bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 3
John 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 4 →
1
Munthu wina wa m'gulu la Afarisi, dzina lake Nikodemo, mkulu wa Ayuda,
2
adadza kwa Yesu usiku. Adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe munthu wotha kuchita zizindikiro zozizwitsa zimene Inu mukuzichita, ngati Mulungu sali naye.”
3
Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati munthu sabadwanso kwatsopano, sangauwone Ufumu wa Mulungu.”
4
Nikodemo adamufunsa kuti, “Kodi munthu angathe kubadwanso bwanji atakalamba kale? Kodi nkukaloŵa m'mimba mwa amai ake kuti abadwe kachiŵiri?”
5
Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati munthu sabadwa m'madzi ndi mwa Mzimu Woyera, sangathe kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu.
6
Chobadwa mwa munthu ndi thupi chabe, koma chobadwa mwa Mzimu Woyera ndi mzimu.
7
Usadabwe m'mene ndakuuza kuti muyenera kubadwanso.
8
Mphepo imaombera komwe ikufuna, ndipo umamva kuwomba kwake, koma sudziŵa komwe yachokera kapena komwe ikupita. Nchimodzimodzi munthu aliyense amene abadwa mwa Mzimu Woyera.”
9
Nikodemo adafunsa kuti, “Zimenezi zingachitike bwanji?”
10
Yesu adati, “Kodi iwe sindiwe mphunzitsi wodziŵika pakati pa Aisraele, nanga sukumvetsa bwanji zimenezi?
11
Ndithu ndikunenetsa kuti timalankhula zimene tikuzidziŵa, ndipo timachitira umboni zimene tidaziwona, koma inu simukukhulupirira mau athuŵa.
12
Ngati simukhulupirira pamene ndikukuuzani zapansipano, nanga mudzakhulupirira bwanji ndikadzakuuzani za Kumwamba?
13
Palibe munthu amene adakwera kupita Kumwamba, koma Mwana wa Munthu ndiye adatsika kuchokera Kumwamba.
14
“Monga momwe Mose adaapachikira njoka pa mtengo m'chipululu muja, momwemonso Mwana wa Munthu ayenera kudzapachikidwa,
15
kuti aliyense wokhulupirira akhale ndi moyo wosatha mwa Iye.
16
Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
17
Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzaŵapulumutse.
18
“Munthu wokhulupirira Mwanayo, sazengedwa mlandu. Koma wosakhulupirira, wazengedwa kale, chifukwa sadakhulupirire Mwana mmodzi yekha uja wa Mulungu.
19
Mlandu wake ndi uwu wakuti ngakhale kuŵala kudadza pansi pano, anthu adakonda mdima, osati kuŵalako, chifukwa zochita zao zinali zoipa.
20
Aliyense wochita zoipa, amadana ndi kuŵala. Saonekera poyera, kuwopa kuti zochita zakezo zingaonekere.
21
Koma wochita zokhulupirika amaonekera poyera, ndipo zochita zake zimadziŵika kuti wazichita momvera Mulungu.”
22
Pambuyo pake Yesu ndi ophunzira ake adapita ku dera la Yudeya. Adakhala nawo kumeneko kanthaŵi, ndipo ankabatiza.
23
Yohane nayenso ankabatiza ku Ainoni pafupi ndi Salimu, chifukwa kumeneko kunali madzi ambiri. Anthu ankafikako, iye nkumaŵabatiza.
24
Pamenepo nkuti Yohane asanaponyedwe m'ndende.
25
Ophunzira ena a Yohane adayamba kukangana ndi Myuda wina pa za mwambo wa kuyeretsa.
26
Choncho ophunzirawo adadza kwa Yohane namuuza kuti, “Aphunzitsi onanitu, munthu uja amene anali ndi inu patsidya pa Yordani, yemwe uja munkamuchitira umboniyu, nayenso akubatiza, ndipo anthu onse akuthamangira kwa Iye.”
27
Yohane adati, “Munthu sangalandire kanthu kalikonse ngati Mulungu sampatsa.
28
Inu nomwe ndinu mboni zanga kuti ndidati, ‘Sindine Mpulumutsi wolonjezedwa uja, koma ndine wotumidwa patsogolo pake.’
29
Mkwati wamkazi mwini wake ndi mkwati wamwamuna. Koma bwenzi la mkwati wamwamuna limaimirira pafupi, nkumamvetsera. Limakondwa kwakukulu likamva mau a mkwati wamwamunayo. Momwemonso ine ndakondwa kwakukulu.
30
Iye uja ayenera kumakula, ine nkumachepa.”
31
“Wochokera Kumwamba ali pamwamba pa onse. Wochokera pansi pano ndi wapansipano, ndipo amalankhula zapansipano. Wochokera Kumwamba ali pamwamba pa onse.
32
Iyeyu akuchitira umboni zimene adaziwona ndi kuzimva komabe palibe amene amakhulupirira mau akewo.
33
Koma munthu akakhulupirira mau akeŵo, pamenepo amatsimikiza kuti Mulungu sanama.
34
Amene Mulungu adamtumayo, amalankhula mau a Mulungu, pakuti Mulungu amapereka Mzimu Woyera mosaumira.
35
Mulungu Atate amakonda Mwana wake, ndipo adaika zonse m'manja mwake.
36
Munthu wokhulupirira Mwanayo, ali ndi moyo wosatha. Koma wokana kukhulupirira Mwanayo, sadzaona moyo, chifukwa chilango cha Mulungu chili pa iye.”
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21