ankavalira.
10
Motero ndidzaonetsa dama lake poyera kwa zibwenzi zake, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzampulumutse m'manja mwanga.
11
Ndidzathetsa chimwemwe chake chonse, zikondwerero zake za pokhala mwezi, za masabata ndi za masiku ena onse opatulika.
12
Ndidzaononga mitengo yake yamphesa ndi yankhuyu imene ankanena kuti, ‘Ameneŵa ndiwo malipiro anga amene zibwenzi zanga zidandipatsa.’ Ndidzaisandutsa malunje, ndipo zilombo zizidzadya kumeneko.
13
Ndidzamlanga chifukwa choti adafukiza lubani kwa Abaala pa zikondwerero zao. Ankadzikongoletsa povala mphete ndi mikanda yamtengowapatali, kuti azithamangira zibwenzi zake, Ine nkumandiiŵala. Ndatero Ine Chauta.”
14
“Tsono tamverani, ndidzamkopa mkaziyo, ndidzapita naye ku chipululu ndi kukamsangalatsa ndi mau achikondi.
15
Kumeneko ndidzambwezera minda yake yamphesa. Ndidzasandutsa Chigwa cha Mavuto kuti chikhale chipata cha kuchiyembekezo. Ndipo kumeneko azidzandiyankha monga m'mene ankandiyankhira pa ubwana wake, atatuluka ku Ejipito.
16
Nthaŵi imeneyo pondiitana uzidzati, ‘Amuna anga.’ Suzidzatinso, ‘Baala wanga.’ Ndikutero Ine Chauta.
17
Ndidzamletsa kuti asatchulenso maina a Abaala, Ndithu anthu sadzatchulanso maina aowo popembedza.
18
Nthaŵi imeneyo ndidzachita chipangano ndi nyama zakuthengo, mbalame zamumlengalenga, ndi zokwaŵa pansi, kuti ziyanjane ndi anthu anga. Tsono ndidzathyola uta, lupanga, ndi zida zina zonse zankhondo, ndipo ndidzazichotsa m'dzikomo, kuti iwo apeze moyo wamtendere.
19
Iwe Israele, ndidzakutomera kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya. Ndidzakutomera mwaungwiro, mwachilungamo, mwa chikondi chosasinthika, ndiponso mwachifundo.
20
Ndidzakutomera mokhulupirika, ndipo udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
21
Chauta akunena kuti, “Nthaŵi imeneyo ndidzamvera mlengalenga, mvula idzagwa pa dziko lapansi.
22
Nthaka idzamvera tirigu, vinyo ndi mafuta, ndipo zimenezi zidzamvera Yezireele.
23
Israele ndidzamubzala m'dziko kuti akhale wanga. Ndidzaonetsa chikondi kwa ‘Sakondedwa’ uja. Anthu amene ndinkaŵatchula ‘Si-anthu-anga,’ ndidzaŵauza kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ Ndipo iwo adzanena kuti, ‘Ndinu Mulungu wathu.’ ”
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14