bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Mark 1
Mark 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 2 →
1
Uwu ndi Uthenga Wabwino wonena za Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu.
2
Udayamba monga mneneri Yesaya adalembera m'buku mwake kuti, “Mulungu akuti, “Ndidzatuma wamthenga wanga m'tsogolo mwako kuti akakonzeretu njira yoti iwe udzapitemo.
3
Liwu la munthu wofuula m'chipululu: akunena kuti, ‘Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo.’ ”
4
Zimenezi zidachitikadi pamene Yohane Mbatizi adaafika ku chipululu, nayamba kulalika. Ankauza anthu kuti, “Tembenukani mtima, mubatizidwe, ndipo Mulungu adzakukhululukirani machimo anu.”
5
Anthu ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi a ku Yerusalemu ankadza kwa iye. Tsono ankati iwo akaulula machimo ao, iye nkumaŵabatiza mu Mtsinje wa Yordani.
6
Yohaneyo ankavala zovala za ubweya wa ngamira, ndipo ankamangira lamba wachikopa m'chiwuno. Chakudya chake chidaali dzombe ndi uchi wam'thengo.
7
Kulalika kwake ankati, “Pambuyo panga pakubwera wina wamphamvu kuposa ine, mwakuti ineyo ndine wosayenera ngakhale kuŵerama nkumasula zingwe za nsapato zake.
8
Ine ndakubatizani ndi madzi, koma Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera.”
9
Pa masiku amenewo Yesu adafika kuchokera ku Nazarete, mudzi wa ku Galileya, ndipo Yohane adambatiza mu mtsinje wa Yordani.
10
Potuluka m'madzimo, adangoona kuthambo kukutsekuka, ndipo Mzimu Woyera akutsika pa Iye ngati nkhunda.
11
Tsono kudamveka mau ochokera kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.”
12
Nthaŵi yomweyo Mzimu Woyera adapititsa Yesu ku chipululu.
13
Yesuyo adakhala kumeneko masiku makumi anai, Satana akumuyesa. Komweko kunalinso nyama zakuthengo, ndipo angelo ankamutumikira.
14
Yohane uja ataponyedwa m'ndende, Yesu adapita ku Galileya akulalika Uthenga Wabwino wonena za Mulungu.
15
Ankati, “Nthaŵi yakwana, Ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwinowu.”
16
Pamene Yesu ankayenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, adaona anthu aŵiri, Simoni ndi mbale wake Andrea, akuponya khoka m'nyanjamo, popeza kuti anali asodzi.
17
Yesu adaŵauza kuti, “Inu, munditsate, ndikakusandutseni asodzi a anthu.”
18
Pomwepo iwo adasiya makoka ao, namamtsatadi.
19
Atapitirira pang'ono, Yesu adaona Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo. Iwowo anali m'chombo, akukonza makoka ao,
20
nthaŵi yomweyo Iye nkuŵaitana. Pamenepo iwowo adasiya bambo wao Zebedeo m'chombomo pamodzi ndi antchito ake, namatsata Yesu.
21
Onsewo adapita ku Kapernao. Tsono litafika tsiku la Sabata, Yesu adaloŵa m'nyumba yamapemphero, nayamba kuphunzitsa.
22
Zophunzitsa zake anthu zidaaŵagwira mtima kwambiri, chifukwa ankaphunzitsa moonetsa ulamuliro, kusiyana ndi m'mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo.
23
M'nyumba yamapempheroyo mudaaloŵa munthu wogwidwa ndi mzimu womuipitsa. Adalankhula mokuŵa kuti,
24
“Kodi takuputani chiyani, Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadzatiwononga? Ndakudziŵani, ndinu Woyera uja wa Mulungu.”
25
Koma Yesu adazazira mzimu woipawo, adati, “Khala chete, tuluka mwa munthuyu.”
26
Apo mzimu womuipitsa uja udamugwedeza kwamphamvu munthuyo, ndipo udakuwa koopsa, nkutuluka.
27
Anthu onse aja adazizwa kwambiri, mpaka kumafunsana kuti, “Kodi zimenezi nzotani? Zophunzitsa zamtundutu zimenezi! Ngakhale mizimu yoipitsa anthu yomwe akuilamula ndi mphamvu, ndipo ikumumveradi.”
28
Mwamsanga mbiri yake idawanda ponseponse ku dera lonse la ku Galileya.
29
Pambuyo pake Yesu adachoka ku nyumba yamapemphero kuja, nakaloŵa pamodzi ndi Yakobe ndi Yohane m'nyumba ya Simoni ndi Andrea.
30
Apongozi a Simoni anali gone, akudwala malungo, ndipo nthaŵi yomweyo anthu adamufotokozera za matendawo.
31
Yesu adapita nakaŵagwira pa dzanja amaiwo nkuŵadzutsa, ndipo malungowo adatha. Pomwepo amai aja adayamba kukonzera anthu chakudya.
32
Madzulo amenewo, dzuŵa litaloŵa, anthu adabwera kwa Yesu ndi anzao onse ovutika, ndi ogwidwa ndi mizimu yoipa.
33
Anthu a m'mudzi monsemo adaasonkhana pakhomopo.
34
Yesu adachiritsa ambiri amene ankavutika ndi matenda osiyanasiyana, ndipo adatulutsa mizimu yoipa yambiri. Koma mizimuyo ankailetsa kuti isalankhule, chifukwa idaamzindikira.
35
M'mamaŵa ndithu, kusanache, Yesu adadzuka napita kumalo kosapitapita anthu. Kumeneko adakapemphera.
36
Simoni ndi anzake aja adamlondola komweko.
37
Atampeza adamuuza kuti, “Anthu onse akukufunafunani.”
38
Koma Iye adaŵauza kuti, “Tiyeni tinke ku midzi ina kufupi konkuno, ndikalalike mau kumenekonso, pakuti ndizo ndidadzera.”
39
Tsono adapita nalalika m'nyumba zamapemphero ku Galileya konseko, ndipo ankatulutsa mizimu yoipa.
40
Munthu wina wakhate adadza kwa Yesu. Adamugwadira nayamba kumdandaulira. Adati, “Mutafuna, mungathe kundichiritsa.”
41
Yesu adamumvera chifundo. Adatambalitsa dzanja nkumukhudza nati, “Chabwino, ndikufuna, chira!”
42
Pomwepo khate lake lija lidatha, ndipo adachiradi.
43
Tsono Yesu adamlamula kuti apite, namuuza mau amphamvu.
44
Adati, “Chenjera, usakambire wina aliyense zimenezi. Ingopita, ukadziwonetse kwa wansembe, ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose ija. Imeneyo ikhale yotsimikizira anthu onse kuti wachiradi.”
45
Koma munthuyo atachoka pamenepo, adayamba kumaulula zonse, ndi kufalitsa nkhani imeneyi, kotero kuti Yesu sadathenso kuwonekera poyera m'mudzi uliwonse. Nchifukwa chake ankakhala kwina, kumalo kosapitapita anthu, koma anthu ankabwerabe kwa Iye kuchokera uku ndi uku.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16