bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 16
John 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 17 →
1
“Ndakuuziranitu zonsezi kuti mungadzataye mtima.
2
Adzakudulani ku mpingo. Komanso nthaŵi ilikudza yakuti aliyense amene adzakuphani, adzayesa kuti akutumikira Mulungu.
3
Adzachita zimenezi chifukwa sadadziŵe Atate kapenanso Ine.
4
Koma ndimati muzimve zimenezi kuti nthaŵi yakeyo ikadzafika, mudzakumbukire kuti ndidaakuuziranitu.” “Sindidakuuzeni zimenezi poyamba paja ai, chifukwa ndinali nanu pamodzi.
5
Koma tsopano ndikupita kwa amene adandituma, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu wondifunsa kuti, ‘Mukupita kuti?’
6
M'mitima mwanu mwadzaza chisoni chifukwa ndakuuzani zimenezi.
7
Komabe ndikukuuzani zoona, kuti nkwabwino koposa kwa inu kuti ndichoke. Pakuti ngati sindichoka, Nkhoswe ija siidzabwera kwa inu. Koma ngati ndipita, ndidzaitumiza kwa inu.
8
Ndipo Iyeyu atafika, adzaŵatsimikiza anthu a pansi pano kuti ngolakwa pa za kuchimwa, za kulungama, ndiponso za kuweruza.
9
Ngolakwa pa za kuchimwa, chifukwa sandikhulupirira.
10
Ngolakwa pa za kulungama, chifukwa ndikupita kwa Atate ndipo simudzandiwonanso.
11
Ngolakwa pa za kuweruza, chifukwa Satana, mfumu ya anthu oipa a dziko lino lapansi, waweruzidwa kale.
12
“Ndili nawo mau ena ambiri oti ndikuuzeni, koma simungathe kuŵamvetsa tsopano ai.
13
Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo.
14
Adzandilemekeza, pakuti adzatenga zochokera kwa Ine nadzakudziŵitsani.
15
Zonse za Atate nzanga. Nchifukwa chake ndanena kuti adzatenga zochokera kwa Ine, nadzakudziŵitsani inu.”
16
“Kanthaŵi pang'ono ndipo simudzandiwonanso, koma patapitanso kanthaŵi pang'ono, mudzandiwona.”
17
Ophunzira ake ena adayamba kufunsana kuti, “Kodi nchiyani akutiwuzachi? Akuti, ‘Kanthaŵi pang'ono ndipo simudzandiwonanso, koma patapitanso kanthaŵi pang'ono, mudzandiwona.’ Akutinso, ‘Chifukwa ndikupita kwa Atate.’
18
Kodi nchiyani akunenachi kuti, ‘Kanthaŵi pang'ono?’ Sitikumvetsa zimene akufuna kunena.”
19
Yesu adaazindikira kuti ophunzirawo akufuna kumufunsa. Choncho adati, “Kodi mukufunsana za mau amene ndanenaŵa akuti, ‘Kanthaŵi pang'ono ndipo simudzandiwonanso, koma patapitanso kanthaŵi pang'ono, mudzandiwona?’
20
Ndithu ndikunenetsa kuti inu mudzalira ndi kukhuza, koma anthu odalira zapansi pano adzakondwa. Inu mudzamva chisoni, koma chisoni chanu chidzasanduka chimwemwe.
21
Pa nthaŵi yochira mai amavutika chifukwa nthaŵi yake yafika. Koma pamene wabadwa mwana, saganizakonso za kuzunzikako, chifukwa cha chimwemwe chakuti kunja kuno kwabadwa mwana.
22
Chomwecho inunso mukuvutika tsopano, koma ndidzakuwonaninso. Pamenepo mtima wanu udzakondwa, ndipo palibe munthu amene adzakulandani chimwemwe chanucho.
23
Pa tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mungapemphe kwa Atate potchula dzina langa, adzakupatsani.
24
Mpaka tsopano simunapemphe kanthu potchula dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu.”
25
“Ndakuuzani zimenezi mophiphiritsa. Nthaŵi ilikudza pamene sindidzalankhula nanunso mophiphiritsa, koma ndidzakudziŵitsani momveka za Atate.
26
Tsiku limenelo mudzapempha potchula dzina langa, ndipo sindikuti Ine ndidzakupempherani kwa Atate ai,
27
pakuti okukondani ndi Atate amene. Amakukondani chifukwa mumandikonda, ndipo mumakhulupirira kuti ndidachokera kwa Iwo.
28
Ndidachokeradi kwa Atate kudza pansi pano. Tsopano ndikuchokanso pansi pano kupita kwa Atate.”
29
Ophunzira ake adati, “Apo ndipo. Tsopano mukulankhula momveka, osatinso mophiphiritsa ai.
30
Tsopano tadziŵa kuti mumadziŵa zonse, ndipo palibenso chifukwa choti munthu akufunseni mafunso. Nchifukwa chake tikukhulupirira kuti ndinu ochokera kwa Mulungu.”
31
Yesu adaŵayankha kuti, “Kani mwakhulupiriratu tsopano?
32
Nthaŵi ilikudza, ndipo yafika kale, pamene mudzabalalikana aliyense kunka kwao, Ine kundisiya ndekha. Komabe sindili ndekha, pakuti Atate ali nane.
33
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21