bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 21
John 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
1
Pambuyo pake Yesu adadziwonetsanso kwa ophunzira ake ku nyanja ya Tiberiasi. Adadziwonetsa motere:
2
Simoni Petro, Tomasi (wotchedwa Didimo), Natanaele wochokera ku mudzi wa Kana m'dera la Galileya, ana aja a Zebedeo, ndiponso ophunzira ena aŵiri, anali pamodzi.
3
Simoni Petro adaŵauza kuti, “Ine ndikukasodza.” Iwo adati, “Ifenso tipita nao.” Adanyamuka nakaloŵa m'chombo. Koma usiku umenewo sadaphe kanthu.
4
Kutacha Yesu adaimirira pa mtunda. Komabe ophunzira aja sadazindikire kuti ndi Yesu.
5
Tsono Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi anzathu, mwaphako kanthu ngati?” Iwo adati, “Ai ndithu, tabwera chabe.”
6
Yesu adaŵauza kuti, “Ponyani khoka ku dzanja lamanja la chombo, mupha kanthu.” Iwo adaponyadi, ndipo sadathe kulikokanso chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba.
7
Pamenepo wophunzira uja amene Yesu ankamukonda kwambiriyu adauza Petro kuti, “Ndi Ambuye!” Pamene Simoni Petro adamva kuti ndi Ambuye, adavala mkanjo wake (chifukwa anali atauvula), ndipo adadziponya m'nyanja.
8
Koma ophunzira ena aja adadza ndi chombo ku mtunda akukoka khoka lodzaza ndi nsomba. Sanali kutali ndi mtunda, koma pafupi, ngati mamita 90.
9
Pamene adafika pa mtunda, adaonapo moto wamakala, pali nsomba, ndiponso buledi.
10
Yesu adaŵauza kuti, “Bwera nazoni nsomba zina zimene mwapha.”
11
Apo Simoni Petro adaloŵa m'chombo muja nakokera khoka lija ku mtunda, lodzaza ndi nsomba zazikulu zokwanira 153. Ngakhale nsombazo zinali zochuluka chotero, khokalo silidang'ambike.
12
Yesu adaŵauza kuti, “Bwerani, mufisule.” Koma mwa ophunzirawo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adaalimba mtima kumufunsa kuti, “Ndinu yani?” Pakuti adaazindikira kuti ndi Ambuye.
13
Yesu adadza natenga buledi uja nkuŵapatsa. Adateronso ndi nsomba zija.
14
Aka nkachitatu kuti Yesu aonekere ophunzira ake Iye atauka kwa akufa.
15
Iwo atafisula, Yesu adafunsa Simoni Petro kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi koposa m'mene amandikondera aŵa?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziŵa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala anaankhosa anga.”
16
Yesu adamufunsanso kachiŵiri kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziŵa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Ŵeta nkhosa zanga.”
17
Yesu adamufunsa kachitatu kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda?” Petro adayamba kumva chisoni kuti Yesu akumufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda?” Ndipo adati, “Ambuye, mumadziŵa zonse. Mukudziŵa kuti ineyo ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala nkhosa zanga.
18
Kunena zoona, pamene unali mnyamata, unkadzimanga wekha lamba nkumapita kulikonse kumene unkafuna kupita. Koma ukadzakalamba, udzatambalitsa manja ako, ndipo wina adzakumanga nkumapita nawe kumene sukufuna.”
19
(Yesu adanena zimenezi pofuna kuŵadziŵitsa za m'mene Petro adzafere ndi kulemekeza Mulungu.) Atatero, adauza Petro kuti, “Unditsate.”
20
Petro adacheuka, naona wophunzira uja amene Yesu ankamukonda kwambiri akuŵatsatira. Ndiye wophunzira yemwe uja amene adaatsamira pa chifukwa cha Yesu paphwando paja namufunsa kuti, “Ambuye, amene adzakuperekani kwa adani anu ndani?”
21
Pamene Petro adamuwona iyeyo, adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, nanga uyu bwanji?”
22
Yesu adamuuza kuti, “Ngati ndifuna kuti iye akhalebe mpaka ndidzabwerenso, kodi iwe uli nazo kanthu? Iweyo unditsate.”
23
Tsono mbiri idamveka pakati pa abale kuti wophunzira mnzaoyo sadzafa. Komatu Yesu sadamuuze kuti sadzafa ai, koma adaati, “Ngati ndifuna kuti iye akhalebe mpaka ndidzabwerenso, kodi iwe uli nazo kanthu?”
24
Ameneyo ndiye wophunzira uja amene akuchitira umboni zimene zidachitikazo, ndipo ndiye amene adazilemba. Tikudziŵa kuti umboni wakewo ngwoona.
25
Koma palinso zina zambiri zimene Yesu ankachita. Zikadalembedwa zonsezo, ndiganiza kuti pa dziko lonse lapansi sipakadaoneka malo okwanira mabuku onse olembedwawo.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21