bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 17
John 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 18 →
1
Yesu atanena zimenezi, adayang'ana kumwamba nati, “Atate, yafika nthaŵi. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwanayo akulemekezeni Inu.
2
Pajatu mudampatsa mphamvu zolamulira anthu onse, kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mudampatsa.
3
Moyo wosathawo ndi wakuti akudziŵeni Inu, amene nokhanu ndinu Mulungu weniweni, ndipo adziŵenso Yesu Khristu amene mudamtuma.
4
Ndakulemekezani pansi pano pakutsiriza ntchito imene mudandipatsa.
5
Ndipo tsopano Inu Atate mundilemekeze pamaso panu ndi ulemerero uja umene ndinali nawo kwa Inu lisanalengedwe dziko lapansi.”
6
“Amene mudaŵapatula mwa anthu onse ndi kundipatsa Ine, ndaŵadziŵitsa dzina lanu. Anali anu, Inu mudaŵapereka kwa Ine, ndipo adasunga mau anu.
7
Tsopano akudziŵa kuti zonse zimene mudandipatsa nzochokera kwa Inu.
8
Pakuti ndaŵapatsa mau amene mudandiwuza Ine, ndipo aŵalandira. Akudziŵadi kuti ndidachokera kwa Inu, ndipo sakayika kuti ndinu mudandituma.
9
“Ine ndikuŵapempherera. Sindikupempherera anthu ena onse, koma ndikupempherera iwoŵa amene mudandipatsa, chifukwa ndi anu.
10
Zanga zonse nzanu, monga zanu zonse nzanga, motero ndimalemekezedwa mwa iwowo.
11
Ndilikudza kwa Inu. Ine sindikhalanso pansi pano ai, koma iwoŵa akhala pansi pano. Atate oyera, asungeni iwoŵa m'dzina lanu limene mudandipatsa, kuti akhale amodzi monga ife.
12
Pamene ndinali nawo pamodzi, ndinkaŵasunga ndi mphamvu za dzina lanu, zimene mudandipatsa. Ndidaŵalondoloza bwino, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adatayika, kupatula yekha uja amene adayenera kutayika, kuti zipherezere zimene Malembo adaaneneratu.
13
“Tsopano ndilikudza kwa Inu. Ndikulankhula zimenezi pamene ndili pansi pano, kuti chimwemwe changa chikhalenso chodzaza mwa iwowo.
14
Ndaŵaphunzitsa mau anu. Anthu odalira zapansipano amadana nawo, chifukwa iwo sali anzao, monga Inenso sindili mnzao.
15
Sindikupempha kuti muŵachotse pansi pano ai, koma kuti muŵatchinjirize kwa Woipa uja.
16
Iwo sali a dziko lapansi, monga Inenso sindili wa dziko lapansi.
17
Muziŵapatula ndi mau anu kuti akhale anthu anu. Mau anuwo ngoona zedi.
18
Monga mudandituma Ine pansi pano, Inenso ndaŵatuma pansi pano.
19
Ndipo chifukwa cha iwoŵa ndikudzipereka kwa Inu, kuti iwonso akhale odzipereka moonadi kwa Inu.”
20
“Sindikupempherera iwo okhaŵa ai, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha mau ao.
21
Ndikuŵapempherera kuti iwo onse akhale amodzi. Monga Inu Atate mumakhala mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife. Motero anthu onse adzakhulupirira kuti mudandituma.
22
Ulemerero womwewo umene mudandipatsa, ndaŵapatsanso iwoŵa. Akhale amodzi monga Ife tili amodzi.
23
Ine ndikhale mwa iwo, Inu mwa Ine, kuti akhale amodzi kwenikweni. Motero anthu onse adzazindikira kuti mudandituma ndinu, ndipo kuti mumaŵakonda monga momwe mumandikondera Ine.
24
“Atate, ndifuna kuti amene mudandipatsa, iwonso akhale pamodzi ndi Ine kumene ndili. Ndifuna kuti aone ulemerero wanga umene mudandipatsa, chifukwa mudandikonda dziko lapansi lisanalengedwe.
25
Atate olungama, anthu odalira zapansipano sadakudziŵeni ai, koma Ine ndimakudziŵani, ndipo aŵa ali panoŵa akudziŵa kuti ndinu mudandituma.
26
Ndidaŵadziŵitsa dzina lanu, ndipo ndidzaŵaphunzitsabe. Ndifuna kuti chikondi chimene mumandikonda nacho, chikhalenso mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.”
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21