bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Mark 11
Mark 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 12 →
1
Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankayandikira ku Yerusalemu, kufupi ndi ku Betefage ndi Betaniya, midzi ya ku Phiri la Olivi, Iye adatuma aŵiri mwa ophunzirawo,
2
naŵauza kuti, “Pitani m'mudzi mukuwonawo. Mukangoloŵamo, mukapeza mwanawabulu ali chimangire, amene munthu sanakwerepo chikhalire. Mukammasule nkubwera naye.
3
Wina akakakufunsani kuti, ‘Inu, nchiyani chimenecho?’ Inu mukati, ‘Ambuye ali naye ntchito, akangothana naye amtumiza konkuno nthaŵi yomweyo.’ ”
4
Ophunzira aja adapitadi, nakapeza mwanawabuluyo ali chimangirire pa khomo m'mbali mwa mseu, ndipo adayamba kummasula.
5
Anthu amene adaali pamenepo adaŵafunsa kuti, “Inu nchiyani chimenecho, buluyo mukummasuliranji?”
6
Ophunzirawo adaŵayankha monga momwe adaaŵauzira Yesu. Tsono anthuwo adaŵalola kuti ammasule.
7
Ophunzira aja adabwera naye mwanawabuluyo kwa Yesu. Adayala zovala zao pamsana pa bulu uja, Yesu nkukwerapo.
8
Anthu ambiri ankayala zovala zao mu mseu, ena nkumayalika nthambi zamasamba zomwe ankakazithyola ku thengo.
9
Anthu amene adaali patsogolo, ndi amene adaali m'mbuyo, adayamba kufuula kuti, “Ulemu kwa Mulungu. Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye.
10
Udalitsidwe Ufumu wa atate athu Davide umene ulikudza tsopano. Ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.”
11
Yesu ataloŵa m'Yerusalemu, adakaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayang'anayang'ana zonse. Tsono poti chisisira chinali chitagwa, adatuluka napita ku Betaniya pamodzi ndi ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja.
12
M'maŵa mwake, pamene iwo ankachoka ku Betaniya kuja, Yesu adaamva njala.
13
Ataona mkuyu chapatali potero, uli ndi masamba, adapitapo kuti kapena nkupezamo nkhuyu. Koma atafika, sadapezemo nkhuyu, koma masamba okhaokha, pakuti siinali nyengo ya nkhuyu.
14
Pamenepo adauza mtengowo kuti, “Mtengo iwe, kuyambira tsopano mpaka muyaya wina aliyense asadzadyekonso zipatso zako.” Mau ameneŵa ophunzira ake aja adaŵamva.
15
Iwo adafika ku Yerusalemu. Tsono Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayamba kutulutsa anthu amene ankachita malonda m'menemo. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda.
16
Sadalolenso kuti wina aliyense azidutsa m'mabwalo a Nyumbayo atasenza chinthu ai.
17
Pambuyo pake adayamba kuŵaphunzitsa naŵauza kuti, “Paja Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.’ Koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.”
18
Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo atamva zimenezi, adayamba kufunafuna njira yoti amuphere. Pakutitu ankachita naye mantha poona kuti anthu onse ankadabwa nazo zimene Iye ankaphunzitsa.
19
Kutayamba kuda, Yesu ndi ophunzira ake adatulukamo mumzindamo.
20
M'maŵa mwake, m'mamaŵa ndithu, iwo akuyenda mu mseu, adaona mkuyu uja waumiratu wonse ndi mizu yomwe.
21
Apo Petro adakumbuka zijazi, ndipo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, taonani, mkuyu uja mudautembererawu wauma.”
22
Yesu adaŵayankha kuti, “Muzikhala ndi chikhulupiriro mwa Mulungu.
23
Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wolamula phiri ili kuti, ‘Choka apa, kadziponye m'nyanja,’ atanena ndi mtima wosakayika, nakhulupirira ndithu kuti zimene akunenazo zichitikadi, ndithu zidzachitikadi monga momwe waneneramo.
24
Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti, m'mapemphero mwanu mukapempha Mulungu chinthu chilichonse, muzikhulupirira kuti mwalandira, ndipo mudzachilandiradi.
25
Ndipo pamene mukuti mupemphere, muziyamba mwakhululukira mnzanu ngati muli naye nkanthu. Mukatero, Atate anunso amene ali Kumwamba adzakukhululukirani machimo anu.” [
26
“Koma ngati inu simukhululukira anzanu, Atate anunso amene ali Kumwamba sadzakhululukira machimo anu.”]
27
Yesu adafikanso ku Yerusalemu. Tsono pamene Iye ankangodziyendera m'Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi akulu a Ayuda adadzamufunsa kuti,
28
“Kodi mphamvu zoti muzichita zimenezi mudazitenga kuti? Ndani adakupatsani mphamvu zimenezi?”
29
Yesu adati, “Nanenso ntakufunsani funso limodzi. Mukandiyankha, ndiye ndikuuzeni kumene ndidatenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.
30
Kodi Yohane kuti azibatiza, mphamvu zake adaazitenga kwa yani, kwa Mulungu kapena kwa anthu? Tandiyankhani.”
31
Iwo aja adayamba kukambirana nkumati, “Tikati adaazitenga kwa Mulungu, Iyeyu anena kuti, ‘Nanga bwanji tsono simudamkhulupirire?’
32
Komanso tikati adaazitenga kwa anthu, apo ndiye ainso.” Adaatero chifukwa choopa anthu, pakuti anthu onse ankati Yohane anali mneneri weniweni.
33
Ndiye adangomuyankha Yesuyo kuti, “Kaya, ife sitikudziŵa.” Apo Iye adati, “Nanenso tsono sindikuuzani kumene ndidazitenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.”
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16