bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 20
John 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 21 →
1
Pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, m'mamaŵa ndithu kudakali kamdima, Maria wa ku Magadala adadza ku manda a Yesu. Adaona kuti chimwala chija chachotsedwa kale pa khomo la mandawo.
2
Choncho adathamanga nakafika kwa Simoni Petro, ndi kwa wophunzira wina uja amene Yesu ankamukonda kwambiri. Adaŵauza kuti, “Aŵachotsa Ambuye m'manda muja, ndipo sitikudziŵa kumene akaŵaika.”
3
Pamenepo Petro ndi wophunzira wina uja adatuluka napita ku manda.
4
Onse aŵiri adathamanga pamodzi, koma wophunzira wina uja adathamanga kopambana Petro, nkuyambira ndiye kufika kumandako.
5
Adaŵerama naona nsalu zija zili chikhalire, koma iye sadaloŵemo.
6
Simoni Petro atafika akumutsatira, adaloŵa m'mandamo. Adaona nsalu zija zili chikhalire,
7
ndiponso kansalu kamene kanali kumutu kwake. Kansaluko sikanali pamodzi ndi nsalu zina zija, koma padera pakokha, kali chipindire.
8
Pamenepo wophunzira wina uja, amene adaayambira kufika ku manda, nayenso adaloŵa; ndipo ataona zimenezi, adakhulupirira.
9
Mpaka nthaŵi imeneyo iwo aja anali asanamvetse Malembo akuti Yesu adzayenera kuuka kwa akufa.
10
Pambuyo pake ophunzirawo adabwerera kwao.
11
Maria adakhalabe chilili panja pafupi ndi manda, akulira. Akulira choncho, adaŵerama kusuzumira m'mandamo,
12
naona angelo aŵiri ovala zovala zoyera. Angelowo adaakhala pansi, wina kumutu, wina kumapazi pamalo pamene padaagona mtembo wa Yesu paja.
13
Iwo adamufunsa kuti, “Inu mai, mukuliranji?” Iye adati, “Chifukwa aŵachotsa Ambuye anga ndipo sindikudziŵa kumene akaŵaika.”
14
Atanena zimenezi adacheuka, naona Yesu ataimirira pomwepo, koma sadamzindikire kuti ndi Yesu.
15
Tsono Yesu adamufunsa kuti, “Mai iwe, ukuliranji? Ukufuna yani?” Maria ankayesa kuti ndi wakumundako, motero adamuuza kuti, “Bambo, ngati mwaŵachotsa ndinu, mundiwuze kumene mwakaŵaika, kuti ndikaŵatenge.”
16
Yesu adati, “Maria!” Iye adacheuka, nanena kuti, “Raboni!” (Ndiye kuti “Aphunzitsi” pa chihebri)
17
Yesu adamuuza kuti, “Usandigwire, pakuti sindinakwerebe kupita kwa Atate. Koma pita kwa abale anga, ukaŵauze kuti, ‘Ndikukwera kupita kwa Atate anga, omwe ali Atate anunso, Mulungu wanga, yemwe ali Mulungu wanunso.’ ”
18
Maria wa ku Magadalayo adapita, nakauza ophunzira aja kuti, “Ndaŵaona Ambuye,” ndipo adaŵakambira zimene Ambuyewo adaamtuma.
19
Madzulo kutada pa tsiku Lamulungu lomwelo, ophunzira aja anali pamodzi. Zitseko zinali zokhoma, chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Tsono Yesu adadza naimirira pakati pao nkunena kuti, “Mtendere ukhale nanu!”
20
Atatero, adaŵaonetsa manja ake ndi m'nthiti mwake, ndipo ophunzira aja adakondwa kwambiri poŵaona Ambuyewo.
21
Yesu adatinso, “Mtendere ukhale nanu. Monga Atate adandituma, Inenso ndikukutumani.”
22
Pambuyo pake adaŵauzira mpweya nati, “Landirani Mzimu Woyera.
23
Anthu amene mudzaŵakhululukira machimo ao, adzakhululukidwadi, koma amene simudzaŵakhululukira, sadzakhululukidwa ai.”
24
Mmodzi mwa ophunzira aja khumi ndi aŵiri, Tomasi (wotchedwa Didimo), sanali pamodzi ndi anzake pamene Yesu adaabwera.
25
Tsono ophunzira anzake aja adamuuza kuti, “Ife taŵaonatu Ambuye.” Koma Tomasi adati, “Ndikapanda kuwona mabala a misomali m'manja mwao, ndi kupisa chala changa m'mabala a misomaliwo, ndipo ndikapanda kupisa dzanja langa m'nthiti mwao, sindingakhulupirire konse.”
26
Patapita masiku asanu ndi atatu, ophunzira aja analinso m'nyumbamo, ndipo Tomasi anali nawo. Zitseko zinali chikhomere, koma Yesu adadza, naimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu!”
27
Atatero, adauza Tomasi kuti, “Ika chala chako apa, ona manja anga. Tambalitsa dzanja lako, ulipise m'nthiti mwangamu. Leka kukayika, uyambepo kukhulupirira.”
28
Tomasi adati, “Ambuye anga! Mulungu wanga!”
29
Yesu adati, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiwona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone.”
30
Yesu adachitanso zizindikiro zina zambiri zozizwitsa pamaso pa ophunzira ake, zimene sizidalembedwe m'buku muno.
31
Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, ndipo kuti pakukhulupirira mukhale ndi moyo m'dzina lake.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21