bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 11
John 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 12 →
1
Panali munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankadwala. Anali wa ku mudzi wa Betaniya, kwao kwa Maria ndi mbale wake Marita.
2
Mariayo ndi yemwe uja amene adaadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira, nkupukuta mapazi ao ndi tsitsi lake. Lazaro ankadwalayo anali mlongo wake.
3
Tsono alongo ake aja adatumiza thenga kwa Yesu kukamuuza kuti, “Ambuye, bwenzi lanu uja akudwala.”
4
Pamene Yesu adamva zimenezi adati, “Kudwalako safa nako ai, koma zatero kuti Mulungu alemekezedwe, ndipo kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo.”
5
Ndiye kuti Yesu ankakonda Marita ndi mng'ono wake Maria ndiponso Lazaro.
6
Komabe pamene adamva za matendawo, Yesu adaswera masiku aŵiri pamalo pomwe adaaliripo.
7
Pambuyo pake adauza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tipitenso ku Yudeya.”
8
Ophunzira akewo adati, “Aphunzitsi, tsopano apa Ayuda ankafuna kukuponyani miyala, ndiye mukuti mupitenso komweko?”
9
Yesu adati, “Kodi suja usana uli ndi maora khumi ndi aŵiri? Munthu akayenda masana, sakhumudwa, chifukwa amaona kuŵala kwa dzikoku.
10
Koma akayenda usiku, amakhumudwa chifukwa kuŵalako alibe.”
11
Atatero adaŵauza kuti, “Lazaro, bwenzi lathu, wagona tulo, koma ndipita kuti ndikamdzutse ku tulo taketo.”
12
Apo ophunzira ake adati, “Ambuye, ngati wagona tulo, achira.”
13
Iwo ankayesa kuti akunena za tulo teniteni, koma Yesu ankanena za imfa yake ya Lazaro.
14
Tsono Yesu adaŵauza mosabisa kuti, “Lazaro wamwalira,
15
komabe chifukwa cha inu ndikukondwera kuti Ine kunalibe kumeneko, kuti choncho mukakhulupirire. Tiyeni tipiteko.”
16
Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, adauza ophunzira anzake kuti, “Tiyeni ifenso tipite nao kuti tikafe naye pamodzi.”
17
Pamene Yesu adafika ku Betaniya, adapeza Lazaro atagona m'manda masiku anai.
18
Ku Betaniya kunali kufupi ndi ku Yerusalemu, mtunda wokwanira pafupi makilomita atatu.
19
Panali anthu ambiri amene adaabwera kwa Marita ndi Maria kudzaŵapepesa chifukwa cha imfa ya mlongo wao.
20
Pamene Marita adamva kuti Yesu akubwera, adapita kukamchingamira. Koma Maria adaatsalira m'nyumba.
21
Tsono Marita adauza Yesu kuti, “Ambuye, mukadakhala kuno, sibwenzi mlongo wanga atamwalira.
22
Koma ngakhale tsopano, ndikudziŵa kuti Mulungu adzakupatsani zilizonse mungampemphe.”
23
Yesu adamuuza kuti, “Mlongo wako adzauka.”
24
Marita adati, “Ndikudziŵa kuti adzauka podzauka anthu kwa akufa pa tsiku lomaliza.”
25
Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso woŵapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo.
26
Ndipo aliyense amene ali ndi moyo nakhulupirira Ine, sadzafa konse. Kodi ukukhulupirira zimenezi?”
27
Iye adati, “Inde Ambuye, ndikukhulupirira kuti Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, amene adayenera kubwera pansi pano.”
28
Marita atanena zimenezi, adaitanira paseri Maria mng'ono wake namuuza kuti, “Afika Aphunzitsi, akukuitana.”
29
Maria atamva zimenezi, adanyamuka msangamsanga, nadza kwa Yesu.
30
Pamenepo nkuti Yesu asanafike kumudziko, koma anali chikhalire pamalo pomwe Marita adaakumana naye.
31
Anthu amene anali m'nyumba akupepesa Mariayo, ataona kuti wanyamuka msangamsanga ndi kutuluka, adamtsatira. Ankayesa kuti akupita kumanda kukalira kumeneko.
32
Maria atafika pamene panali Yesu, namuwona, adadzigwetsa kumapazi kwake nati, “Ambuye, mukadakhala kuno, sibwenzi mlongo wanga atamwalira.”
33
Yesu ataona Maria akulira, ndiponso anthu amene adaadza naye iwonso akulira, zidamkhudza kwambiri ndipo adavutika mu mtima.
34
Tsono adaŵafunsa kuti, “Mudamuika kuti?” Iwo adati, “Ambuye, tiyeni mukaone.”
35
Yesu adayamba kulira.
36
Pamenepo anthu aja adati, “Onani, ankamukonda zedi.”
37
Koma ena mwa iwo adati, “Munthu uyu suja adapenyetsa munthu wosapenya uja? Monga sakadatha kuchitapo kanthu kuti Lazaroyu asafe?”
38
Yesu adavutikanso mu mtima, nakafika ku manda amene anali phanga. Pakhomo pake panali chimwala.
39
Tsono adati, “Tachotsani chimwalacho.” Marita, mlongo wa womwalirayo, adamuuza kuti, “Pepani Ambuye, wayamba kale kununkha, pakuti wagonamo masiku anai.”
40
Yesu adamufunsa kuti, “Kodi sindidakuuze kuti ukakhulupirira uwona ulemerero wa Mulungu?”
41
Tsono anthu adachotsa chimwala chija. Yesu adayang'ana kumwamba nati, “Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimvera.
42
Ndikudziŵa kuti mumandimvera nthaŵi zonse. Koma ndanena zimenezi chifukwa cha khamu la anthu amene ali panoŵa, kuti akhulupirire kuti ndinu mudandituma.”
43
Atatero adaitana mokweza mau kuti, “Lazaro, tuluka!”
44
Pomwepo munthu amene adaamwalirayo adatuluka, miyendo yake ndi manja ake zili zomangidwa ndi nsalu zamaliro. Nkhope yake inali yokutidwa ndi nsalu. Yesu adaŵauza kuti, “Mmasuleni, ndipo mlekeni azipita.”
45
Ambiri mwa anthu amene adaabwera kwa Maria, adaona zimene Yesu adaachita, ndipo adamkhulupirira.
46
Koma ena adapita kwa Afarisi, nakaŵasimbira zimene Yesu adaachita.
47
Apo akulu a ansembe ndi Afarisi adaitanitsa Bungwe Lalikulu la Ayuda, nafunsana kuti, “Titani pamenepa, popeza kuti munthuyu akuchita zozizwitsa zambiri?
48
Tikamlekerera chomwechi, anthu onse adzamkhulupirira, ndipo Aroma adzabwera nkudzatiwonongera malo athu oyeraŵa ndiponso mtundu wathuwu.”
49
Koma mmodzi mwa iwo, dzina lake Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe onse chaka chimenecho, adaŵauza kuti, “Inu simudziŵa kanthu konse ai.
50
Monga inu simukuwona kuti nkwabwino koposa kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu onse, m'malo moti mtundu wathu wonse uwonongeke?”
51
(Kwenikwenitu sadanene zimenezi ndi nzeru za iye yekha ai. Koma popeza kuti anali mkulu wa ansembe onse chaka chimenecho, ankalosa kuti Yesu adzafera mtundu wa Ayuda.
52
Tsono osati kungofera fuko chabe, komanso kusonkhanitsa pamodzi ana a Mulungu amene adabalalika.)
53
Kuyambira tsiku limenelo akulu aja a Ayuda adayamba kupangana zoti amuphe.
54
Nchifukwa chake Yesu sankayenda poyera pakati pa anthu. Koma adachokako napita ku dziko limene linali pafupi ndi chipululu, ku mudzi wina dzina lake Efuremu, ndipo adakhala kumeneko pamodzi ndi ophunzira ake.
55
Chikondwerero cha Paska chija chinkayandikira. Choncho anthu ambiri ochokera ku midzi adapita ku Yerusalemu kukachita mwambo wa kudziyeretsa, Paska isanayambe.
56
Ankamufunafuna Yesu, ndipo pamene adasonkhana m'Nyumba ya Mulungu ankafunsana kuti, “Kodi inu mukuganiza bwanji? Kodi monga Iye uja abwera kuchikondwerero kuno?”
57
Koma akulu a ansembe ndi Afarisi anali atalamula kuti aliyense akadziŵa kumene kuli Yesu, aŵadziŵitse, kuti akamgwire.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21