bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Mark 14
Mark 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 15 →
1
Kudangotsala masiku aŵiri kuti chifike chikondwerero cha Paska ndi chikondwerero cha masiku odya buledi wosafufumitsa. Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti amgwirire Yesu mochenjera, nkumupha.
2
Koma ankati, “Zimenezi tisadzachite pa nthaŵi ya chikondwerero ai, pangadzachitike chipolowe pakati pa anthu.”
3
Tsiku lina Yesu anali ku Betaniya, m'nyumba ya Simoni wotchedwa Wakhate. Pamene ankadya, kudafika mai wina atatenga nsupa yagalasi ya mafuta enieni onunkhira, amtengowapatali, a mtundu wa narido. Maiyo adaphwanya nsupa ija, nayamba kuthira mafutawo pamutu pa Yesu.
4
Anthu ena pamenepo adaipidwa nazo nanena kuti, “Chifukwa chiyani kuŵasakaza chotere mafuta onunkhiraŵa?
5
Ndithu mafuta ameneŵa akadatha kuŵagulitsa, pa mtengo wopitirira ndalama zasiliva mazana atatu, kenaka ndalamazo nkukapatsa anthu osauka?” Choncho anthuwo adamupsera mtima mai uja.
6
Koma Yesu adati, “Mlekeni maiyu, mukumuvutiranji kodi? Zimenetu wandichitira iyeyuzi nzabwino kwambiri.
7
Anthu osauka muli nawo nthaŵi zonse, kotero kuti pamene mufuna kuŵachitira zachifundo, mungathe kuŵachitira. Koma Ine simudzakhala nane nthaŵi zonse.
8
Iyeyu wachita zimene akadatha kuchita. Wadzozeratu thupi langa ndi mafuta onunkhira, kuti alikonzeretu lisanaikidwe m'manda.
9
Ndithu ndikunenetsa kuti kulikonse kumene anthu azikalalika Uthenga Wabwino pa dziko lonse lapansi, azidzafotokozanso zimene maiyu wachita, kuti anthu azidzamkumbukira.”
10
Pambuyo pake Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja, adapita kwa akulu a ansembe kuti akapereke Yesu kwa iwo.
11
Pamene iwo adamva zimenezi adakondwa, ndipo adamlonjeza kuti adzampatsa ndalama. Iyeyo tsono adayamba kufunafuna mpata womuperekera kwa iwo.
12
Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, tsiku lomwe anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska, ophunzira a Yesu adamufunsa kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?”
13
Yesu adatuma aŵiri mwa ophunzira ake, naŵauza kuti, “Pitani m'mudzimu. Mukumana ndi munthu wamwamuna atasenza mtsuko wa madzi. Mukamtsatire.
14
Kunyumba kumene ati akaloŵe, mukauze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa kuti, kodi nchiti chipinda cha alendo choti Iwowo adzadyeremo phwando la Paska ndi ophunzira ao?’
15
Iyeyo akakuwonetsani chipinda chachikulu cham'mwamba, momwe akonzamo zonse zofunikira. M'menemo mukatikonzere chakudya.”
16
Ophunzira aja adanyamuka naloŵa mumzindamo. Adachipezadi monga momwe Yesu adaaŵauzira, ndipo adakonza za phwando la Paska.
17
Kutada, Yesu adabwera ndi ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja.
18
Onse atakhala pansi nkumadya, Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti wina mwa inu, mnzanga wodya nane, andipereka kwa adani anga.”
19
Ophunzirawo adamva chisoni, nayamba mmodzimmodzi kumufunsa kuti, “Monga nkukhala ine?”
20
Yesu adaŵayankha kuti, “Ndi wina ndithu mwa khumi ndi aŵirinu, yemwe akusunsa mkate m'mbalemu pamodzi ndi ine.
21
Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Malembo akunenera za Iye. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo. Kukadakhala bwino koposa kwa munthu ameneyo, akadapanda kubadwa.”
22
Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagaŵira ophunzira aja, ndipo adati, “Kwayani, ili ndi thupi langa.”
23
Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu, nkuchipereka kwa ophunzirawo, naamwa onse.
24
Ndipo adaŵauza kuti, “Aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka.
25
Kunena zoona, sindidzamwanso chakumwa cha mtengo wamphesachi, mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.”
26
Tsono ataimba nyimbo yotamanda Mulungu, onse adatuluka nkumapita ku Phiri la Olivi.
27
Pambuyo pake Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya. Paja Malembo akuti, ‘Ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa zidzangoti balala.’
28
Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola ndine kupita ku Galileya.”
29
Petro adati, “Ngakhale onse akhumudwe nkukusiyani, ine ndekha ai.”
30
Yesu adamuuza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino usiku womwe uno, tambala asanalire kachiŵiri, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.”
31
Apo Petro adanenetsanso kuti, “Ngakhale atati andiphere nanu kumodzi, ine sindingakukaneni konse kuti sindikudziŵani.” Ophunzira ena onse aja nawonso adanena chimodzimodzi.
32
Yesu adapita ndi ophunzira ake aja ku malo ena, otchedwa Getsemani. Tsono adauza ophunzirawo kuti, “Inu bakhalani pano, Ine ndikukapemphera.”
33
Adatengako Petro, Yakobe ndi Yohane. Yesu adayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuvutika mu mtima.
34
Adaŵauza kuti, “Mumtima mwanga muli chisoni chachikulu chofa nacho. Inu khalani pompano, koma mukhale masotu.”
35
Adapita patsogolo pang'ono, nadzigwetsa pansi, nkuyamba kupemphera. Adati, “Ngati nkotheka nthaŵi yoopsa ino indipitirire.”
36
Adanenanso kuti, “Abba, Atate, mungathe kuchita chilichonse. Mundichotsere chikho cha masautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
37
Atatero adabwerera kwa ophunzira aja, naŵapeza ali m'tulo. Tsono adafunsa Petro kuti, “Simoni, uli m'tulo kodi iwe? Mongadi walephera kukhala maso ndi kanthaŵi kochepa komwe?
38
Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”
39
Adachokanso nakapemphera ndi mau omwe aja.
40
Pamene adabwerakonso, adaŵapeza ali m'tulo, chifukwa zikope zao zinkalemera ndi tulo. Choncho iwowo adasoŵa choyankha.
41
Pamene adabwerako kachitatu, adati, “Kodi monga mukugonabe ndi kupumula? Basi tsopano. Nthaŵi ija yafika, Mwana wa Munthu akuperekedwa kwa anthu ochimwa.
42
Dzukani, tiyeni tizipita. Suuyu wodzandipereka uja, wafika.”
43
Yesu akulankhula choncho, nthaŵi yomweyo wafika Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Adaabwera ndi khamu la anthu atatenga malupanga ndi zibonga. Anthuwo adaaŵatuma ndi akulu a ansembe, aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda.
44
Wodzampereka uja anali ataŵauza chizindikiro kuti, “Yemwe ndikamumpsompsoneyo, ndi ameneyo. Mukamgwire nkupita naye, osamtaya.”
45
Pamene Yudasi adabwera, adadzangofikira pa Yesu, nkunena kuti, “Aphunzitsi!” Atatero adamumpsompsona.
46
Apo anthu aja adamugwira Yesu.
47
Koma wina mwa ophunzira amene anali naye pamenepo, adasolola lupanga lake, natema wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu.
48
Tsono Yesu adaŵafunsa anthu aja kuti, “Bwanji mwachita kunditengera malupanga ndi zibonga, ngati kuti ndine chigaŵenga?
49
Tsiku ndi tsiku ndidaali nanu m'Nyumba ya Mulungu ndikuphunzitsa, inuyo osandigwira. Koma izi zatere kuti zipherezere zomwe Malembo adanena.”
50
Pamenepo ophunzira ake onse aja adathaŵa, kumsiya yekha.
51
Mnyamata wina ankatsatira Yesu, atangofundira nsalu yokha, opanda chovala china. Anthu aja adaati amgwire,
52
koma iye adaikolopola nsalu ija, nkuthaŵa ali maliseche.
53
Tsono anthu aja adapita naye Yesu kwa mkulu wa ansembe onse. Kumeneko kudaasonkhana onse akulu a ansembe, akulu a Ayuda, ndi aphunzitsi a Malamulo.
54
Petro ankamutsatira Yesu chapatali, mpaka ku bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembe uja. Adakhala pansi pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, nkumaotha nao moto.
55
Akulu a ansembe aja ndi onse a m'Bwalo Lalikulu la Ayuda ankafunafuna umboni woneneza Yesu kuti amuphe, koma osaupeza.
56
Ambiritu ankamuneneza zabodza, koma umboni wao sunkagwirizana.
57
Ena adaimirira nayamba kumneneza zabodza.
58
Adati, “Munthu uyu ife tidamumva akunena kuti, ‘Ine ndidzapasula Nyumba ya Mulunguyi, yomangidwa ndi anthu chabe, ndipo patapita masiku atatu ndidzamanga ina yosamangidwa ndi anthu.’ ”
59
Koma ngakhale aponso zokamba zaozo sizinali zogwirizana.
60
Tsono mkulu wa ansembe onse adaimirira pamaso pao, nafunsa Yesu kuti, “Kodi ulibe poyankha? Nzotani zimene anthuŵa akukunenezazi?”
61
Yesu adangokhala chete, osayankha kanthu. Pamenepo mkulu wa ansembe uja adafunsanso kuti, “Kodi ndiwedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu Wolemekezeka?”
62
Yesu adayankha kuti, “Inde, ndinedi. Ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvuzonse. Mudzamuwona akubwera pa mitambo.”
63
Apo mkulu wa ansembe uja adang'amba zovala zake, nati, “Kodi pamenepa tikusoŵanso mboni zina?
64
Mwadzimvera nokha kunyoza Mulungu koopsaku. Tsono mukuganiza bwanji?” Onse adagamula kuti ayenera kuphedwa.
65
Ena adayamba kumthira malovu, namuphimba m'maso nkumamuwomba makofi, namanena kuti, “Lotatu, wakumenya ndani?” Alonda aja nawonso adayamba kummenya.
66
Petro anali kunsi pa bwalo. Mtsikana wina, wantchito wa mkulu wa ansembe onse, adafika pomwepo.
67
Ataona Petro akuwotha moto, adamuyang'anitsitsa, nati, “Inunsotu munali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.”
68
Koma Petro adakana, adati, “Zimenezo ine sindikuzidziŵa, sindikuzimvetsa konse.” Ndipo adatuluka kumapita cha ku chipata. Pamenepo tambala adalira.
69
Koma mtsikana uja adamuwona, nayambanso kuuza amene anali pamenepo kuti, “Akulu ameneŵa anali m'gulu lomweli.”
70
Koma Petro adakananso. Patangopita kanthaŵi, anthu amene adaali pamenepo adamuuza Petro kuti, “Ndithu nawenso ndiwe wa gulu lomweli. Kodi kwanu si ku Galileya iwe?”
71
Koma Petro adayamba kudzitemberera nkumalumbira kuti, “Mtheradi, munthu amene mukunenayu ine sindimdziŵa.”
72
Nthaŵi yomweyo tambala adalira kachiŵiri. Tsono Petro adakumbukira mau aja a Yesu akuti, “Tambala asanalire kaŵiri, ukhala utakana katatu kuti sundidziŵa.” Pomwepo Petro adayamba kulira misozi.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16