bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hosea 10
Hosea 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 11 →
1
Aisraele ali ngati mpesa wokondwa umene unkabala zipatso zambiri. Chuma chao chikamanka chichuluka, chipembedzo chachikunja chinkakulirakuliranso. Dziko lao likamanka litukuka, iwo ankakometserakometsera mafano ao amene ankaŵapembedza.
2
Mtima wao ndi wonyenga. Tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha machimo ao. Chauta adzagumula maguwa ao ansembe, ndipo adzaononga miyala yao yoimiritsa yachipembedzo.
3
Posachedwa anthuwo adzanena kuti, “Tilibe mfumu tsopano chifukwa sitidamvere Chauta. Komabe mfumuyo ikadatichitira chiyani ife?”
4
Mafumu akungolankhula mau opandapake. Amangochita zipangano ndi malonjezo abodza. Chilungamo chasanduka kusalungama kumene kumaphuka ngati udzu woipa m'munda.
5
Anthu a ku Samariya adzachita mantha, fano la mwanawang'ombe la ku Betehaveni likadzaonongedwa. Anthu ake adzalirira. Nawonso ansembe ake aja adzalira maliro a mulungu waoyo, chifukwa ulemerero wake wonse wachokeratu.
6
Zoonadi, fanolo lidzatengedwa kupita ku Asiriya, kuti likakhale mphatso yoperekedwa kwa mfumu yaikulu. Aefuremu adzachita manyazi, Aisraelewo adzachita manyazi chifukwa cha malangizo onama amene ankamvera.
7
Mfumu ya ku Samariya idzatengedwa kunka kutali ngati kanthambi koyenda pa madzi.
8
Akachisi opembedzerako milungu yabodza amene Aisraele ankachimwirako, idzaonongedwa. Minga ndi mitungwi zidzamera pa maguwawo. Anthu adzauza mapiri kuti, “Tigwereni!” Adzauza magomo kuti, “Tipsinjeni!”
9
Chauta akuti, “Kuyambira uchimo wa ku Gibea, Aisraele akhala akuchimwabe. Motero adzagonjetsedwa pa nkhondo ku Gibea komweko.
10
Ndidzabwera kudzalimbana ndi anthu aupanduŵa kuti ndiŵalange. Anthu a mitundu ina adzasonkhana kuti aŵathire nkhondo chifukwa cha uchimo wao waukulu.
11
Kale Efuremu anali ngati ng'ombe yophunzitsidwa imene inkakonda kupuntha tirigu. Tsopano m'khosi lake lokongola ndaikamo goli, kuti agwire ntchito koposa. Ndifuna kuti Yuda azitipula, Yakobe azimwanya mauma.
12
Mudzifesere m'chilungamo, ndipo mudzakolola madalitso a chikondi changa chosasinthika. Tipulani tsala lanu pakuti nthaŵi yofunafuna Chauta yakwana. Funafunani Chautayo mpaka atabwera kudzakugwetserani mvula ya madalitso.
13
Mudabzala zolakwa, ndipo mudakolola chilango chake. Mwadya zotsatira zake za mabodza. Chifukwa choti mwadalira magaleta anu, ndi kuchuluka kwa anthu anu a nkhondo,
14
adani anu adzakuthirani nkhondo. Malinga anu onse adzaonongedwa monga momwe Salamani adaonongera Betaribele pa tsiku la nkhondo. Adaphwanya azimai pamodzi ndi ana omwe.
15
Momwemo zidzakuchitikirani inu a ku Betele chifukwa cha uchimo wanu waukulu. Nkhondo ikadzangoyamba m'mamaŵa, nayonso mfumu ya ku Israele idzaphedwa.”
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14