bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Mark 10
Mark 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 11 →
1
Yesu adachoka ku Kapernao, napita ku dera la ku Yudeya ndi ku dera la kutsidya kwa mtsinje wa Yordani. Anthu ambirimbiri adadzasonkhananso kwa Iye, ndipo monga ankazoloŵera, adayambanso kuŵaphunzitsa.
2
Tsono kudafika Afarisi ena, namufunsa kuti, “Kodi nkololedwa kuti munthu asudzule mkazi wake?” Pomufunsa chonchi ankangofuna pomupezera chifukwa.
3
Koma Yesu poyankha adati, “Kodi Mose adakulamulani zotani?”
4
Iwo adati, “Mose adalola kuti munthu azilembera mkazi wake kalata yachisudzulo kenaka nkumuchotsa.”
5
Yesu adati, “Mose adaakulemberani lamulo limeneli chifukwa cha kukanika kwanuku.
6
Komatu pachiyambi paja, pamene Mulungu adalenga zonse, adaŵalenga anthu, wina wamwamuna wina wamkazi.
7
Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ndi amai, nakaphatikizana ndi mkazi wake,
8
ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi. Choncho tsopano salinso aŵiri, koma thupi limodzi.
9
Tsono zimene Mulungu wazilumikiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”
10
Pamene adaloŵanso m'nyumba, ophunzira adamufunsanso Yesu za nkhani yomweyi.
11
Iye adaŵauza kuti, “Aliyense amene asudzula mkazi wake nakwatira wina, akuchita chigololo, ndipo akumchimwira mkazi wakeyo.
12
Chimodzimodzinso ngati mkazi asudzula mwamuna wake, kenaka nkukwatiwa ndi wina, nayenso akuchita chigololo.”
13
Anthu ena ankabwera ndi ana kwa Yesu kuti aŵakhudze ndi kuŵadalitsa, ophunzira ake nkumaŵazazira.
14
Yesu ataona zimenezi, adakalipa naŵauza kuti, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere.
15
Ndithu ndikunenetsa kuti yemwe salandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, ameneyo sadzaloŵamo.”
16
Atatero adayamba kuŵafungata anawo, naŵasanjika manja ndi kuŵadalitsa.
17
Pamene Yesu ankanyamuka kuti azipita, munthu wina adamthamangira. Adadzamugwadira namufunsa kuti, “Aphunzitsi abwino, kodi ndizichita chiyani kuti ndikalandire moyo wosatha?”
18
Yesu adamuyankha kuti, “Ukunditchuliranji wabwino? Wabwinotu ndi mmodzi yekha, Mulungu basi.
19
Malamulo ukuŵadziŵa: Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama, usadyerere mnzako, lemekeza atate ako ndi amai ako.”
20
Munthu uja adati, “Aphunzitsi, zonsezi ndakhala ndikuzitsata kuyambira ndili mwana.”
21
Yesu atamuyang'ana, adamkonda nkumuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”
22
Atamva zimenezo, munthu uja nkhope yake idagwa, adangochokapo ali wovutika mu mtima, chifukwa adaali munthu wa chuma chambiri.
23
Yesu adayang'ana ophunzira ake amene adaamzungulira naŵauza kuti, “Nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”
24
Ophunzirawo adadabwa nawo kwambiri mau akeŵa. Koma Yesu adabwerezanso, adati, “Ndithu, inu ana anga, nkwapatali kukaloŵa mu Ufumu wa Mulungu.
25
Nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wachuma akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”
26
Pamenepo ophunzira aja adazizwa koposa, nayamba kufunsana kuti, “Tsono nanga angathe kupulumuka ndani?”
27
Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu nkosathekadi, koma ndi Mulungu ai, nkotheka. Paja ndi Mulungu zonse nzotheka.”
28
Pamenepo Petro adayamba kulankhula naye, adati, “Ifetu paja tidasiya zonse kuti tizikutsatani.”
29
Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wosiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena atate, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine, ndiponso chifukwa cha Uthenga Wabwino,
30
ameneyo pansi pompano adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale: nyumba, abale, alongo, amai, ana, minda, komanso mazunzo. Ndipo kutsogoloko adzalandira moyo wosatha.
31
Komatu ambiri amene ali oyambirira adzakhala otsirizira, ndipo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira.”
32
Pamene iwo anali pa ulendo wopita ku Yerusalemu, Yesu ankayenda patsogolo pa ophunzira ake. Ophunzirawo anali oda nkhaŵa kwambiri. Ndipo anthu amene ankaŵatsatira anali ndi mantha. Yesu adaŵaitaniranso pambali ophunzira khumi ndi aŵiri aja, nayamba kuŵafotokozera zimene zinalikudzamugwera.
33
Adati, “Tilitu pa ulendo wa ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Iwo akamuweruza ndi kugamula kuti aphedwe. Ndipo akampereka kwa anthu akunja.
34
Amenewo akamchita chipongwe, akamthira malovu, akamkwapula nkumupha. Koma patapita masiku atatu, Iye adzauka.”
35
Yakobe ndi Yohane, ana aja a Zebedeo, adadzauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ife timati bwanji titakupemphani kanthu, mutichitire.”
36
Yesu adaŵafunsa kuti, “Inuyo mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani?”
37
Iwo adati, “Timafuna kuti pamene mudzakhale mu ulemerero wanu, mudzatiike wina ku dzanja lanu lamanja, wina ku dzanja lanu lamanzere.”
38
Koma Yesu adati, “Simukudziŵa zimene mukupempha. Kodi inu mungathe kumwa nao chikho chamasautso chimene ndikudzamwera Ine? Kodi inu mungathe kulandira nao ubatizo wa mavuto umene ndikudzalandira Ine?”
39
Iwo aja adayankha kuti, “Inde, tingathe.” Apo Yesu adati, “Chabwino, chikho chimene Ine ndikudzamwacho, inunso mudzamwa nao, ndipo ubatizo umene Ine ndikudzalandirawo, inunso mudzalandira nao.
40
Koma Ineyo si udindo wanga kusankha munthu kuti akhale ku dzanja langa lamanja, kapena ku dzanja langa lamanzere. Mulungu ndiye adzapereke malo ameneŵa kwa omwe Iye mwini adaŵakonzera.”
41
Pamene khumi ena aja adamva zimenezi, adapsera mtima Yakobeyo ndi Yohaneyo.
42
Koma Yesu adaŵaitana ophunzira akewo, naŵauza kuti, “Mukudziŵa kuti pakati pa anthu akunja, anthu amene amati ngolamulira, amadyera anthu ao masuku pa mutu. Akuluakulu aonso amaonetsadi mphamvu zao pa anthu ao.
43
Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, azikhala mtumiki wanu.
44
Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, azikhala kapolo wa onse.
45
Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
46
Yesu ndi ophunzira ake pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu adafika ku mzinda wa Yeriko. Tsono pamene ankatuluka mumzindamo, adapeza wakhungu wina wopemphapempha atakhala pansi pamphepete pa mseu. Munthuyo dzina lake anali Baratimeo, mwana wa Timeo.
47
Tsono iyeyo atamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, adayamba kufuula kuti, “Inu Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.”
48
Anthu ambiri adamzazira kuti akhale chete. Koma iye adafuulirafuulira kuti, “Inu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.”
49
Yesu adaima, nauza anthu kuti, “Tamuitanani.” Anthu aja adamuitana wakhunguyo namuuza kuti, “Limba mtima, nyamuka, akukuitana.”
50
Pomwepo iye uja adadzambatuka, mwinjiro wake uko chi, kuthamangira kwa Yesu.
51
Yesu adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Wakhunguyo adayankha kuti, “Mbuyanga, ndikufuna kuti ndizipenyanso.”
52
Yesu adamuuza kuti, “Chabwino, ungathe kupita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Nthaŵi yomweyo adayambadi kupenya, nkumatsata Yesu pa ulendowo.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16