bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Mark 13
Mark 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 14 →
1
Pamene Yesu ankachoka ku Nyumba ya Mulungu, wophunzira wake wina adamuuza kuti, “Aphunzitsi, taonani kukongola kwake miyalayi ndi nyumbazi.”
2
Yesu adamuuza kuti, “Kodi mukuziwona nyumba zikuluzikuluzi? Sipadzatsala konse mwala ndi umodzi womwe pamwamba pa mwala unzake: yonse adzaigumula.”
3
Pambuyo pake Yesu adakhala pansi, pa Phiri la Olivi, kuyang'anana ndi Nyumba ya Mulungu. Tsono Petro, Yakobe, Yohane ndi Andrea adamufunsa paokha, kuti,
4
“Tatiuzani bwino, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti zonsezi zili pafupi kuchitika?”
5
Yesu adayamba kuŵauza kuti, “Chenjerani kuti wina aliyense asadzakusokezeni.
6
Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine,’ ndipo adzasokeza anthu ambiri.
7
Koma inu mukadzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno, kapena mphekesera za nkhondo zakutali, musadzade nkhaŵa ai. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai.
8
Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana, ndipo kudzakhala njala. Tsono zonsezitu nkuyamba chabe kwa mavuto.
9
“Koma inu muchenjere. Anthu adzakuperekani ku mabwalo amilandu a Ayuda, ndipo adzakukwapulani m'nyumba zao zamapemphero. Mudzaonekera kwa akulu a Boma ndi kwa mafumu chifukwa cha Ine, kuti mukandichitire umboni pamaso pao.
10
Nkofunika kuti Uthenga Wabwino uyambe walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.
11
Tsono akadzakugwirani ndi kukuperekani ku mlandu, musadzaderetu nkhaŵa nkumaganiza kuti, ‘Kodi tikanene chiyani?’ Ai, inu mukangonena zimene Mulungu akakuuzeni pa nthaŵi imeneyo. Pajatu odzalankhula sindinu ai, koma Mzimu Woyera.
12
Mbale azidzapereka mbale wake kuti aphedwe, bambo azidzapereka mwana wake. Ana azidzaukira makolo ao, mpaka kuŵaphetsa.
13
Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha Ine. Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.”
14
“Chosakaza chonyansa chija chidzakhala atachiimika pamalo pomwe sichiyenera kukhalapo. (Umvetse bwino amene ukuŵerengawe.) Mukadzaona zimenezi, pamenepo amene ali m'Yudeya adzathaŵire ku mapiri.
15
Amene ali padenga pa nyumba yake, asati atsike kuti akatenge chinthu m'nyumba mwakemo.
16
Yemwe ali ku munda, asabwererenso ku nyumba kuti akatenge mwinjiro.
17
Ali ndi tsoka akazi amene adzakhale ndi pathupi, ndiponso azimai oyamwitsa ana masiku amenewo.
18
Pempherani kuti zimenezi zisadzaoneke pa nyengo yachisanu,
19
chifukwa masautso amene adzaoneke masiku amenewo, sanaonekepo chilengedwere dziko lapansi mpaka pano, ndipo sadzaonekanso.
20
Tsonotu masiku amenewo, Ambuye akadapanda kuŵachepetsa, sakadapulumukapo munthu ndi mmodzi yemwe. Koma masikuwo Mulungu adaŵachepetsa chifukwa cha anthu omwe Iye adaŵasankha.
21
“Pa nthaŵi imeneyo, wina akadzakuuzani kuti, ‘Ali panotu Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Uyo ali apoyo,’ musadzakhulupirire.
22
Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti, ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.
23
Koma inu chenjerani. Ine ndiye ndakuuziranitu zonse.”
24
“Masiku amenewo, mavutowo atatha, dzuŵa lidzada, mwezi udzaleka kuŵala.
25
Nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo, ndipo mphamvu zamumlengalenga zidzagwedezeka.
26
Pamenepo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo, ali ndi mphamvu zazikulu ndi ulemerero.
27
Tsono Iye adzatuma angelo ake kuti akasonkhanitse osankhidwa ake kuchokera ku mbali zonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.”
28
“Phunziriraniko kwa mkuyu. Mukamaona kuti nthambi zake zayamba kukhala zanthete ndipo masamba akuphuka, mumadziŵa kuti chilimwe chayandikira.
29
Momwemonso mukadzaona zija ndanenazi zikuchitika, mudzadziŵe kuti Mwana wa Munthu ali pafupi, ali pakhomo penipeni.
30
Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse.
31
Thambo ndi dziko lapansi zidzatha, koma mau anga sadzatha mphamvu konse.”
32
“Koma za tsiku lake kapena nthaŵi yake, palibe amene amadziŵa. Angelo omwe akumwamba sadziŵa. Ngakhale Ineyo Mwanane sindidziŵa, amadziŵa ndi Atate okha basi.
33
Tsono chenjerani, khalani maso, chifukwa simudziŵa kuti nthaŵiyo idzakwana liti.
34
Ndi monga ngati bwana amene akunyamuka ulendo kuchoka kunyumba kwake. Amasiya zinthu m'manja mwa antchito ake, aliyense ntchito yake, ndipo amauza wapakhomo kuti azikhala maso.
35
Nanunso tsono khalani maso, chifukwa simudziŵa mwini nyumba adzabwerera nthaŵi yanji: kaya ndi madzulo, kaya ndi pakati pa usiku, kaya ndi tambala woyamba, kapena mbandakucha.
36
Atha kudzabwera mwadzidzidzi, tsono asadzakupezeni muli m'tulo.
37
Zimene ndikunenazi, sindikuuza inu nokha ai, koma ndikuuza anthu onse kuti, ‘Khalani maso.’ ”
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16