bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Mark 16
Mark 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
1
Tsiku la Sabata ya Ayuda litapita, Maria wa ku Magadala, ndi Maria, mai wa Yakobe, ndiponso Salome adakagula zonunkhira kuti akadzoze mtembo wa Yesu.
2
M'mamaŵa ndithu pa tsiku lotsatira Sabatayo, adapita kumanda kuja, dzuŵa litatuluka.
3
Ankafunsana kuti, “Kodi ndani akatichotsere chimwala cha pakhomo pa manda chija?”
4
Koma poyang'anitsitsa adaona kuti chimwalacho achigubuduza kale; tsonotu chinali chachikuludi.
5
Ataloŵa m'mandamo adaona mnyamata wakhala pansi mbali ya ku dzanja lamanja, atavala mkanjo woyera. Azimaiwo adadzidzimuka.
6
Koma mnyamatayo adaŵauza kuti, “Musade nkhaŵa. Mukufuna Yesu wa ku Nazarete, uja adaampachika pa mtandayu. Wauka, sali muno. Taonani, si apa pamene adaamuika.
7
Koma inu pitani mukauze ophunzira ake, makamaka Petro, kuti, ‘Iye watsogola kunka ku Galileya. Mukamuwonera kumeneko, monga muja adakuuziranimu.’ ”
8
Pamenepo azimaiwo adatuluka nkuthaŵako kumandako, popeza kuti adaagwidwa ndi mantha, mpaka kumangonjenjemera. Ndipo chifukwa cha manthawo sadauze munthu aliyense kanthu. [
9
Yesu atauka kwa akufa, m'maŵa ndithu, tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, poyambayamba adaaonekera Maria wa ku Magadala, uja adaamtulutsa mizimu yoipa isanu ndi iŵiriyu.
10
Mariayo adapita kukauza amene ankakhala ndi Yesu aja. Iwowo nkuti ali ndi chisoni ndipo akungolira.
11
Ngakhale atamva kuti Yesu ali moyo, ndipo kuti Maria wamuwona, iwo sadakhulupirire.
12
Pambuyo pake Yesu, ali ndi maonekedwe osiyana, adaonekera ophunzira ake ena aŵiri, pamene iwowo anali pa ulendo kunja kwa mzinda wa Yerusalemu.
13
Ophunzirawo adabwerera kudzauza anzao aja, koma iwonso sadaŵakhulupirire.
14
Potsiriza Yesu adaonekera ophunzira khumi ndi mmodzi aja alikudya. Adaŵadzudzula chifukwa cha kusakhulupirira kwao ndi kupulupudza kwao, chifukwa sadakhulupirire anzao aja amene adaamuwona Iye atauka kwa akufa.
15
Tsono adaŵauza kuti, “Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni anthu onse Uthenga Wabwino.
16
Amene akakhulupirire ndi kubatizidwa, adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira, adzaweruzidwa kuti ngwolakwa.
17
Okhulupirira azidzachita zozizwitsa izi: azidzatulutsa mizimu yoipa potchula dzina langa, azidzalankhula zilankhulo zachilendo,
18
ndipo akagwira njoka kapena kumwa chakumwa chotha kuŵapha, sadzapwetekedwa. Akasanjika manja pa anthu odwala, anthuwo azidzachira.”
19
Ambuye Yesu atalankhula nawo, adatengedwa kupita Kumwamba, nakakhala ku dzanja lamanja la Mulungu.
20
Tsono ophunzira aja adanka nalalika ponseponse. Ambuye ankagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo ankatsimikiza mau ao ndi zozizwitsa zimene ankachita.]
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16