bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Mark 5
Mark 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 6 →
1
Tsono Yesu ndi ophunzira ake adafika ku tsidya la Nyanja ya Galileya, ku dera la Agerasa.
2
Yesu atangotuluka m'chombo, munthu wina wogwidwa ndi mzimu woipa adadzakumana naye kuchokera ku manda.
3
Munthuyo ankakhala kumandako, ndipo padaalibe wina wothanso kummanga, ngakhale ndi unyolo womwe.
4
Kale anthu adaayesa kangapo kummanga miyendo ndi zitsulo, ndiponso kummanga manja ndi maunyolo, koma iye ankangoŵamwetsula maunyolowo, ndipo zitsulo zomanga miyendozo ankangozithyola. Padaalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumgonjetsa.
5
Usana ndi usiku ankakhala kumandako ndi m'mapiri, akumangofuula ndi kudzipweteka ndi miyala.
6
Pamene iye adaona Yesu chakutali, adamthamangira nadzamgwadira.
7
Mokweza mau adati, “Kodi ndakuputani chiyani, Inu Yesu, Mwana wa Mulungu Wopambanazonse? M'dzina la Mulungu ndikukupemphani, musandizunze.”
8
Adaatero chifukwa Yesu anali atanena kuti, “Mzimu woipawe, tuluka mwa munthuyu!”
9
Tsono Yesu adamufunsa munthuyo kuti, “Dzina lako ndani?” Iye adayankha kuti, “Dzina langa ndine ‘Chigulu,’ chifukwa tilipo ochuluka.”
10
Ndipo iye adadandaulira Yesu kwambiri kuti mizimuyo asaitulutsire kunja kwa dera limenelo.
11
Pafupi pomwepo, pachitunda poteropo, pankadya gulu lalikulu la nkhumba.
12
Tsono mizimu yoipa ija idapempha Yesu kuti, “Tipirikitsireni ku nkhumbazo, tiloleni tikaloŵe m'menemo.”
13
Yesu adailoladi. Iyo idatuluka nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja, mpaka kufera m'madzimo. Zonse zidaalipo ngati zikwi ziŵiri.
14
Oŵeta nkhumbazo adathaŵa, nakasimbira anthu mu mzinda ndi ku midzi. Pamenepo anthu adatuluka kuti akaone zimene zidaachitikazo.
15
Atafika kumene kunali Yesuko, adaona munthu adaagwidwa ndi mizimu yoipa uja atakhala pansi, atavala, misala ija itatha, munthu woti adaloŵedwa ndi chigulu cha mizimu yoipa. Anthuwo adagwidwa ndi mantha.
16
Anzao amene adaaonerera zonse zikuchitika, adaŵasimbira zimene zidaamuchitikira munthu wamizimuyo ndiponso nkhumba zija.
17
Apo anthuwo adampempha Yesu kuti achoke ku dera laolo.
18
Pamene Yesu ankakaloŵa m'chombo, munthu amene adaagwidwa ndi mizimu yoipa uja adampempha kuti apite nao.
19
Koma Yesu adakana namuuza kuti, “Iyai, iwe pita kumudzi kwa anthu akwanu, ukaŵafotokozere zazikulu zimene Ambuye akuchitira mwa chifundo chao.”
20
Munthuyo adapitadi nakayamba kufalitsa ku dera lotchedwa Mizinda Khumi, zazikulu zimene Yesu adaamchitira. Atamva zimenezo anthu onse adazizwa kwambiri.
21
Yesu adaolokanso nyanja. Pamene adafika pa tsidya, chinamtindi cha anthu chidasonkhana pamphepete pa nyanja pamene panali Iyepo.
22
Tsono kudafika munthu wina, dzina lake Yairo, amene anali mmodzi mwa akulu a nyumba yamapemphero. Ataona Yesu, adadzigwetsa ku mapazi ake,
23
nayamba kumdandaulira kwambiri. Adati, “Pepani, mwana wanga wamkazi ali pafupi kufa. Ngati nkotheka, mukamsanjike manja kuti achire ndi kukhala ndi moyo.”
24
Yesu adanyamuka namapita naye. Anthu ambiri adatsagana naye namayenda momupanikiza.
25
Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri.
26
Adaazunzika zedi ndi asing'anga ochuluka amene ankayesa kumuchiza. Mwakuti adaamwaza chuma chake chonse, komabe osapeza bwino konse. M'malo mwake matendawo analikunka nakulirakulira.
27
Maiyo anali atamva za Yesu. Tsono adaloŵa m'chinamtindi cha anthu chija, nkuphaphatiza mpaka kukafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza chovala chake.
28
Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Ndikangokhudza ngakhale zovala zake zokhazo, ndichira.”
29
Ndipodi nthaŵi yomweyo matenda a msambowo adaleka, mwiniwakeyo nkumva m'thupi mwake kuti matenda ake aja atha.
30
Pomwepo Yesu adazindikira kuti mphamvu zina zatuluka mwa Iye. Tsono adatembenuka nayang'ana anthu aja ndipo adafunsa kuti, “Kodi ndani wandikhudza zovala?”
31
Ophunzira ake adati, “Ndi Inu nomwe mukuwona kuti anthu akukupanikizani, ndiye mungafunse bwanji kuti, ‘Ndani wandikhudza?’ ”
32
Koma Yesu adayang'anayang'ana kuti aone yemwe wachita zimenezo.
33
Apo mai uja adachita mantha nayamba kunjenjemera, chifukwa anali atazindikira zimene zidaamuwonekerazo. Adadza pafupi, nadzigwetsa pansi pamaso pa Yesu, nkumufotokozera zonse monga momwe zidaachitikira.
34
Yesu adamuuza kuti, “Inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi mtendere. Matenda anu atheretu.”
35
Yesu akulankhulabe, kudafika anthu kuchokera kunyumba kwa mkulu uja. Adamuuza mkuluyo kuti, “Mwana uja watsirizika. Musaŵavutenso Aphunzitsiŵa.”
36
Koma Yesu sadasamale zimene anthuwo ankanena. Adauza mkulu uja kuti, “Musaope ai, inu mungokhulupirira.”
37
Tsono sadalole kuti winanso atsagane naye, koma Petro, ndi Yakobe, ndi Yohane, mbale wa Yakobeyo.
38
Pamene iwo adafika kunyumba kwa mkulu wa nyumba yamapemphero uja, Yesu adaona chipiringu cha anthu, akulira ndi kubuma.
39
Iye ataloŵa, adaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita phokoso lonseli ndi kubuma? Mwanayutu sadamwalire ai, ali m'tulo chabe.”
40
Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola. Iye adaŵatulutsira panja onse, nangotenga bambo wake ndi mai wake wa mwanayo, ndiponso amene adaali naye aja, nkuloŵa kuchipinda kumene kunali mwana uja.
41
Tsono adagwira mwanayo pa dzanja namuuza kuti, “Talita, kumi.” (Ndiye kuti, “Mtsikana iwe, ndikuti dzuka.”)
42
Pomwepo mtsikanayo adadzukadi, nayamba kuyenda, pakuti adaali wa zaka khumi ndi ziŵiri. Pamenepo anthu aja adazizwa kwambiri.
43
Koma Yesu adaŵalamula mwamphamvu kuti zimenezo wina aliyense asazidziŵe. Kenaka adaŵauza kuti ampatse chakudya mtsikanayo.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16