bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 7
John 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 8 →
1
Pambuyo pake Yesu ankayendera dera la Galileya. Sadafune kukayendera dera la Yudeya, chifukwa akuluakulu a Ayuda ankafuna kumupha.
2
Nthaŵiyo nkuti chikondwerero cha Misasa chili pafupi.
3
Tsono abale ake a Yesu adamuuza kuti, “Bwanji muchokeko kuno, mupite ku Yudeya kuti ophunzira anu kumeneko nawonso akaone ntchito zamphamvu zimene mukuchitazi.
4
Munthu sachita kanthu m'seri akafuna kudziŵika ndi anthu. Popeza kuti Inu mukuchita ntchito zoterezi, mudziwonetse poyera pamaso pa anthu onse.”
5
(Ndiye kuti abale akewo ankatero chifukwa ngakhale iwo omwe sankamukhulupirira.)
6
Yesu adaŵauza kuti, “Nthaŵi yanga siinafikebe, koma yanu ndi nthaŵi iliyonse.
7
Anthu ongokonda zapansipano sangadane nanu, koma amadana ndi Ine, chifukwa ndimapereka umboni wosonyeza kuti ntchito zao nzoipa.
8
Inuyo pitani kuchikondwereroko. Ine sindipitako ku chikondwerero chimenechi, chifukwa nthaŵi yanga yoyenera siinafike.”
9
Yesu atanena zimenezo, adatsalira m'Galileya.
10
Koma abale ake atapita ku chikondwerero cha Misasa chija, Yesu nayenso adapitako. Sadapite moonekera, koma mobisika.
11
Akulu a Ayuda ankamufunafuna kuchikondwereroko, nkumafunsana kuti, “Kodi amene uja ali kuti?”
12
Ndipo panali manong'onong'o ambiri okamba za Iye pakati pa khamu la anthu. Ena ankanena kuti, “Ndi munthutu wabwino.” Koma ena ankati, “Iyai, amangosokeza anthu ameneyu.”
13
Komabe panalibe munthu wolankhula poyera za Iye, chifukwa choopa akulu a Ayuda.
14
Chikondwerero chija chikali pakati, Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu nayamba kuphunzitsa.
15
Akulu a Ayuda adadabwa nati, “Bwanji munthu ameneyu ali ndi nzeru zotere, pamene sadaphunzire konse?”
16
Yesu adati, “Zimene ndimaphunzitsa si zangatu ai, ndi za Atate amene adandituma.
17
Aliyense wofuna kuchita kufuna kwa Mulungu, adzadziŵa ngati zimene Ine ndimalankhula nzochokera kwa Mulungu kapena kwa Ine ndekha.
18
Amene amangolankhula zakezake, amadzifunira yekha ulemu. Koma yemwe amafunira ulemu amene adamtuma, ameneyo ndiye woona, ndipo mumtima mwake mulibe chinyengo.
19
Kodi suja Mose adakupatsani Malamulo a Mulungu? Komabe palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene akuŵatsata. Nanga mukufuniranji kundipha?”
20
Koma khamu la anthu lidamuyankha kuti, “Wagwidwa ndi mizimu yoipa Iwe. Akufuna kukupha ndani?”
21
Yesu adati, “Ndinangochita ntchito yozizwitsa imodzi yokha, nonsenu nkumadabwa.
22
Mose adakulamulani kuti muziwumbala ana anu aamuna (ngakhale mwambowo si wochokera kwa Mose koma kwa makolo); ndipo inu mumaumbala mwana wamwamuna ngakhale mpa tsiku la Sabata.
23
Mwanayo mumamuumbala pa Sabata, kuwopa kuti Lamulo la Mose lingaphwanyidwe. Bwanji mukuipidwa nane chifukwa ndinachiritsa munthu kwathunthu pa tsiku la Sabata?
24
Musamaweruza poyang'ana maonekedwe chabe, koma muziweruza molungama.”
25
Pamenepo anthu ena a ku Yerusalemu adati, “Kodi munthu akufuna kumupha uja, si ameneyu?
26
Si uyu akulankhula poyerayu, popandanso wonenapo kanthu! Kodi kapenatu ndiye kuti akuluakulu akuzindikiradi kuti ameneyu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja eti?
27
Komatu Mpulumutsi wolonjezedwa uja akadzabwera, palibe amene adzadziŵe kumene wachokera. Koma uyu tonse tikudziŵa kumene adachokera.”
28
Pamene Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, adalankhula mokweza mau kuti, “Ine mukundidziŵa, ndipo kumene ndidachokera mukudziŵakonso. Koma sindidabwere mwa kufuna kwanga ai. Atate amene ali wokhulupirika ndiwo adandituma. Inu simukuŵadziŵa.
29
Koma Ine ndikuŵadziŵa, chifukwa ndine wochokera kwa Iwo, ndipo ndiwo adandituma.”
30
Pamenepo anthu adafuna kumgwira Yesu, koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene adamkhudza, chifukwa nthaŵi yake inali isanafike.
31
Koma anthu ambiri a m'khamu limenelo adamkhulupirira, ndipo ankati, “Kodi akadzabwera Mpulumutsi wolonjezedwa uja, adzachita zizindikiro zozizwitsa zoposa zimene munthuyu wachita?”
32
Afarisi adamva manong'onong'o a chikhamu cha anthu okamba za Yesu. Tsono iwo pamodzi ndi akulu a ansembe adatuma asilikali a ku Nyumba ya Mulungu kuti akamgwire.
33
Apo Yesu adati, “Ndili nanube kanthaŵi pang'ono ndisanapite kwa Atate amene adandituma.
34
Mudzandifunafuna, koma simudzandipeza. Ndipo kumene ndizikakhala Ine, inu simungathe kufikako.”
35
Pamenepo akulu a Ayudawo adayamba kufunsana kuti, “Kodi iyeyu afuna kupita kuti kumene ife sitingakampeze? Kodi kapena akufuna kupita kwa anzathu amene adabalalikira kwa anthu a mitundu ina? Monga nkuti afuna kukaphunzitsa anthu akunja?
36
Akunena kuti, ‘Mudzandifunafuna koma simudzandipeza,’ ndiponso kuti, ‘Kumene ndizikakhala Ine, inu simungakafikeko.’ Kodi mau ameneŵa akutanthauza chiyani?”
37
Tsiku lotsiriza la chikondwerero chija linali lalikulu. Pa tsikulo Yesu adaimirira nkunena mokweza kuti, “Ngati pali munthu ali ndi ludzu, abwere kwa Ine kuti adzamwe.
38
Paja Malembo akuti, ‘Munthu wokhulupirira Ine, mtima wake udzakhala ngati gwelo la mitsinje ya madzi opatsa moyo.’ ”
39
(Pakutero Yesu ankanena za Mzimu Woyera amene anthu okhulupirira Iye analikudzalandira. Nthaŵi imeneyo nkuti Mzimu Woyera asanafike, chifukwa Yesu anali asanalandire ulemerero wake.)
40
Pamene khamu la anthu lidamva mau ameneŵa, ena mwa iwo ankati, “Zoonadi munthuyu ndiye Mneneri uja.”
41
Ena ankanena kuti, “Ameneyu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.” Koma ena ankanena kuti, “Kodi Mpulumutsiyo nkuchokera ku Galileya ngati?
42
Suja Malembo akuti kholo lake ndi mfumu Davide? Ndipo sujanso akuti adzachokera ku mudzi wa Betelehemu kumene Davideyo anali?”
43
Choncho khamu la anthu lidagaŵikana chifukwa cha Iye.
44
Ena ankafuna kumgwira, koma panalibe amene adamkhudza.
45
Asilikali a ku Nyumba ya Mulungu aja adabwerera kwa akulu a ansembe ndi kwa Afarisi aja. Iwo adafunsa asilikaliwo kuti, “Bwanji simudabwere naye?”
46
Asilikali aja adayankha kuti, “Palibenso wina amene adalankhulapo ngati munthu ameneyo nkale lonse.”
47
Apo Afarisi adati, “Kani inunso wakunyengani?
48
Kodi mudamvapo kuti pakati pa akuluakulu kapena pakati pa Afarisi alipo wokhulupirira amene uja?
49
Koma anthu wambaŵa sadziŵa Malamulo a Mose; ngotembereredwa basi!”
50
Tsono Nikodemo, mmodzi mwa Afarisi, yemwe uja amene kale adaapita kwa Yesu, adafunsa anzakewo kuti,
51
“Kodi Malamulo athu amatilola kuweruza munthu tisanamve mau ake kuti tidziŵe zimene wachita?”
52
Iwo adati, “Kani iwenso ndiwe wa ku Galileya? Kafunefune m'Malembo ndipo udzaona kuti palibe mneneri wochokera ku Galileya.” [
53
Pamenepo anthu onse adabwerera kwao.]
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21