bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hosea 5
Hosea 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 6 →
1
“Ansembe inu, imvani izi! Aisraele inu, mumvetsere nonse. Inu a m'banja la mfumu, mvetserani mau anga. Chilango chidzakugwerani, chifukwa inu munali msampha ku Mizipa, mudachita ngati kuyala ukonde ku phiri la Tabori.
2
Opandukawo azama kwambiri m'machimo ao, Ine ndidzaŵalanga onsewo.
3
“Aefuremu ndikuŵadziŵa, Aisraele ndi osabisika kwa Ine. Aefuremu akhala osakhulupirika, Aisraele adziipitsa.”
4
Ntchito zao zoipa zatseka njira yao yobwerera kwa Mulungu wao, pakuti mtima wa kusakhulupirika uli mwa iwo, ndipo salabadako za Chauta.
5
Kudzikuza kwa Israele kwasanduka umboni womutsutsa. Zoonadi Efuremu adzagwa ndi machimo ake. Nayenso Yuda adzateronso.
6
Anthu amapereka nsembe zankhosa ndi zang'ombe pofunafuna Chauta, koma samupeza, waŵachokera.
7
Adachita zosakhulupirika kwa Chauta, motero ana ao nawonso si ake a Mulungu. Tsono chipembedzo chao chachikunja chidzaŵaonongetsa pamodzi ndi minda yao.
8
Imbani malipenga ankhondo ku Gibea! Lizani mbetete ku Rama! Chenjezani a ku Betehaveni! Inu a ku Benjamini tsogolani!
9
Efuremu adzasanduka bwinja pa tsiku lachilango. Ndikulengeza zoona kwa inu nonse Aisraele.
10
Chauta akuti, “Atsogoleri a ku Yuda amachita nkhondo kuti afutuze malire. Nchifukwa chake ndidzaŵamiza ndi mkwiyo wanga ngati madzi achigumula.
11
Aefuremu akuŵapondereza, akuŵalanga chifukwa chomvera za ena.
12
Nchifukwa chake ndidzaononga Efuremu, monga momwe njenjete zimaonongera nsalu, ndidzakhala ngati chilonda choola pa anthu a ku Yuda.
13
“Tsono anthu a ku Efuremu ataona kuti akudwala, ndipo Ayuda ataona kuti ali ndi mabala, Aefuremuwo adapita kwa Aasiriya, Ayuda natuma uthenga kwa mfumu yaikulu, kuti iŵathandize. Koma siingathe kuŵachiritsa kapena kupoletsa mabala ao.
14
Ndidzalumphira Aefuremu ngati mkango, ndidzambwandira Ayuda ngati msona wa mkango. Ine mwini ndidzaŵakadzula nkuchokapo. Pamene ndizidzaŵaguza, palibe wina aliyense wotha kudzaŵalanditsa.
15
“Ndidzabwerera ku malo anga, mpaka anthu anga atasaukiratu, ndi kuyamba kundifunafuna. M'mavuto ao adzayesetsa kundipeza.”
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14