bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Mark 7
Mark 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 8 →
1
Tsiku lina Afarisi ena pamodzi ndi aphunzitsi ena a Malamulo, amene adaachokera ku Yerusalemu, adasonkhana kwa Yesu.
2
Iwo adaaona kuti ophunzira ake ena ankangodya chakudya osasamba m'manja moyenera (ndiye kuti mosasamala mwambo wosamba m'manja.)
3
Pajatu Afarisi ndi Ayuda ena onse saadya asanasambe m'manja mwa njira yoyenera. Amatero kuti asunge mwambo wa makolo.
4
Ndipo akachokera ku msika, saadya osasamba m'manja. Amasunganso miyambo ina yambiri imene makolo ao adaŵasiyira, monga kutsuka zikho, miphika, ndi ziŵiya zamkuŵa [ndi mabedinso.]
5
Choncho Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo aja adamufunsa Yesu kuti, “Chifukwa chiyani ophunzira anu sasunga mwambo wa makolo, koma amangodya chakudya osasamba m'manja moyenera?”
6
Yesu adaŵayankha kuti, “Inu anthu achiphamaso, ndithu mneneri Yesaya adaanenadi zoona muja adaalemba kuti, “ ‘Anthu aŵa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe, koma mtima wao uli kutalitali ndi Ine.
7
Amandipembedza inde, koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu, chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni, ndi malamulo a anthu chabe.’ ”
8
Kenaka Yesu adati, “Inu mumasiya Malamulo a Mulungu, nkumasunga miyambo ya anthu.”
9
Tsono popitiriza mau, Yesu adati, “Koma ndiye muli ndi njira yanu yochenjera yosiyira Malamulo a Mulungu kuti musunge miyambo yanu.
10
Paja Mose adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’
11
Koma inu mumati, ‘Munthu akauza atate ake kapena amai ake kuti, “Zimene ndikadakuthandiza nazoni zasanduka Korobani,” (ndiye kuti zoperekedwa kwa Mulungu),
12
ameneyo sasoŵanso kuŵathandiza atate ake ndi amai ake.’
13
Pakutero mau a Mulungu inu mumaŵasandutsa achabechabe, chifukwa cha mwambo wanu umene mumasiyirana. Ndipo mumachita zinanso zambiri zotere.”
14
Pambuyo pake Yesu adaitananso anthu aja kuti adze pafupi, ndipo adaŵauza kuti, “Mverani nonsenu, ndipo mumvetse bwino.
15
Palibe chinthu chochokera kunja ndi kuloŵa m'kati mwa munthu chimene chingathe kumuipitsa. Koma zimene zimatuluka mwa munthu ndizo zimamuipitsa.” [
16
“Yemwe ali ndi makutu akumva, amve!”]
17
Pamene Yesu adasiya khamu lija la anthu nakaloŵa m'nyumba, ophunzira ake adamufunsa za fanizo limeneli.
18
Iye adaŵayankha kuti, “Kani ngakhale inunso simumvetsa? Kodi simukudziŵa kuti chilichonse chochokera kunja, ndi kuloŵa mwa munthu, sichingathe kumuipitsa?
19
Pajatu sichiloŵa mumtima mwake, koma m'mimba, pambuyo pake nkumakatayidwa ku thengo.” (Pakunena zimenezi, Yesu adagamula kuti zakudya zonse anthu angathe kuzidya.)
20
Adatinso, “Zimene zimatuluka mwa munthu, ndizo zimamuipitsa.
21
Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za chiwerewere, za kuba, za kuphana,
22
zigololo, masiriro, kuipa mtima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa.
23
Zoipa zonsezi zimachokera m'kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa.”
24
Yesu adanyamuka kupita ku dera la ku Tiro. Adakakhala kunyumba kwina, ndipo sadafune kuti anthu adziŵe kuti ali kumeneko. Komabe sadathe kubisika.
25
Nthaŵi yomweyo mai wina, amene mwana wake wamkazi ankavutika ndi mzimu woipa, adamva za Iye. Adabwera kwa Yesu nagwada kumapazi kwake.
26
Maiyo anali mkunja, wa mtundu wa anthu a ku Siro-Fenisiya. Adapempha Yesu kuti akatulutse mzimu woipawo mwa mwana wake.
27
Koma Yesu adamuyankha kuti, “Ai, alekeni ana ayambe adya nkukhuta. Sibwino kutenga chakudya cha ana nkuponyera agalu.”
28
Apo maiyo adati, “Nzoonadi, Ambuye, koma suja ngakhale agalu omwe amakhala m'munsi mwa tebulo nkumadyako nyenyeswa zimene ataya ana?”
29
Apo Yesu adamuuza kuti, “Chifukwa cha mau mwanenaŵa, pitani, mzimu woipawo watuluka mwa mwana wanu.”
30
Mai uja adabwerera kunyumba kwake, nakapezadi mwanayo ali gone pa bedi, mzimu woipa uja utatuluka.
31
Yesu adachokanso ku dera lija la ku Tiro, namayenda kudutsa dera la ku Sidoni, kupita ku nyanja ya ku Galileya, kudzera pakati pa dera la Mizinda Khumi.
32
Anthu ena adabwera kwa Iye ndi munthu yemwe anali gonthi ndi wolankhula movutikira. Anthuwo adapempha Yesu kuti amchiritse pomusanjika manja munthuyo.
33
Yesu adatengera munthu uja pambali kumchotsa pa khamu la anthu. Adapisa zala m'makutu a munthuyo, nalavula malovu, nkukhudza lilime la munthu uja.
34
Adayang'ana kumwamba, nadzuma, nkumuuza kuti, “Efata!” ndiye kuti “Tsekuka!”
35
Pomwepo makutu a munthuyo adatsekuka, ndipo chimene chinkamanga lilime lake chidamasuka, mpaka adayamba kulankhula bwino lomwe.
36
Yesu adalamula anzake a munthuyo kuti, “Musakauzetu wina aliyense zimenezi.” Koma ngakhale adaŵaletsa mwamphamvu choncho, iwo adanka nalengeza ndithu zimenezi.
37
Ndipo anthu adazizwa kopitirira ndithu. Adati, “Ameneyu amachita zonse bwino. Ngakhale agonthi amaŵachiritsa nkumamva, ndipo osalankhula amaŵalankhulitsa.”
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16