bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 1
John 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 2 →
1
Pachiyambi pa zonse Iye amene amatchedwa dzina loti Mau, anali alipo kale. Anali kwa Mulungu, ndipo anali Mulungu.
2
Anali kwa Mulungu chikhalire.
3
Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye.
4
Mwa Iyeyo munali moyo, ndipo moyowo unali kuŵala kounikira anthu.
5
Kuŵalako kukuunikabe mu mdima, ndipo mdima sudathe kugonjetsa kuŵalako.
6
Mulungu adaatuma munthu wina, dzina lake Yohane.
7
Iyeyu adaabwera ngati mboni, kudzachitira umboni kuŵala kuja, kuti anthu onse akhulupirire chifukwa cha umboni wakewo.
8
Sikuti iyeyo ndiye anali kuŵalako ai, koma adangobwera kudzachitira umboni kuŵalako.
9
Kuŵala kwenikweni, kounikira anthu onse, kunkadza pansi pano.
10
Wotchedwa Mauyo anali m'dziko lapansi, ndipo Mulungu adalenga dziko lapansilo kudzera mwa Iye, komabe anthu apansipano sadamzindikire.
11
Adaabwera kwao ndithu, koma anthu ake omwe sadamlandire.
12
Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo ameneŵa Iye adaŵapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu.
13
Kukhala ana a Mulungu kumeneku sikudachokere m'kubadwa kwao, kapena ku chifuniro cha thupi, kapena ku chifuniro cha munthu ai, koma kudachokera kwa Mulungu.
14
Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.
15
Yohaneyo adaamchitira umboni. Ankauza anthu mwamphamvu kuti, “Uyu ndiye uja ndinkanenayu kuti amene akubwera pambuyo panga ngwoposa ine; pakuti ine ndisanabadwe, Iye alipo.”
16
Kuchokera m'kukoma mtima kwake kwathunthu ife tonse tidalandira madalitso, madalitso ake otsatanatsatana.
17
Paja Mulungu adatipatsa Malamulo ake kudzera mwa Mose, koma kudzera mwa Yesu Khristu adatizindikiritsa kukoma mtima ndi kukhulupirika kwake.
18
Chikhalire palibe munthu amene adaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekha uja, amene ali wapamtima wa Atate, ndiye adaulula za Mulunguyo.
19
Nthaŵi ina akuluakulu a Ayuda a ku Yerusalemu adaatuma ansembe ndi Alevi ena kukafunsa Yohane kuti, “Kodi iwe ndiwe yani?”
20
Iye adayankha mosabisa konse, adanenetsa ndithu kuti, “Inetu sindine Mpulumutsi wolonjezedwa uja ai.”
21
Adamufunsanso kuti, “Nanga ndiwe yani? Ndiwe Eliya kodi?” Iye adati, “Iyai, sindine Eliya.” Iwo adati, “Kodi ndiwe Mneneri tikumuyembekeza uja?” Koma Yohane adayankha kuti, “Ainso.”
22
Tsono adamuuza kuti, “Tanena zenizenitu, kuti tikaŵafotokozere bwino amene atituma. Mwiniwakewe umati ndiwe yani?”
23
Yohane adaŵayankha kuti, “Monga adaanenera mneneri Yesaya: “Ine ndine liwu la munthu wofuula m'chipululu; akunena kuti, ‘Ongolani mseu wodzadzeramo Ambuye.’ ”
24
Anthu aja adaaŵatuma ndi Afarisi.
25
Tsono adafunsa Yohane kuti, “Ngati sindiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, kapena Eliya, kapenanso Mneneri tikumuyembekeza uja, nanga bwanji umabatiza?”
26
Yohane adaŵayankha kuti, “Ine ndimabatiza ndi madzi, koma pakati panupa pali wina amene inu simukumdziŵa.
27
Iyeyu ngwobwera pambuyo panga, komabe sindili woyenera ngakhale kumasula zingwe za nsapato zake.”
28
Zimenezi zidachitikira ku Betaniya, kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, kumene Yohane ankabatiza.
29
M'maŵa mwake Yohane adaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo a anthu a pa dziko lonse lapansi.
30
Iyeyu ndi amene ndinkanena uja kuti, ‘Pambuyo panga pakubwera munthu wopambana ine, pakuti ine ndisanabadwe, Iye alipo.’
31
Inenso sindinkamudziŵa, koma ndidabwera kudzabatiza ndi madzi kuti Aisraele amdziŵe.”
32
Yohane adachitanso umboni, adati, “Ndidaona Mzimu Woyera akutsika kumwamba ngati nkhunda, nakhazikika pa Iye.
33
Ine sindinkamudziŵa, koma Mulungu amene adandituma kudzabatiza ndi madzi, ndiye adaandiwuza kuti, ‘Amene udzaone Mzimu Woyera akutsika ndi kukhazikika pa Iye, ndi Iyeyo wobatiza mwa Mzimu Woyera.’
34
Ineyo ndidaziwonadi, ndipo ndikuchita umboni kuti ameneyu ndi Mwanadi wa Mulungu.”
35
M'maŵa mwakenso Yohane anali pamalo pomwepo pamodzi ndi ophunzira ake ena aŵiri.
36
Pamene adaona Yesu akuyenda, iye adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu.”
37
Ophunzira aŵiri aja atamva mauwo, adatsatira Yesu.
38
Yesu adacheuka naona kuti akumtsatira, tsono adaŵafunsa kuti, “Kodi ulendowu?” Iwo adati, “Timati tidziŵe, kodi mumakhala kuti, Rabi?” (Tanthauzo la Rabi ndiye kuti, Mphunzitsi.)
39
Yesu adati, “Tiyeni mukakuwone.” Iwo adapita naye. Pamenepo nthaŵi inali ngati 4 koloko madzulo. Adakaonako kumene Iye ankakhala, ndipo adakhala naye tsiku limenelo.
40
Mmodzi mwa aŵiri aja amene adaamva mau a Yohane natsatira Yesu, anali Andrea, mbale wake wa Simoni Petro.
41
Iye adayamba kukapeza mbale wakeyo Simoni, namuuza kuti, “Tampeza Mesiya.” (Ndiye kuti, Mpulumutsi wolonjezedwa uja.)
42
Motero adamtenga kupita naye kwa Yesu. Pamene Yesu adamuwona adati, “Ndiwe Simoni, mwana wa Yohane. Dzina lako lidzakhala Kefa.” (Tanthauzo la Kefa ndi Petro, ndiye kuti Thanthwe.)
43
M'maŵa mwake Yesu adaganiza zopita ku Galileya. Adapeza Filipo, namuuza kuti, “Unditsate.”
44
Filipo anali wa ku mudzi wa Betsaida, kwaonso kwa Andrea ndi Petro.
45
Filipo adakapeza Natanaele namuuza kuti, “Tampeza Ujayu amene Mose adalemba za Iye m'buku la Malamulo, uja anenerinso adalemba za Iye. Ndi Yesu Mwana wa Yosefe, wa ku Nazarete.”
46
Koma Natanaele adamufunsa kuti, “Kodi ku Nazarete nkuchokera kanthu kabwino?” Filipo adati, “Tiye ukadziwonere wekha.”
47
Pamene Yesu adaona Natanaele akubwera potero, adati, “Mwamuwonatu Mwisraele weniweni wopanda chinyengo.”
48
Natanaele adamufunsa kuti, “Mwandidziŵa bwanji?” Yesu adati, “Muja unakhala patsinde pa mkuyu paja, Filipo asanakuitane, Ine ndinakuwona.”
49
Natanaele adati, “Aphunzitsi, ndinudi Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Israele.”
50
Yesu adamuyankha kuti, “Kodi wakhulupirira chifukwa ndakuuza kuti ndinakuwona patsinde pa mkuyu paja? Udzaona zoposa pamenepa.”
51
Adatinso, “Ndithu ndikunenetsa kuti mudzaona Kumwamba kutatsekuka, angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika pa Mwana wa Munthu.”
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21