bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Mark 3
Mark 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 4 →
1
Yesu adakaloŵanso m'nyumba yamapemphero. M'menemo mudaali munthu wina wopuwala dzanja.
2
Anthu ena ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, motero ankangomuyang'anitsitsa kuti aone ngati achiritse munthuyo pa tsiku la Sabata.
3
Yesu adalamula munthuyo kuti, “Imirira, bwera kutsogolo kuno.”
4
Tsono adafunsa anthuwo kuti, “Kodi pa tsiku la Sabata chololedwa nchiti? Kuchitira anthu zabwino, kapena kuŵachita zoipa? Kupulumutsa moyo wa munthu, kapena kuuwononga?” Anthuwo adangoti chete.
5
Pamenepo Yesu mtima wake udamuŵaŵa, poona kuti anali anthu okanika chotero, ndipo adaŵayang'ana ndi mkwiyo. Tsono adalamula munthuyo kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino.
6
Pamenepo Afarisi aja adatuluka nakachita upo ndi anthu a m'chipani cha Herode, kuti apangane njira yophera Yesu.
7
Yesu pamodzi ndi ophunzira ake adachokapo napita ku Nyanja ya Galileya. Khamu lalikulu la anthu lidamtsatira.
8
Anthu ake anali a ku Galileya, ena a ku Yudeya ndi ku Yerusalemu, ena a ku Idumeya, ndi kutsidya kwa Yordani, ndiponso kudera la ku Tiro ndi ku Sidoni. Onsewo adaafika kwa Iye, chifukwa anali atamva zimene Iye ankachita.
9
Yesu adauza ophunzira ake kuti amuikire chombo pafupi, kuwopa kuti anthu angayambe kumpanikiza, chifukwa chidaali chikhamu chachikulu.
10
Pakuti anali atachiritsa anthu ambiri, ndipo onse amene adaali ndi matenda ankakankhana pofuna kuti amkhudze.
11
Mizimu yoipa inkati ikamuwona, inkadzigwetsa pansi pafupi ndi Iye nkumafuula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”
12
Koma Iye ankailetsa mwamphamvu kuti isamuulule.
13
Yesu adakwera ku phiri, ndipo adaitana anthu amene Iye mwini ankaŵafuna, iwo nkupitadi kumene kunali Iyeko.
14
Tsono adasankhapo khumi ndi aŵiri, naŵatcha dzina loti, “Atumwi.” Adaŵauza kuti, “Ndasankha inu kuti muzikhala nane, ndidzakutumani kukalalika,
15
ndipo mudzakhala ndi mphamvu zotulutsira mizimu yoipa.”
16
Anthu khumi ndi aŵiri amene adaaŵasankhawo ndi aŵa: Simoni (amene Yesu adamutcha dzina loti Petro),
17
Yakobe ndi mbale wake Yohane, ana aja a Zebedeo (ameneŵa adaŵapatsa dzina lina lakuti Aboaneje, ndiye kuti “Oopsa ngati bingu”),
18
Andrea ndi Filipo, kudza Bartolomeo, Mateyo, Tomasi, Yakobe (mwana wa Alifeyo), Tadeyo, Simoni (wa m'chipani chandale cha Azelote,)
19
ndiponso Yudasi Iskariote (amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake.)
20
Pambuyo pake Yesu adapita kwao, ndipo anthu ambiri adasonkhananso, kotero kuti Iye ndi ophunzira ake analibe ndi mpata womwe wodyera chakudya.
21
Achibale ake atamva zimenezi, adabwera kuti adzamtenge, chifukwa ankati, “Wachita misala.”
22
Aphunzitsi ena a Malamulo, amene adaabwera kuchokera ku Yerusalemu, ankanena kuti, “Munthu ameneyu wagwidwa ndi Belezebulu.” Ankatinso, “Mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipa nzochokera kwa mkulu wa mizimuyo.”
23
Tsono Yesu adaitana anthu kuti adze pafupi, nanena mwafanizo kuti, “Kodi a mu ufumu wa Satana angathe bwanji kutulutsana okhaokha?
24
Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo sungalimbe.
25
Ndipo anthu a m'banja limodzi akayamba kugaŵikana, banja lotere silingalimbe.
26
Tsono ngati a mu ufumu wa Satana aukirana okhaokha nagaŵikana, Satanayo sangalimbe, ndiye kuti watha basi.
27
“Wina sangathe kungoloŵa m'nyumba ya munthu wamphamvu nkumulanda katundu wake. Amayamba wammanga, kenaka ndiye kufunkha za m'nyumba mwakemo.
28
“Ndithu ndikunenetsa kuti anthu angathe kukhululukidwa machimo onse, ngakhalenso zonena zao zonse zomunyoza Mulunguyo.
29
Koma aliyense wonyoza Mzimu Woyera, sadzakhululukidwa konse. Tchimo lakelo limakhala mpaka muyaya.”
30
Yesu adalankhula zimenezi poona kuti anthu aja ankanena kuti, “Wagwidwa ndi mzimu woipa.”
31
Amai ake ndi abale ake a Yesu adabwera kunyumbako. Adaima panja, natuma anthu kuti akamuitane.
32
Anthu ambirimbiri adaakhala pansi pomzungulira. Ndiye iwo aja adamuuza kuti, “Amai anu ndi abale anu ali panjapa, akukufunani.”
33
Koma Iye adati, “Amai anga! Abale anga! Otinso?”
34
Apo adayang'ana anthu amene anali pomzungulira aja nati, “Inetu amai anga ndi abale anga ndi aŵa.
35
Aliyense wochita zimene Mulungu akufuna, ameneyo ndiye mbale wanga ndi mlongo wanga ndi amai anga.”
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16