bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Mark 15
Mark 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 16 →
1
M'maŵa kutangocha, akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda ndi aphunzitsi a Malamulo, pamodzi ndi ena onse a m'Bwalo Lalikulu la Ayuda adapanga upo. Adammanga Yesu napita naye kwa Pilato.
2
Pilatoyo adafunsa Yesu kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adamuyankha kuti, “Mwanena nokha.”
3
Akulu a ansembe aja adayamba kumneneza zambiri.
4
Pilato adamufunsanso kuti, “Kodi ulibe poyankha? Ona zonse zimene akukunenezazi.”
5
Koma Yesu sadayankhenso kanthu, kotero kuti Pilato adadabwa.
6
Pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska, bwanamkubwa ankaŵamasulira mkaidi mmodzi, yemwe Ayudawo ankapempha.
7
Panali munthu wina, dzina lake Barabasi, amene anali m'ndende pamodzi ndi anthu ena chifukwa choukira Boma ndi kupha anthu.
8
Tsono chikhamu cha anthu chidabwera, nkuyamba kupempha Pilato kuti aŵachitire zomwe adaazoloŵera.
9
Pilato adaŵafunsa kuti, “Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayudayi?”
10
Adaatero chifukwa adaadziŵa kuti Yesuyo akulu a ansembewo angodzampereka chifukwa cha kaduka chabe.
11
Koma akulu a ansembewo adasonkhezera anthu onse aja kuti apemphe kuŵamasulira Barabasi.
12
Tsono Pilato adaŵafunsanso kuti, “Nanga tsono mukuti ndichite naye chiyani uyu amene mukuti ndi Mfumu ya Ayudayu?”
13
Anthuwo adafuula kuti, “Mpachikeni pa mtanda!”
14
Pilato adaŵafunsa kuti, “Adalakwanji?” Koma iwo adafuula koposa kuti, “Mpachikeni pa mtanda!”
15
Choncho Pilato, pofuna kukondwetsa anthuwo, adaŵamasulira Barabasi, nalamula kuti Yesu akwapulidwe. Pambuyo pake adampereka kuti akampachike pa mtanda.
16
Pamenepo asilikali adaloŵetsa Yesu m'bwalo, kunyumba kwa bwanamkubwa, nasonkhanitsa gulu lonse la asilikali anzao.
17
Adamuveka chovala chofiirira, naluka nsangamutu yaminga nkuiika pamutu pake.
18
Kenaka adayamba kumampatsa moni kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda.”
19
Ankamumenya m'mutu ndi ndodo, namamthira malovu, nkumamugwadira monyodola.
20
Ataseŵera naye mwachipongwe choncho, adamuvula chovala chija, namuvekanso zovala zake. Kenaka adamtenga, nkupita naye kuti akampachike pa mtanda.
21
Pa njira adakumana ndi munthu wina, amene ankadutsa pamenepo kuchokera ku midzi. Munthuyo anali Simoni wa ku Kirene, bambo wake wa Aleksandro ndi Rufu. Tsono asilikali aja adamkakamiza kuti asenze mtanda wa Yesu.
22
Iwowo adapita naye Yesuyo ku malo otchedwa Gologota, (ndiye kuti “Malo a Chibade cha Mutu.”)
23
Adaafuna kumpatsa vinyo wosanganiza ndi mure kuti amwe, koma Iye adakana.
24
Atampachika pa mtanda, adagaŵana zovala zake. Adaachita maere kuti aone zimene aliyense atenge.
25
Pamene adampachika pa mtanda, nkuti nthaŵi ili 9 koloko m'maŵa.
26
Mau osonyeza mlandu womuphera, adaaŵalemba motere, “Mfumu ya Ayuda.”
27
Pamodzi ndi Yesu adaapachikanso pa mitanda zigaŵenga ziŵiri, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere. [
28
Motero zidachitikadi zimene mau a Mulungu adaanena kuti, “Adamuyesa mnzao wa anthu ophwanya malamulo.”]
29
Anthu amene ankadutsa pamenepo ankamunyodola. Ankapukusa mitu nkumanena kuti, “Ha, suja iwe unkati, ‘Ndidzapasula Nyumba ya Mulungu nkuimanganso pa masiku atatu?’
30
Tadzipulumutsatu, tsika pamtandapo!”
31
Nawonso akulu a ansembe ankamuseka, nkumauzana ndi aphunzitsi a Malamulo kuti, “Adapulumutsa anthu ena, koma akulephera kudzipulumutsa Iye yemwe!
32
Uja ankati ndi Mpulumutsi wolonjezedwayu, Mfumu ya Aisraele, atatsikatu tsopano pamtandapa, kuti tiwone ndi kumkhulupirira!” Ndiponso amene adaŵapachika pamodzi naye aja ankamunyoza.
33
Nthaŵi itakwana 12 koloko masana, padaagwa mdima pa dziko lonse mpaka pa 3 koloko.
34
Tsono nthaŵi ili 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti, “Eloi, Eloi, lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?”
35
Atamva mauwo, ena amene adaaimirira pamenepo adati, “Tamverani, akuitana Eliya.”
36
Motero wina adathamanga nakaviika chinkhupule m'vinyo wosasa, nkuchitsomeka ku bango nampatsira, kuti amwe. Anzakewo adati, “Taima, tiwone ngati Eliyayo abweredi kudzamtsitsa.”
37
Koma Yesu adafuula kwakukulu, natsirizika.
38
Chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi.
39
Mkulu wa asilikali amene adaaimirira pomwepo kuyang'anana naye, ataona kuti Yesu watsirizika akufuula chotero, adati, “Ndithudi, munthuyu adaalidi Mwana wa Mulungu.”
40
Patali poteropo padaali azimai, akungoyang'anitsitsa. Ena mwa iwo anali Maria wa ku Magadala, ndi Maria, mai wa Yakobe wamng'ono uja ndi wa Yosefe, ndiponso Salome.
41
Azimaiŵa ankatsata Yesu pamene Iye anali ku Galileya, ndi kumamtumikira. Padaalinso azimai ena ambiri omwe adaabwera naye ku Yerusalemuko.
42
Tsopano chisisira chinali chitagwa. Ndiye popeza kuti linali Lachisanu, tsiku lokonzekera Sabata,
43
Yosefe wa ku Arimatea adafika. Adaali mkulu wodziŵika ndithu, wa m'Bwalo Lalikulu la Ayuda. Nayenso ankayembekeza Ufumu wa Mulungu. Tsono iye adalimba mtima, napita kwa Pilato kukapempha kuti ampatsire mtembo wa Yesu.
44
Pilato adaadabwa kumva kuti Yesu wafa kale. Choncho adaitanitsa mkulu wa asilikali uja, namufunsa kuti, “Kodi Yesu wafa kaledi?”
45
Mkulu wa asilikaliyo atavomera, Pilato adamlola Yosefe kuti akatenge mtembowo.
46
Yosefeyo adagula nsalu yoyera yabafuta, natsitsa mtembo uja nkuukuta ndi nsaluyo. Adauika m'manda ochita chosema m'thanthwe, kenaka adagubuduzira chimwala pa khomo kutseka pamandapo.
47
Maria uja wa ku Magadala, ndi Maria mai wa Yosefe, ankaona kumene adamuika Yesu.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16