bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
John 10
John 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 11 →
1
“Kunena zoona, munthu woloŵa m'khola la nkhosa osadzera pa khomo, koma kuchita kukwerera pena, ameneyo ndi wakuba ndi wolanda.
2
Koma munthu woloŵera pa khomo ndiye mbusa wa nkhosazo.
3
Iyeyo mlonda amamtsekulira. Nkhosa zimamva mau ake, ndipo amaziitana maina nkhosa zakezo, nazitulutsa.
4
Akazitulutsa nkhosa zake zonse, amazitsogolera, izo nkumamtsatira, chifukwa zimadziŵa mau ake.
5
Mlendo sizidzamtsatira ai, zidzamthaŵa, chifukwa sizidziŵa mau a alendo.”
6
Yesu adaŵaphera fanizoli, koma iwo sadamvetse zimene ankaŵauzazo.
7
Tsono Yesu adatinso, “Ndithu ndikunenetsa kuti Ine ndine khomo la nkhosa.
8
Ena onse amene adabwera Ine ndisanafike, ngakuba ndi olanda, koma nkhosa sizinaŵamvere.
9
Khomo ndine. Munthu akaloŵera pa Ine, adzapulumuka. Azidzaloŵa ndi kutuluka, ndipo adzapeza chakudya.
10
Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka.
11
“Ine ndine mbusa wabwino. Mbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.
12
Koma wolembedwa ntchito chabe akaona mmbulu ulikudza, amazisiya nkhosazo iye nkuthaŵa. Amatero popeza kuti si mbusa weniweni, ndipo nkhosa si zake ai. Tsono mmbulu uja umagwirapo zina, zina nkumwazikana.
13
Wolembedwa ntchito uja amathaŵa, chifukwa amangotsata malipiro chabe, ndipo salabadirako za nkhosazo.
14
Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziŵa, ndipo izozo Ineyo zimandidziŵa,
15
monga momwe Atate amadziŵira Ine, nanenso nkuŵadziŵa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo.
16
Ndili nazo nkhosa zina zimene sizili za m'khola lino. Zimenezonso ndiyenera kuzikusa. Zidzamva mau anga, ndipo padzakhala gulu limodzi mbusa wakenso mmodzi.
17
“Nchifukwa chake Atate amandikonda, popeza kuti ndikupereka moyo wanga kuti ndikautengenso.
18
Palibe munthu wondilanda moyo wangawu, koma ndikuupereka ndekha. Ndili nazo mphamvu zoutaya moyo wanga, ndili nazonso mphamvu zoutenganso. Udindo umenewu ndidaulandira kwa Atate anga.”
19
Anthu adaayambanso kutsutsana okhaokha chifukwa cha mau ameneŵa.
20
Ambiri mwa iwo ankati, “Ali ndi mizimu yoipa, ndipo wapenga. Bwanji mukumumveranso Iyeyu?”
21
Koma ena ankati, “Mau ameneŵa si a munthu wogwidwa ndi mizimu yoipa. Kodi mizimu yoipa nkupenyetsa anthu akhungu?”
22
Ku Yerusalemu kunali chikondwerero chokumbukira kuperekedwanso kwa Nyumba ya Mulungu. Inali nyengo yozizira.
23
Yesu ankangodziyendera m'Nyumba ya Mulungu, m'khonde lotchedwa Khonde la Solomoni.
24
Anthu adamzinga namufunsa kuti, “Kodi udzaleka liti kutikayikitsa? Ngati ndiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, tiwuze momveka.”
25
Yesu adati, “Ndidakuuzani kale, komabe simukhulupirira. Ntchito zimene ndimachita m'dzina la Atate anga, ndizo zimandichitira umboni.
26
Koma inu simukhulupirira konse, chifukwa simuli a m'gulu la nkhosa zanga.
27
Nkhosa zanga zimamva mau anga. Ine ndimazidziŵa, ndipo zimanditsatira.
28
Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m'manja mwanga.
29
Atate anga amene adandipatsa nkhosazo amapambana onse, ndipo palibe amene angathe kuzilanda m'manja mwao.
30
Ine ndi Atate ndife amodzi.”
31
Anthuwo adatolanso miyala kuti amlase.
32
Yesu adaŵafunsa kuti, “Ndakuwonetsani ntchito zabwino zambiri zimene Atate adandichititsa. Nanga mwa zimenezi ntchito imene mukuti mundiponyere miyala ndi iti?”
33
Anthu aja adamuyankha kuti, “Sitikufuna kukuponya miyala chifukwa cha ntchito yabwino ai, koma chifukwa ukunyoza Mulungu. Iwe, amene uli munthu chabe, ukudziyesa Mulungu.”
34
Yesu adati, “Kodi m'Malamulo mwanu suja mudalembedwa kuti ‘Mulungu adati, Ndinu milungu?’
35
Paja mau a m'Malembo ngoona mpaka muyaya, ndipo Mwiniwakeyo adaŵatcha milungu anthu aja Iye ankalankhula nawoŵa.
36
Inetu Atate adandipatula nandituma pansi pano. Tsono inuyo munganene bwanji kuti ndikunyoza Mulungu, chifukwa ndati ndine Mwana wa Mulungu?
37
Ngati sindichita ntchito zimene Atate anga adandipatsa, musandikhulupirire.
38
Koma ngati ndimazichitadi, khulupirirani ntchitozo, ngakhale simukhulupirira Ine. Apo mudzadziŵa mosapeneka konse kuti Atate amakhala mwa Ine, ndipo Ine ndimakhala mwa Atate.”
39
Pamenepo anthu aja adafunanso kumgwira, koma Iye adazemba.
40
Yesu adabwereranso kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, kumene Yohane ankabatizira anthu poyamba paja, ndipo adakhala komweko.
41
Anthu ambiri adadza kwa Iye, nkumanena kuti, “Yohane sadachite chizindikiro chozizwitsa ai, koma zonse zimene ankanena za Munthuyu zinali zoonadi.”
42
Motero anthu ambiri adakhulupirira Yesu kumeneko.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21