bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Mark 4
Mark 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 5 →
1
Yesu adayambanso kuphunzitsa pambali pa Nyanja ya Galileya. Anthu ochuluka adasonkhana kumeneko, kotero kuti Iye adaayenera kuloŵa m'chombo, nakhala pansi m'menemo panyanjapo. Anthu onse adaakhala pansi pa mtunda m'mphepete mwa nyanjayo,
2
ndipo Yesu adayamba kuŵaphunzitsa zambiri m'mafanizo. Poŵaphunzitsa adati,
3
“Mvetsetsani! Munthu wina adapita kukafesa mbeu.
4
Akufesa choncho, mbeu zina zidagwera m'njira, ndipo mbalame zidabwera nkuzitolatola.
5
Mbeu zina zidagwera pa nthaka yamiyala, pamene panalibe dothi lambiri. Zidamera msanga, chifukwa nthakayo inali yosazama.
6
Koma pamene dzuŵa lidakwera, zidapserera kenaka zidauma, chifukwa zinali zosazika mizu.
7
Mbeu zina zidagwera pa zitsamba zaminga. Zitsambazo pokula zidalanda chakudya cha mbeu zija, kotero kuti mbeuzo sizidabereke konse.
8
Koma mbeu zina zidagwera pa nthaka yabwino. Zidamera bwino nkukula, ndipo zidabereka. Ngala zina zinali ndi njere makumi atatu, zina makumi asanu ndi limodzi, zina makumi khumi.”
9
Tsono Yesu adati, “Yemwe ali ndi makutu akumva, amve!”
10
Pamene Yesu anali payekha, ophunzira khumi ndi aŵiri aja pamodzi ndi enanso amene ankakhala naye adadzamufunsa za mafanizowo.
11
Iye adaŵayankha kuti, “Inuyo Mulungu adakuululirani zobisika zokhudza Ufumu wake. Koma enaŵa amene ali kunja, zonse amazimvera m'mafanizo chabe,
12
kuti choncho, monga mau a Mulungu aja amanena, “ ‘Kuyang'ana ayang'ane ndithu, koma asapenye kanthu, ndipo kumva amve ndithu, koma asamvetse kanthu, kuti angatembenuke mtima, ndipo Mulungu angaŵakhululukire.’ ”
13
Pambuyo pake Yesu adaŵafunsa kuti, “Monga simukulimvetsadi fanizo limeneli? Nanga mudzamvetsa bwanji fanizo lina lililonse?
14
Wofesa mbeu uja ndi amene amafesa mau a Mulungu.
15
Mbeu zogwera m'njira zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu. Koma nthaŵi yomweyo Satana amabwera, nkuchotsa mau aja amene adafesedwa m'mitima mwao.
16
Mbeu zofesedwa pa nthaka yamiyala zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, nthaŵi yomweyo nkuŵalandira ndi chimwemwe.
17
Tsono popeza kuti mauwo sadazike mizu yozama, anthuwo amangolimbika kanthaŵi pang'ono chabe. Mwakuti pakangofika mavuto kapena masautso chifukwa cha mau aja, nthaŵi yomweyo anthuwo amabwerera m'mbuyo.
18
Mbeu zofesedwa pa zitsamba za minga zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu.
19
Koma kutanganidwa ndi zapansipano, kukondetsa chuma ndi kukhumba zinthu zina zambiri kumaloŵapo nkufooketsa mau aja, motero sabereka konse zipatso.
20
Koma mbeu zofesedwa pa nthaka yabwino zija zikutanthauza anthu amene amamva mau a Mulungu, naŵalandira. Anthu otere amabereka zipatso, mwina makumi atatu, mwina makumi asanu ndi limodzi, mwina makumi khumi.”
21
Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi anthu amatenga nyale nkuivundikira ndi mbiya, kapena kuibisa kunsi kwa bedi? Suja amaiika pa malo oonekera?
22
Pajatu chinthu chilichonse chobisika chidzaululuka, ndipo chilichonse chachinsinsi chidzaonekera poyera.
23
Yemwe ali ndi makutu akumva, amve!”
24
Adaŵauzanso kuti, “Muzisamala pa mau amene mumamva. Muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu, ndipo inuyo adzakubzoletserani.
25
Paja amene ali ndi kanthu kale, adzamuwonjezera zina. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.”
26
Yesu adaŵauzanso kuti, “Za Ufumu wa Mulungu tingazifanizire motere: munthu afesa mbeu m'munda.
27
Iyeyo atha kumangogona usiku, m'maŵa nadzuka, nthaŵi yonseyo mbeu adafesa zija zikumera ndi kukula, mwiniwakeyo osadziŵa m'mene zonsezi zikuchitikira.
28
Paja nthaka imabereketsa mbeuzo yokhayokha. Umayamba ndi mmera, kenaka ngala, pambuyo pake njere m'ngala muja zimakhwima.
29
Tsono mbeuzo zikacha, munthu uja amatenga mpeni wodulira, pakuti nyengo yokolola yafika.”
30
Yesu adatinso, “Kodi Ufumu wa Mulungu tingauyerekeze ndi chiyani? Kaya tiwufanizire ndi chiyani?
31
Uli ngati njere ya mbeu ya mpiru. Pamene aifesa m'nthaka, ndi yaing'ono kwambiri mukaiyerekeza ndi njere zina pansi pano.
32
Koma akaifesa, imamera, mbeu yake nkukula ndithu kupambana zitsamba zina zonse. Imachita nthambi zazikulu, kotero kuti mbalame zimatha kudzamanga zisa mumthunzi mwake.”
33
Yesu ankaphunzitsa anthu ndi mafanizo ambiri onga ameneŵa, polinganiza ndi nzeru za anthuwo.
34
Sankaŵaphunzitsa popanda mafanizo. Koma ankati akakhala payekha ndi ophunzira ake, ankaŵatanthauzira zonse.
35
Tsiku lomwelo, dzuŵa litaloŵa, Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwoloke, tipite ku tsidya.”
36
Tsono iwo adasiya khamu la anthu lija, natenga Yesu m'chombo momwe adaalimo. Padaalinso zombo zina zotsagana naye.
37
Tsono padauka namondwe woopsa. Mafunde ankaloŵa m'chombomo, kotero kuti chidaayamba kudzaza ndi madzi.
38
Koma nthaŵi imeneyo Yesu anali kumbuyo m'chombomo, ali m'tulo atatsamira mtsamiro. Pamenepo ophunzira aja adamudzutsa, adati, “Aphunzitsi, kodi simukusamalako kuti tikumira?”
39
Yesu adadzuka, ndipo adadzudzula mphepoyo, nalamula nyanja kuti, “Tonthola! Khala bata!” Mphepo ija idalekadi, kenaka padagwa bata lalikulu.
40
Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuchita mantha? Kani mulibe chikhulupiriro inu?”
41
Koma iwo adaagwidwa ndi mantha kwambiri, nkumafunsana kuti, “Kodi Iyeyu ndi munthu wotani kuti ngakhale mphepo ndi nyanja zizimumvera?”
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16