bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Mark 9
Mark 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 10 →
1
Yesu adaŵauzanso kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti alipo ena pompano omwe sadzafa asanaone Ufumu wa Mulungu utafika ndi mphamvu.”
2
Patapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro ndi Yakobe ndi Yohane, nakwera nawo ku phiri lalitali, kwaokha. Tsono maonekedwe a Yesu adasinthika iwo akuwona.
3
Zovala zake zidasanduka zoŵala ndi zoyera kuti mbee, kupambana m'mene mmisiri wina aliyense angayeretsere nsalu pansi pano.
4
Nthaŵi yomweyo ophunzira aja adaona Eliya ndi Mose, akukambirana ndi Yesu.
5
Petro adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Tiloleni timange misasa itatu, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.”
6
Ankatero chifukwa chosoŵa chonena, pakuti iye ndi anzake aja anali atagwidwa ndi mantha aakulu.
7
Tsono padafika mtambo, nuŵaphimba, ndipo mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, muzimumvera.”?
8
Mwadzidzidzi ophunzirawo poyang'anayang'ana, adangoona kuti palibenso wina amene anali nawo pamenepo, koma Yesu yekha.
9
Pamene ankatsika phirilo, Yesu adaŵaletsa kuti zimene adaaonazo asauze wina aliyense mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa.
10
Iwo adasungadi chinsinsichi, koma ankafunsana okhaokha kuti, “Kodi kuuka kwa akufa akunena Yesuku ndiye kuti chiyani?”
11
Tsono adamufunsa kuti, “Nanga bwanji aphunzitsi a Malamulo amati Eliya adzayenera kuyamba wabwera?”
12
Yesu adaŵayankha kuti, “Zoonadi, Eliya adzayambadi wabwera, kuti adzakonzenso zonse. Komabe bwanji Malembo amanena kuti Mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri ndi kunyozedwa?
13
Ine ndikukuuzani kuti Eliya adafikadi, ndipo anthu adamchita zonse zomwe iwo ankafuna, monga momwe Malembo adaanenera za iye.”
14
Pamene Yesu ndi ophunzira atatuwo adabwerera kwa ophunzira ena aja, adapeza chikhamu chachikulu cha anthu chitaŵazinga. Aphunzitsi a Malamulo ankatsutsana ndi ophunzirawo.
15
Pamene anthu onsewo adaona Yesu, adadabwa kwambiri, ndipo adamthamangira kudzamlonjera.
16
Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi mukutsutsana zotani?”
17
Mmodzi mwa anthuwo adayankha kuti, “Aphunzitsi, ine ndinabwera ndi mwana wanga wamwamuna kuti ndidzampereke kwa Inu, chifukwa adaloŵedwa ndi mzimu woipa womuletsa kulankhula.
18
Umati ukangomugwira, umamgwetsa pansi, mwanayo nkumangoti thovu tututu kukamwa, namakukuta mano, mpaka thupi gwagwagwa kuuma. Ndiye ndinapempha ophunzira anuŵa kuti autulutse, koma alephera.”
19
Apo Yesu adati, “Ha! Anthu a mbadwo wopanda chikhulupiriro! Ndiyenera kukhala nanube mpaka liti? Ndiyenera kukupirirani mpaka liti? Tabwera nayeni kuno mwanayo.”
20
Adabwera nayedi. Mzimu woipa uja utangoona Yesu, nthaŵi yomweyo wayamba kumzunguza mwamphamvu mnyamata uja, mpaka iye pansi khu, nkumangovimvinizika, thovu lili tututu kukamwa.
21
Yesu adafunsa bambo wake uja kuti, “Kodi zimenezi zidamuyamba liti?” Bambo wakeyo adati, “Zidamuyamba ali mwana ndithu.
22
Mzimu umenewu wakhala ukumugwetsa kaŵirikaŵiri, mwina amagwa pa moto, mwina m'madzi, kufuna kumupha. Koma ngati Inu mungathe kuchitapo kanthu, chonde tatichitirani chifundo, mutithandize.”
23
Yesu adati, “Bwanji mukuti, ‘Ngati mungathe?’ Zinthu zonse nzotheka kwa amene ali ndi chikhulupiriro.”
24
Pomwepo bambo wa mwana uja adanena mokweza mau kuti, “Ndikukhulupirira, koma mpang'ono chabe. Thandizeni kuti ndikhulupirire kwenikweni.”
25
Pamene Yesu adaona kuti chikhamu cha anthu chija chayamba kupanikizana pamenepo, adazazira mzimu woipawo, adati, “Iwe mzimu woletsa kulankhula ndi kumva, ndikukulamula kuti utuluke mwa mwanayu, ndipo usadzaloŵenso mwa iye.”
26
Mzimuwo udafuula numzunguza mwamphamvu mwana uja, kenaka nkutuluka. Mwanayo adangoti zii ngati wafa, mpaka ambiri nkumati, “Watsirizika basi!”
27
Koma Yesu adamugwira dzanja namdzutsa, mwanayo nkuimirira.
28
Yesu atakaloŵa m'nyumba, ophunzira ake adamufunsa ali paokha, kuti, “Ifeyo ndiye tinalephera bwanji kuutulutsa mzimu woipa uja?”
29
Yesu adayankha kuti, “Mzimu wa mtundu umenewu, pokhapokha mutayamba mwapemphera mpamene mungautulutse.”
30
Atachoka kumeneko, Yesu ndi ophunzira ake ankadutsa m'dziko la Galileya. Koma Iye sadafune kuti anthu adziŵe,
31
chifukwa ankaphunzitsa ophunzira ake. Ankaŵauza kuti, “Mwana wa Munthu akudzaperekedwa kwa anthu, ndipo iwowo adzamupha. Koma atamupha, Iye adzauka patapita masiku atatu.”
32
Ophunzira ake sadamvetse mau ameneŵa, komabe ankaopa kumufunsa.
33
Yesu ndi ophunzira ake adafika ku Kapernao. Ataloŵa m'nyumba, Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi panjira paja mumatsutsana zotani?”
34
Ophunzirawo adangoti chete. Ndiye kuti zimene ankatsutsana panjirapo zinali zakuti wamkulu ndani pakati pao.
35
Yesu adakhala pansi, naŵaitana ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Ndipo adaŵauza kuti, “Ngati wina afuna kukhala wamkulu, adzisandutse wamng'ono, wotumikira onse.”
36
Atatero adatenga mwana, namkhazika pakati pao nkumufungata, naŵauza kuti,
37
“Aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene. Ndipo wondilandira Ine bwino, ndiye kuti akulandira bwino osati Ineyo, koma Atate amene adandituma.”
38
Yohane adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ife tinaona munthu wina akutulutsa mizimu yoipa potchula dzina lanu, ndiye ife tinayesa kumletsa chifukwa sayenda nafe.”
39
Koma Yesu adati, “Musamletse ai, chifukwa munthu sangati atachita zamphamvu m'dzina langa, nthaŵi yomweyo nkundinyoza.
40
Chifukwa wosatsutsana nafe, ndi wogwirizana nafe ameneyo.
41
Aliyense amene akupatsani chikho cha madzi chifukwa chakuti ndinu ake a Khristu, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.”
42
“Aliyense wochimwitsa ngakhale mmodzi mwa ana okhulupirira Ineŵa, ameneyo kukadakhala kwabwino koposa kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukamuponya m'nyanja.
43
Tsono ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo wosatha uli woduka dzanja, kupambana kuti ukaloŵe uli ndi manja onse aŵiri ku Gehena, kwa moto wosazimika.” [
44
“Kumeneko mphutsi zoŵazunza sizifa, moto wakenso woŵatentha suzima.”]
45
“Ngati phazi lako likuchimwitsa, lidule. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo wosatha uli woduka phazi, kupambana kuti ukaponyedwe ku Gehena uli ndi miyendo yonse iŵiri.” [
46
“Kumeneko mphutsi zoŵazunza sizifa, moto wakenso woŵatentha suzima.”]
47
“Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi bwino kuti ukaloŵe mu Ufumu wa Mulungu uli ndi diso limodzi lokha, kupambana kuti akakuponye ku Gehena uli ndi maso onse aŵiri.
48
Kumeneko mphutsi zoŵazunza sizifa, moto wakenso woŵatentha suzima.
49
“Onse adzayeretsedwa ndi moto monga momwe nsembe imayeretsedwa ndi mchere.
50
Mchere ndi wabwino, koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? Moyo wanu ukhale ngati wothiridwa mchere, ndipo muzikhala ndi mtendere pakati panu.”
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16