bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hosea 8
Hosea 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 9 →
1
Chauta akuti, “Lizani lipenga! Adani akugudukira dziko la Chauta ngati adembo pamwamba pa nyama. Anthu anga aphwanya chipangano changa, ndipo achimwira malamulo anga.
2
Amalirira kwa Ine kuti ndiŵathandize, amati, ‘Ife Aisraele tikukudziŵani Inu Mulungu wathu.’
3
Koma Aisraele akana zabwino. Nchifukwa chake adani ao adzaŵapirikitsa.
4
“Amadzilongera mafumu mosatsata kufuna kwanga. Amadziikira atsogoleri popanda chilolezo changa. Adzipangira mafano asiliva ndi agolide, koma adziwononga nawo.
5
Fano la mwanawang'ombe limene a ku Samariya akupembedza likundinyansa. Motero mkwiyo wanga waŵayakira kwambiri anthuwo. Padzapita nthaŵi yaitali chotani asanasinthe kuti ayere anthu a ku Israele?
6
“Fanolo si mulungu konse, adalipanga ndi munthu waluso. Fano la ku Samariyali lidzatswanyidwa pafupipafupi.
7
“Aisraele amafesa kamphepo, ndipo amakolola kamvulumvulu. Tirigu alibe ngala, sadzabala chakudya. Akadabala, alendo akadadya chakudyacho.
8
Aisraele amezedwa. Asanduka ngati chiŵiya chachabe pakati pa anthu a mitundu ina.
9
Adathaŵira ku Asiriya ngati mbidzi yongodziyendera payokha. Aefuremu adalipira anthu a ku maiko ena kuti akhale oŵathandiza.
10
Chifukwa choti adagwirizana ndi anthu a mitundu ina, ndidzaŵasonkhanitsa ndi kuŵaononga. Posachedwa adzazunzika kwambiri chifukwa cha ulamuliro wa mfumu ya ku Asiriya.
11
“Aefuremu adachulukitsa maguwa ansembe ochotserapo machimo, koma maguwawo asanduka malo ochimwirapo.
12
Ndidaŵapatsa malamulo ambiri olembedwa, koma saŵasamala. Amaŵayesa achilendo.
13
Amapereka nsembe zanyama kwa Ine nkumadya, koma Ine Chauta sindikondwera nazo konse. Sindidzaiŵala zolakwa zao, ndidzaŵalanga chifukwa cha zimenezo. Ndidzaŵabwezera ku ukapolo ku Ejipito.
14
Aisraele adzimangira nyumba zikuluzikulu, kuiŵala Mlengi wao. Ayuda achulukitsa mizinda yamalinga. Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yaoyo, ndipo motowo udzatentha nyumba zao zazikuluzo.”
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14