bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Mark 8
Mark 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 9 →
1
Pasanapite nthaŵi yaitali anthu ambirimbiri adasonkhananso. Pamene Yesu adaona kuti anthuwo alibe chakudya, adaitana ophunzira ake naŵauza kuti,
2
“Ndikuŵamvera chifundo anthuŵa, chifukwa akhala nane masiku atatu tsopano, ndipo alibe chakudya.
3
Ndikangoŵabweza kwao ali ndi njala chonchi, alefuka pa njira, chifukwa ena achokera kutali.”
4
Ophunzira ake adamufunsa kuti, “Anthu ochuluka chotereŵa munthu angaŵapezere bwanji chakudya chokwanira, kuthengo ngati kuno?”
5
Yesu adaŵafunsa kuti, “Buledi ndiye muli naye mngati?” Iwo aja adati, “Msanu ndi muŵiri.”
6
Apo Yesu adalamula anthu aja kuti akhale pansi. Kenaka adatenga buledi msanu ndi muŵiri uja, adathokoza Mulungu, namunyemanyema nkumupereka kwa ophunzira ake kuti akagaŵire anthu aja. Ophunzira aja adaŵagaŵiradi anthuwo.
7
Adaalinso ndi tinsomba toŵerengeka. Yesu adathokoza Mulungu chifukwa cha tinsombato, nalamula ophunzira ake kuti atiperekenso kwa anthu aja.
8
Anthu adadya mpaka kukhuta. Adatola zotsala, nadzaza madengu asanu ndi aŵiri.
9
Anthu amene adaali pamenepo, amuna okha adaalipo ngati zikwi zinai.
10
Pambuyo pake Yesu adatsazikana nawo anthu aja, kenaka Iye ndi ophunzira ake adaloŵa m'chombo napita ku dera la Dalamanuta.
11
Tsiku lina kudabwera Afarisi ena, nayamba kutsutsana ndi Yesu. Iwo adaapempha Yesu kuti aŵaonetse chizindikiro chozizwitsa chochokera kumwamba. Pakutero ankangofuna kumutchera msampha.
12
Yesu adadzumira mu mtima nati, “Kodi bwanji anthu a mbadwo uno amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa? Ndithu ndikunenetsa kuti anthu a mbadwo unowu sadzachiwona chizindikiro akufunacho.”
13
Atatero, Yesu adaŵasiya, naloŵanso m'chombo kuwolokera ku tsidya lina.
14
Ophunzira a Yesu anali ataiŵala kutenga buledi, kotero kuti m'chombomo adaali ndi buledi mmodzi yekha.
15
Tsono Yesu adayamba kuŵalangiza kuti, “Muchenjere nacho chofufumitsira buledi cha Afarisi ndi cha Herode.”
16
Apo ophunzirawo adayamba kukambirana nkumati, “Akuterotu chifukwa tilibe buledi.”
17
Yesu adaadziŵa zimene iwo ankanena. Ndiye adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukukambirana zakuti mulibe buledi? Kodi mpaka pano simunazindikirebe kapena kumvetsa? Kani mitu yanu ndi youma, eti?
18
Maso muli nawo, kodi simuwona? Ndipo makutu muli nawo, kodi simumva? Kodi inu simukukumbukira zijazi?
19
Muja ndidaanyemanyema buledi msanu kuti ndidyetse anthu zikwi zisanumu, kodi mudaadzaza madengu angati a zotsala?” Ophunzirawo adati, “Madengu khumi ndi aŵiri.”
20
Yesu adaŵafunsanso kuti, “Nanga muja ndidaanyemanyema buledi msanu ndi muŵiri ndi kudyetsa anthu zikwi zinaimu, mudaatola madengu angati a zotsala?” Iwo adati, “Madengu asanu ndi aŵiri.”
21
Apo Yesu adati, “Nanga ndiye simunamvetsebe?”
22
Yesu ndi ophunzira ake adafika ku Betsaida. Kumeneko anthu adabwera ndi munthu wakhungu, napempha Yesu kuti amchiritse pomkhudza.
23
Yesu adamgwira dzanja, natuluka naye kunja kwa mudzi. Adapaka malovu m'maso mwa munthuyo, namsanjika manja nkumufunsa kuti, “Kodi ukuwona kanthu?”
24
Munthu uja adaŵeramuka nati, “Ndikuwona anthu akuyenda, koma akuwoneka ngati mitengo.”
25
Yesu adamuikanso manja kumaso kwake. Munthu uja adayang'anitsitsa ndipo adachira, nayamba kumapenya zonse bwino lomwe.
26
Yesu adamuuza kuti apite kwao, namlamula kuti, “Usaloŵe ndi m'mudzi momwemu.”
27
Yesu ndi ophunzira ake adapita ku midzi ya ku Kesareya-Filipi. Pa njira Yesu adafunsa ophunzira akewo kuti, “Kodi anthu amati Ine ndine yani?”
28
Iwo adayankha kuti, “Ena amati ndinu Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya, enanso amati ndinu mmodzi mwa aneneri.”
29
Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Nanga inuyo, mumati ndine yani?” Petro adamuyankha kuti, “Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja.”
30
Yesu adaŵalamula kuti asauze munthu wina aliyense za Iye.
31
Yesu adayamba kuphunzitsa ophunzira ake kuti, “Mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri. Akulu a Ayuda, ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzamkana. Iye adzaphedwa, koma patapita masiku atatu adzauka.”
32
Zimenezi adazinena mosabisa konse. Apo Petro adamtengera pambali, nayamba kumdzudzula.
33
Koma Yesu adacheuka, nayang'ana ophunzira ake ena aja, ndipo adadzudzula Petro. Adati, “Choka apa, iwe Satana! Maganizo akoŵa si maganizo a Mulungu ai, ndi maganizo a anthu chabe.”
34
Pambuyo pake Yesu adaitana khamu la anthu pamodzi ndi ophunzira aja kuti adze pafupi naye, ndipo adaŵauza kuti, “Munthu wofuna kutsana Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata.
35
Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine ndi Uthenga Wabwino, adzaupulumutsa.
36
Nanga ndiye kuti munthu wapindulanji atapata zonse za pansi pano, iyeyo nkutaya moyo wake?
37
Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake?
38
Tsono ngati munthu achita manyazi ndi Ine ndiponso ndi mau anga pamaso pa anthu ochimwa a makonoŵa amene ali osakhulupirika, ameneyo nanenso Mwana wa Munthune ndidzachita naye manyazi pamene ndidzabwera pamodzi ndi angelo oyera, ndili ndi ulemerero wa Atate anga.”
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16